Yeremiya 44:1-30

44  Mulungu anauza Yeremiya uthenga woti akauze Ayuda onse amene anali kukhala m’dziko la Iguputo,+ m’madera a Migidoli,+ Tahapanesi,+ Nofi+ ndi Patirosi.+ Uthengawo unali wakuti:  “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Inu mwaona masoka onse amene ndagwetsera Yerusalemu+ ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda imeneyi yakhala mabwinja ndipo palibe amene akukhalamo.+  Izi zachitika chifukwa cha zinthu zoipa zimene mwachita ndi kundikhumudwitsa nazo. Mwafukiza nsembe zautsi+ ndi kutumikira milungu ina imene inu kapena makolo anu simunaidziwe.+  Ine ndinali kukutumizirani atumiki anga onse aneneri, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza.+ Ndinali kuwatuma uthenga wakuti: “Chonde, musachite zinthu zonyansa zoterezi zimene ndimadana nazo.”+  Koma inu simunamvere+ kapena kutchera khutu lanu kuti musiye kuchita zinthu zoipa zomwe ndi kupereka nsembe zautsi kwa milungu ina.+  Choncho ndasonyeza mkwiyo wanga ndi ukali wanga ndipo watentha mizinda ya Yuda ndi misewu ya Yerusalemu.+ Lero malo amenewa ndi owonongeka ndipo asanduka bwinja.’+  “Tsopano Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukudziitanira tsoka lalikulu?+ Kodi simukudziwa kuti muphetsa amuna, akazi, ana aang’ono ndi ana oyamwa+ pakati pa Yuda, moti sipapezeka wotsala aliyense?  Mukudziitanira tsoka mwa kundilakwira ndi ntchito za manja anu. Mukuchita zimenezi mwa kufukiza nsembe zautsi kwa milungu ina+ m’dziko la Iguputo limene munalowamo kuti mukhale monga alendo. Mudziphetsa chifukwa cha zimenezi ndipo mudzakhala otembereredwa ndi otonzedwa pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.+  Kodi mwaiwala zoipa zimene makolo anu anachita?+ Kodi mwaiwala zoipa za mafumu a Yuda+ ndi za akazi awo,+ zoipa zanu ndi za akazi anu,+ zimene munachita m’dziko la Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu? 10  Simunadzichepetse kufikira lero+ ndipo simunachite mantha,+ kapena kutsatira malamulo+ ndi malangizo amene ndinapatsa inu ndi makolo anu.’+ 11  “Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndakukanani* ndipo ndikugwetserani tsoka ndi kupha anthu onse a mu Yuda.+ 12  Ine ndigwira otsala a Yuda amene anatsimikiza mtima kulowa m’dziko la Iguputo ndi kukhala mmenemo monga alendo,+ moti onse adzathera m’dziko la Iguputo.+ Iwo adzakanthidwa ndi lupanga ndipo onsewo, osasiyapo aliyense, adzatha chifukwa cha njala yaikulu.+ Adzafa ndi lupanga komanso njala yaikulu. Iwo adzakhala otembereredwa, chinthu chodabwitsa ndi chotonzedwa.+ 13  Ndidzalanga onse okhala m’dziko la Iguputo monga mmene ndinalangira Yerusalemu. Ndidzawalanga ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri.+ 14  Sipadzapezeka aliyense wothawa kapena wopulumuka mwa otsala a Yuda amene alowa m’dziko la Iguputo ndi kukhala mmenemo monga alendo,+ kupatulapo anthu ochepa chabe amene adzathawa. Sipadzapezeka wobwerera kudziko la Yuda kumene akulakalaka kubwerera kuti akakhaleko.’”+ 15  Ndiyeno amuna onse amene anali kudziwa kuti akazi awo anali kupereka nsembe zautsi kwa milungu ina,+ akazi onse amene anaimirira ndi kupanga mpingo waukulu, komanso anthu onse amene anali kukhala ku Iguputo+ m’dera la Patirosi,+ anayankha Yeremiya kuti: 16  “Ife sitimvera mawu amene watiuza m’dzina la Yehova.+ 17  Ife tichita zonse zimene tanena.+ Tipereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa+ kwa ‘mfumukazi yakumwamba.’