Yeremiya 2:1-37

2  Ndiyeno Yehova anandiuzanso+ kuti:  “Pita, ukafuule m’makutu a anthu a ku Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Ndikukumbukira bwino kwambiri kukoma mtima kosatha kumene unali nako pamene unali wachinyamata,+ chikondi chimene unali nacho pa nthawi imene unali kulonjezedwa kukwatiwa,+ ndi kuti unanditsatira poyenda m’chipululu, m’dziko losabzalidwa kalikonse.+  Isiraeli anali wopatulika kwa Yehova,+ ndipo anali zipatso zoyambirira kwa Iye.”’+ ‘Anthu onse ofuna kumumeza anali kukhala ndi mlandu+ ndipo tsoka linali kuwagwera,’ watero Yehova.”+  Tamverani mawu a Yehova, inu a m’nyumba ya Yakobo+ ndi inu nonse mafuko a m’nyumba ya Isiraeli.+  Yehova wanena kuti: “Kodi makolo anu anandipeza ndi chiyani chosalungama+ kuti akhale patali ndi ine?+ Anandipeza ndi chiyani kuti ayambe kutsatira fano lopanda pake+ iwonso n’kukhala anthu opanda pake?+  Iwo sananene kuti, ‘Ali kuti Yehova, amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo,+ amene anatitsogolera m’chipululu,+ m’dera lam’chipululu lodzaza ndi mayenje, m’dziko lopanda madzi+ ndi la mdima wandiweyani,+ dziko limene simunadutse munthu aliyense komanso mmene simunali kukhala munthu aliyense?’  “M’kupita kwa nthawi, ndinakulowetsani m’dziko la minda ya zipatso kuti mudye zipatso zake ndi zinthu zabwino za m’dzikolo,+ koma munalowa m’dziko langa ndi kuliipitsa. Cholowa changa munachisandutsa chinthu chonyansa.+  Ansembe sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova?’+ Ndipo anthu ophunzitsa chilamulo sanandidziwe.+ Abusa nawonso anaphwanya malamulo anga,+ ndipo aneneri anali kulosera m’dzina la Baala+ ndi kutsatira milungu yopanda phindu.+  “‘Choncho ndidzapitirizabe kulimbana nanu anthu inu,’+ watero Yehova, ‘ndipo ndidzalimbananso ndi ana a ana anu.’+ 10  “‘Wolokerani ku Kitimu,+ m’mbali mwa nyanja, kuti muone. Tumizani anthu ku Kedara+ ndipo muganizire bwinobwino kuti muone ngati zoterezi zinachitikapo kumeneko.+ 11  Kodi pali mtundu wa anthu umene unasinthanitsapo milungu yawo+ ndi zinthu zimene kwa iwo si milungu yeniyeni?+ Koma anthu anga asinthanitsa ulemerero wanga ndi zinthu zosapindulitsa.+ 12  Yang’anitsitsani zimenezi modabwa, inu kumwamba, ndipo tsitsi lanu liimirire ndi mantha aakulu kwambiri,’ watero Yehova,+ 13  ‘chifukwa pali zinthu ziwiri zoipa zimene anthu anga achita: Iwo asiya ine+ kasupe wa madzi amoyo,+ ndipo akumba zitsime zawozawo, zitsime zong’ambika zimene sizingasunge madzi.’ 14  “‘Isiraeli si mtumiki wanga+ komanso si kapolo wobadwira m’nyumba mwanga, si choncho kodi? Nanga n’chifukwa chiyani wafunkhidwa? 15  Mikango yamphamvu imamubangulira.+ Imamutulutsira mawu awo.+ Ndipo yapangitsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa kwa ena. Mizinda yake aiyatsa moto, choncho simukukhala munthu aliyense.+ 16  Ngakhale anthu a ku Nofi+ ndi ku Tahapanesi+ anawononga dziko lako.*+ 17  Kodi sunadzichitire wekha zimenezi mwa kusiya Yehova Mulungu wako+ pa nthawi imene anali kukuyendetsa m’njira yake?+ 18  Ndiyeno n’chifukwa chiyani ukufuna kuyenda m’njira ya ku Iguputo+ kuti ukamwe madzi a mumtsinje wa Sihori?+ N’chifukwa chiyani ukufuna kuyenda m’njira yopita kudziko la Asuri+ kuti ukamwe madzi a mumtsinje wa Firate? 19  Uphunzirepo kanthu pa kuipa kwako+ ndipo zochita zako zosakhulupirika zikudzudzule.+ Dziwa izi, ndipo ona kuti kusiya kwako Yehova Mulungu wako ndi chinthu choipa ndi chowawa.+ Iwe sundiopa ine,’+ watero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 20  “‘Ine ndinaphwanya goli lako kukhala zidutswazidutswa kalekale.