Yeremiya 18:1-23

18  Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa:  “Nyamuka, pita kunyumba ya woumba mbiya,+ ndipo ndikakuuza mawu anga kumeneko.”  Pamenepo ndinapita kunyumba ya woumba mbiya, ndipo ndinam’peza akugwira ntchito yake pamikombero ya woumba mbiya.  Chiwiya chimene anali kupanga ndi dongo chinawonongeka ndi dzanja la woumbayo. Choncho iye anasintha ndipo anapanga chiwiya china ndi dongo lomwelo malinga ndi zimene anaona kuti n’zabwino.+  Ndiyeno Yehova anapitiriza kundiuza kuti:  “‘Anthu inu, kodi sindingathe kukuchitirani mofanana ndi mmene woumba mbiyayu anachitira, inu nyumba ya Isiraeli?’ watero Yehova. ‘Taonani! Mofanana ndi dongo limene lili m’manja mwa woumba mbiya, ndi mmene inunso mulili kwa ine, inu nyumba ya Isiraeli.+  Pa nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndizula, kugwetsa ndi kuwononga mtundu uliwonse wa anthu kapena ufumu,+  ndiyeno anthuwo n’kusiya zoipa zimene anali kuchita, zimene ndinawadzudzula nazo,+ pamenepo ndidzasintha maganizo anga kuti ndisawagwetsere tsoka limene ndinafuna kuwagwetsera.+  Koma pa nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndimanga ndi kubzala mtundu wa anthu kapena ufumu,+ 10  ndiyeno anthuwo n’kumachita zoipa pamaso panga mwa kusamvera mawu anga,+ pamenepo ndidzasintha maganizo anga pa zabwino zimene ndinali kufuna kudzawachitira pofuna kuwapindulitsa.’ 11  “Tsopano uza anthu a mu Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikukukonzerani tsoka, ndipo ndikuganizira zokuchitani chinthu choipa.+ Chonde, aliyense wa inu atembenuke kusiya njira yake yoipa ndipo muyambe kuyenda m’njira zabwino ndi kuchita zinthu zabwino.”’”+ 12  Koma iwo anati: “Zimenezo ayi!+ Ife titsatira maganizo athu, ndipo aliyense wa ife adzaumitsabe mtima wake woipawo.”+ 13  Choncho Yehova wanena kuti: “Funsafunsani pakati pa mitundu ya anthu. Ndani anamvapo zoterezi? Namwali wa Isiraeli wachita chinthu choopsa mopyola malire.+ 14  Kodi chipale chofewa chidzasungunuka ndi kuchoka pamapiri a ku Lebanoni? Kapena kodi madzi ochokera kudziko lina ozizira bwino, amene akudontha, adzauma? 15  Pakuti anthu anga andiiwala+ moti amapereka nsembe zautsi kwa chinthu chopanda pake,+ ndiponso amapunthwitsa anthu amene akuyenda panjira zawo,+ m’njira zakale,+ ndi kuwayendetsa m’njira zina, njira zokumbikakumbika. 16  Choncho dziko lawo lidzakhala chinthu chodabwitsa kwa ena,+ chinthu chimene adzachiimbira mluzu mpaka kalekale.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi dzikoli adzaliyang’anitsitsa modabwa ndipo adzapukusa mutu wake.+ 17  Ndidzawamwaza pamaso pa adani awo ngati mmene mphepo yochokera kum’mawa imamwazira fumbi.+ Sindidzawaonetsa nkhope yanga,+ koma ndidzawafulatira pa tsiku la tsoka lawo.” 18  Iwo anapitiriza kunena kuti: “Bwerani anthu inu, timukonzere chiwembu Yeremiya,+ pakuti chilamulo sichidzachoka pakamwa pa ansembe athu.+ Anthu athu anzeru sadzaleka kupereka malangizo ndiponso aneneri athu sadzaleka kulosera.+ Tabwerani, tiyeni timuukire ndi malilime athu+ ndipo tisamvere mawu ake ngakhale pang’ono.” 19  Ndimvereni, inu Yehova, ndipo imvani mawu a anthu amene akutsutsana nane.+ 20  Kodi zabwino amazibwezera ndi zoipa?+ Kumbukirani nthawi zonse zija pamene ndinaima pamaso panu kuwalankhulira zabwino kuti muwachotsere mkwiyo wanu.+ Koma iwo tsopano andikumbira mbuna.+ 21  Chotero ana awo muwakhaulitse ndi njala yaikulu,+ ndipo aphedwe ndi lupanga.+ Akazi awo akhale amasiye ndipo ana a akaziwo afe.+ Amuna awo afe ndi mliri woopsa ndipo anyamata awo aphedwe ndi lupanga pa nkhondo.+ 22  M’nyumba zawo mumveke kulira mukawabweretsera magulu achifwamba mwadzidzidzi,+ chifukwa andikumbira mbuna kuti andigwire ndipo anditchera misampha kuti akole mapazi anga.+ 23  Koma inu Yehova mukudziwa bwino chiwembu chimene andikonzera kuti andiphe.+ Musakhululukire* cholakwa chawo, ndipo musafafanize tchimo lawolo pamaso panu. Koma iwo apunthwe pamaso panu.+ Muwachitire zimenezi pa nthawi ya mkwiyo wanu.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “musaphimbe.”