+ Tichita zimenezi monga mmene ife,+ makolo athu,+ mafumu athu+ ndi akalonga athu anachitira m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu pamene tinali kudya mkate ndi kukhuta ndipo zinthu zinali kutiyendera bwino, moti sitinaone tsoka lililonse.+ 18  Ndipotu kuyambira pamene tinasiya kupereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa ‘mfumukazi yakumwamba,’+ chilichonse chikutisowa, ndipo tawonongeka chifukwa cha lupanga ndi njala yaikulu.+ 19  “Komanso popereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa ‘mfumukazi yakumwamba,’+ kodi sitinafunse amuna athu popangira mfumukaziyo mikate yopereka nsembe yopangidwa m’chifanizo chake kuti tipereke kwa iye nsembe zachakumwazo?”+ 20  Poyankha, Yeremiya anauza anthu onse amene anali kumuyankha ndi mawu amenewa, amuna amphamvu, akazi awo ndi anthu ena onse, kuti: 21  “Kodi Yehova sanakumbukire nsembe zautsi zimene munali kufukiza m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu?+ Kodi nsembe zimene inuyo,+ makolo anu,+ mafumu anu,+ akalonga anu+ ndi anthu a m’dzikolo anali kupereka, sizinalowe mumtima mwake?+ 22  Kenako Yehova sanathenso kupirira zimenezo chifukwa zochita zanu zinaipa kwambiri, chifukwa munachita zinthu zonyansa.+ Chotero dziko lanu linasanduka bwinja, chinthu chodabwitsa ndi chotembereredwa ndipo tsopano mulibe munthu wokhalamo.+ 23  Popeza munachimwira Yehova,+ munali kupereka nsembe zautsi+ ndipo simunamvere mawu a Yehova+ ndi kutsatira malamulo ake,+ malangizo ake ndi zikumbutso zake, n’chifukwa chake masoka onsewa akugwerani lero.”+ 24  Ndiyeno Yeremiya anapitiriza kuuza anthu onse ndi akazi onse kuti: “Tamverani mawu a Yehova inu nonse a ku Yuda amene muli ku Iguputo kuno.+ 25  Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Mawu awa akukhudza amuna inu ndi akazi anu.+ Akazi inu mumalankhula ndi pakamwa panu (ndipo anthu nonsenu mwakwaniritsa zonena zanu ndi manja anu) kuti: “Ife tidzakwaniritsa malonjezo athu+ akuti ‘tidzapereka nsembe zautsi kwa ‘mfumukazi yakumwamba’+ ndi kuti tidzapereka nsembe yachakumwa kwa iye.”+ Akazi inu mudzachitadi zimene mwalonjeza ndipo mudzakwaniritsadi malonjezo anu.’ 26  “Tsopano imvani mawu a Yehova, inu nonse a ku Yuda amene mukukhala mu Iguputo muno.+ Yehova wanena kuti: “Ine ndalumbira m’dzina langa+ kuti m’dziko lonse la Iguputo simudzapezeka munthu aliyense wa ku Yuda woitanira pa dzina langa+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo, Ambuye Wamkulu Koposa!’+ 27  Ine ndikhala tcheru kuti ndiwabweretsere tsoka osati zabwino.+ Ndipo anthu onse a ku Yuda amene ali m’dziko la Iguputo adzafa ndi lupanga ndi njala yaikulu kufikira atatheratu.+ 28  Anthu amene adzathawa lupanga kuchoka ku Iguputo kubwerera kudziko la Yuda adzakhala ochepa.+ Ndipo otsala onse ochokera ku Yuda amene akubwera m’dziko la Iguputo kuti adzakhalemo monga alendo adzadziwa kuti ndi mawu a ndani amene ali oona, mawu anga kapena mawu awo.”’”+ 29  “Yehova wanena kuti: ‘Tsopano chizindikiro cha zimenezi kwa inu ndi ichi,+ ine ndikulangani m’dziko lino kuti mudziwe kuti mawu anga adzakwaniritsidwadi moti ndidzakugwetserani tsoka.+ 30  Yehova wanena kuti: “Ine ndikupereka Farao Hofira, mfumu ya Iguputo,+ m’manja mwa adani ake ndiponso m’manja mwa ofuna moyo wake,+ monga mmene ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mdani wa Zedekiyayo amene akufunanso moyo wake.”’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ndakuikirani nkhope yanga motsutsana nanu.”