Yeremiya 26:1-24
26 Kuchiyambi kwa ufumu wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panafika mawu ochokera kwa Yehova akuti:
2 “Yehova wanena kuti, ‘Ukaimirire m’bwalo la nyumba ya Yehova,+ ndipo anthu onse amene akubwera kudzalambira panyumba ya Yehova ukawauze zimene zidzachitikira mizinda yonse ya Yuda. Ukawauze mawu onse amene ndidzakulamula kuti uwauze.+ Usachotsepo mawu ngakhale amodzi.+
3 Mwina adzamvera ndipo aliyense wa iwo adzabwerera kuchoka panjira yake yoipa.+ Pamenepo ndidzasintha maganizo anga pa tsoka limene ndikufuna kuwagwetsera chifukwa cha zochita zawo zoipa.+
4 Choncho uwauze kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ngati simudzandimvera mwa kutsatira chilamulo+ chimene ndakupatsani,+
5 komanso kumvera mawu a atumiki anga aneneri amene ndikuwatumiza kwa inu, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza, amene inu simunawamvere,+
6 pamenepo ine ndidzachititsa nyumba iyi kukhala ngati nyumba ya ku Silo.+ Ndipo mzinda uwu ndidzausandutsa chinthu chotembereredwa pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.’”’”+
7 Choncho ansembe, aneneri ndi anthu onse anayamba kumvetsera pamene Yeremiya anali kulankhula mawu amenewa m’nyumba ya Yehova.+
8 Ndiyeno Yeremiya atamaliza kulankhula mawu onse amene Yehova anamulamula kuti akauze anthu onse, nthawi yomweyo ansembe, aneneri ndi anthu onse anamugwira ndi kunena kuti: “Ukufa basi.+
9 N’chifukwa chiyani wanenera m’dzina la Yehova kuti, ‘Nyumba iyi idzafanana ndi nyumba ya ku Silo+ ndipo mzinda uwu udzawonongedwa moti simudzapezeka aliyense wokhalamo’?” Pamenepo anthu onse anali kubwera ndi kuzungulira Yeremiya m’nyumba ya Yehova.
10 Kenako akalonga a Yuda anamva mawu amenewa ndipo anakwezeka kuchokera kunyumba ya mfumu kupita kunyumba ya Yehova.+ Kumeneko anakhala pansi pachipata chatsopano cha nyumba ya Yehova.+
11 Pamenepo ansembe ndi aneneri anayamba kuuza akalongawo ndi anthu onse kuti: “Munthu uyu akuyenera chiweruzo cha imfa+ chifukwa chakuti wanenera za mzinda uwu monga mmene mwamvera ndi makutu anu.”+
12 Atatero, Yeremiya anauza akalonga onse ndi anthu onse kuti: “Yehova ndi amene anandituma kuti ndidzanenere mawu onse amene mwamva okhudza nyumba iyi ndi mzinda uwu.+
13 Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu kuti zikhale zabwino+ ndipo muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu. Mukatero, Yehova adzasintha maganizo ake pa tsoka limene wanena kuti akugwetserani.+
14 Kunena za ine, ndilitu m’manja mwanu.+ Ndichiteni zimene mukuona kuti n’zabwino ndi zoyenera.+
15 Koma mudziwe kuti, mukandipha mupalamula mlandu wamagazi chifukwa chopha munthu wosalakwa. Mlanduwo ukhala pa inuyo, pamzindawu ndi pa anthu onse okhala mumzindawu+ chifukwa kunena zoona, Yehova ndi amene wandituma kuti ndidzakuuzeni mawu onsewa.”+
16 Zitatero, akalonga+ ndi anthu onse anauza ansembe ndi aneneriwo kuti: “Munthu uyu sakuyenera chiweruzo cha imfa+ chifukwa walankhula nafe m’dzina la Yehova Mulungu wathu.”+
17 Ndiyeno akuluakulu ena a anthu a m’dzikomo anaimirira ndi kuyamba kuuza mpingo wonse wa anthuwo kuti:+
18 “Mika+ wa ku Moreseti+ nayenso anali kunenera m’masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda.+ Iye anauza anthu onse a mu Yuda kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ziyoni adzagawulidwa ngati munda,+ ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.”’+
19 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a mu Yuda anamupha? Kodi iye sanaope Yehova ndi kukhazika pansi mtima wa Yehova?+ Kodi atatero, Yehova sanasinthe maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti adzawagwetsera?+ Pamenepatu ife tikudziitanira tsoka lalikulu.+
20 “Panalinso munthu wina amene anali kunenera m’dzina la Yehova. Iyeyu anali Uliya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-yearimu.+ Iye anali kunenera zimene zidzachitikira mzinda uwu ndi dziko ili mogwirizana ndi mawu onse a Yeremiya.
21 Ndiyeno Mfumu Yehoyakimu,+ asilikali ake onse amphamvu ndi akalonga onse anamva mawu amene Uliya anali kunena. Pamenepo mfumu inakonza zoti imuphe.+ Uliya atamva zimenezo, nthawi yomweyo anachita mantha+ ndipo anathawira ku Iguputo.
22 Koma Mfumu Yehoyakimu inatumiza Elinatani, mwana wa Akibori+ ndi amuna ena ku Iguputo.
23 Kumeneko anthuwo anagwira Uliya ndi kubwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Ndiyeno mfumuyo inapha Uliya ndi lupanga+ ndi kutaya mtembo wake m’manda a anthu wamba.”
24 Koma Ahikamu,+ mwana wa Safani+ anali kuteteza Yeremiya kuti anthu asamuphe.+