+ Ndinadula zingwe zimene anakumanga nazo. Koma iwe unati: “Sindikutumikirani,” ndipo unagona motangadza+ paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira+ n’kumachita uhule+ pamenepo. 21  Koma ine ndinakubzala ngati mtengo wa mpesa wofiira, wabwino kwambiri.+ Mtengo wonsewo unali mbewu yeniyeni yabwino. Ndiye wandisinthira bwanji kukhala mphukira yachabechabe ya mtengo wa mpesa wachilendo?’+ 22  “‘Koma ngakhale utasambira soda ndiponso sopo wambiri,+ cholakwa chako chidzaonekerabe ngati banga pamaso panga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 23  Unganene bwanji kuti, ‘Sindinadziipitse.+ Sindinatsatire mafano a Baala’?+ Ganizira bwinobwino njira yako m’chigwa.+ Onetsetsa zimene wachita. Wakhala ngati ngamila yaing’ono yaikazi imene ikungothamangira uku ndi uku. 24  Wakhala ngati mbidzi+ yaikazi yozolowera kukhala m’chipululu imene ili ndi chilakolako champhamvu, imene ikupuma mwawefuwefu.+ Ndani angaibweze pa nthawi yake yokweredwa? Mbidzi zamphongo zoifunafuna sizidzavutika kuipeza. M’mwezi wake wokweredwa zidzaipeza. 25  Samala kuti phazi lako lisakhale lopanda nsapato, ndi kuti usachite ludzu.+ Koma iwe unati, ‘Zimenezo ayi!+ Ine ndakondana ndi alendo+ ndipo ndidzawatsatira.’+ 26  “Monga mmene mbala imachitira manyazi ikagwidwa, anthu a m’nyumba ya Isiraeli nawonso achita manyazi,+ iwowo, mafumu awo, akalonga awo, ansembe awo ndiponso aneneri awo.+ 27  Iwo akuuza mtengo kuti, ‘Ndinu bambo anga,’+ ndipo akuuza mwala kuti, ‘Ndinu amene munandibereka.’ Iwo andifulatira ndipo sanandisonyeze nkhope yawo.+ Koma tsoka likadzawagwera adzanena kuti, ‘Chonde, bwerani mudzatipulumutse!’+ 28  “Kodi milungu yako imene wadzipangira ili kuti?+ Imeneyo ibwere kwa iwe ngati ingathe kukupulumutsa pa nthawi ya tsoka.+ Pakuti iwe Yuda, milungu yako yachuluka mofanana ndi mizinda yako.+ 29  “‘Kodi n’chifukwa chiyani anthu inu mukupitiriza kundiimba mlandu?+ N’chifukwa chiyani nonsenu mwaphwanya malamulo anga?’+ watero Yehova. 30  Ndalanga ana anu aamuna koma sizinathandize.+ Iwo sanamve chilango* changa.+ Lupanga lanu lapha aneneri anu, ngati mkango umene ukupha anthu ambiri.+ 31  Inu anthu a m’badwo uwu, ganizirani mawu a Yehova.+ “Kodi ndangokhala ngati chipululu kwa Isiraeli+ kapena ngati dziko la mdima wandiweyani? N’chifukwa chiyani anthu angawa anena kuti, ‘Takhala tikuyendayenda mmene tikufunira. Sitibwereranso kwa inu’?+ 32  Kodi namwali angaiwale zodzikongoletsera? Kodi mkwatibwi angaiwale lamba wake wa pachifuwa? Koma anthu anga andiiwala kwa masiku osawerengeka.+ 33  “N’chifukwa chiyani mkazi iwe wakonza njira yako kuti ufunefune amuna oti akukonde? Pa chifukwa chimenechi wadziphunzitsa kuchita zinthu zoipa.+ 34  Komanso, pazovala zako papezeka madontho a magazi a anthu+ osauka osalakwa.+ Madontho a magaziwo sindinawapeze panyumba, ngati kuti anali kuthyola nyumbayo, koma ndawapeza pazovala zako zonse.+ 35  “Koma iwe ukuti, ‘Ine ndilibe mlandu uliwonse. Ndithudi mkwiyo wake wandichokera.’+ “Tsopano ndikuyamba kukuimba mlandu chifukwa chonena kuti, ‘Sindinachimwe.’+ 36  N’chifukwa chiyani kusintha njira kwako ukukuona mopepuka?+ Udzachitanso manyazi ndi Iguputo+ monga mmene unachitira manyazi ndi Asuri.+ 37  Pa chifukwa chimenechi, udzayenda manja ako ali kumutu,+ chifukwa Yehova wakana zinthu zimene umazidalira ndipo sizidzakupindulitsa.”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “anakudya paliwombo.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.