Yeremiya 35:1-19
35 M’masiku a Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti:
2 “Pita kunyumba ya Arekabu,+ ndipo ukalankhule nawo ndi kubwera nawo kunyumba ya Yehova. Ukalowe nawo m’chimodzi mwa zipinda zodyera ndipo ukawapatse vinyo kuti amwe.”
3 Pamenepo ndinatenga Yaazaniya, mwana wa Yeremiya mwana wa Habaziniya, pamodzi ndi abale ake. Ndinatenganso ana ake onse aamuna ndi mabanja onse a Arekabu.
4 Onsewa ndinawabweretsa m’nyumba ya Yehova. Ndinalowa nawo m’chipinda chodyera+ cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu woona. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda chodyera cha akalonga chimene chinali pamwamba pa chipinda chodyera cha Maaseya mwana wa Salumu,+ amene anali mlonda wa pakhomo.
5 Kenako ndinaika makapu odzaza vinyo ndi zipanda pamaso pa ana a Rekabu ndi kuwauza kuti: “Imwani vinyoyu.”
6 Koma iwo anati: “Sitingamwe vinyo, chifukwa Yonadabu mwana wa Rekabu,+ kholo lathu, anatilamula kuti, ‘Inuyo kapena ana anu musamamwe vinyo mpaka kalekale.+
7 Musamamange nyumba, musamafese mbewu, musamabzale mpesa kuti ukhale wanu. Muzikhala m’mahema masiku onse a moyo wanu kuti mukhale ndi moyo wautali padziko lapansi limene mukukhala monga alendo.’+
8 Choncho ife timamvera mawu a Yehonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu, pa chilichonse chimene anatilamula.+ Timachita zimenezi mwa kupewa kumwa vinyo masiku onse a moyo wathu, ifeyo, akazi athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi.+
9 Sitimanga nyumba zoti tikhalemo ndipo sitibzala mpesa, kulima minda kapena kubzala mbewu kuti zikhale zathu.
10 Timakhala m’mahema ndipo timamvera ndi kutsatira zonse zimene Yonadabu,+ kholo lathu linatilamula.+
11 Koma pamene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anabwera kudzaukira dzikoli+ tinati, ‘Tiyeni tilowe mu Yerusalemu chifukwa kukubwera magulu ankhondo a Akasidi ndi magulu ankhondo a ku Siriya. Tiyeni tikakhale mu Yerusalemu.’”+
12 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Yeremiya kuti:
13 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Pita ukalankhule ndi anthu a ku Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuti: “Kodi inu simunali kulimbikitsidwa nthawi zonse kuti muzimvera mawu anga?”+ watero Yehova.
14 “Anthu a m’nyumba ya Rekabu akhala akutsatira mawu a Yehonadabu mwana wa Rekabu,+ amene analamula ana ake kuti asamwe vinyo, ndipo sanamwe vinyo kufikira lerolino. Iwo achita zimenezi chifukwa chomvera lamulo la kholo lawo.+ Koma ine ndinali kulankhula nanu anthu inu, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kulankhula nanu,+ koma simunandimvere.+
15 Ndinali kukutumizirani atumiki anga onse aneneri,+ kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza. Ndinali kuwatuma uthenga wakuti, ‘Bwererani chonde, aliyense asiye njira zake zoipa+ ndipo sinthani zochita zanu kuti zikhale zabwino.+ Musatsatire milungu ina ndi kuitumikira.+ Mupitirize kukhala m’dziko limene ndinakupatsani, inuyo ndi makolo anu.’+ Koma inu simunatchere khutu kapena kundimvera.+
16 Ana a Yehonadabu mwana wa Rekabu+ atsatira lamulo limene kholo lawo linawalamula,+ koma anthu awa sanandimvere.”’”+
17 “Choncho Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Tsopano Yuda ndi anthu onse okhala mu Yerusalemu ndiwagwetsera masoka onse amene ndanena.+ Ndichita zimenezi chifukwa ndalankhula nawo koma sanandimvere ndipo ndinali kuwaitana koma sanandiyankhe.’”+
18 Ndiyeno Yeremiya anauza anthu a m’nyumba ya Rekabu kuti: “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti mwamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu,+ ndipo mukupitiriza kusunga malamulo ake onse ndi kuchita zonse zimene anakulamulani,+
19 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Sipadzasowa munthu wa m’banja la Yonadabu mwana wa Rekabu woima+ pamaso panga kuti azinditumikira nthawi zonse.”’”+