Yeremiya 25:1-38
25 Awa ndi mawu amene Yeremiya anauzidwa onena za anthu onse a mu Yuda m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, chimenenso chinali chaka choyamba cha ulamuliro wa Nebukadirezara mfumu ya Babulo.
2 Mneneri Yeremiya analankhula mawu amenewa ponena za anthu onse a mu Yuda komanso ponena za anthu onse okhala mu Yerusalemu kuti:
3 “Kuyambira m’chaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya+ mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero, zaka 23 zonsezi, Yehova wakhala akundiuza mawu ndipo ine ndakhala ndikukuuzani mawuwo, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kukuuzani mawu akewo koma simunandimvere.+
4 Yehova anakutumizirani atumiki ake onse aneneri. Anali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza, koma inu simunawamvere+ kapena kutchera khutu lanu kuti mumvetsere.+
5 Aneneriwo anali kukuuzani kuti, ‘Chonde, aliyense wa inu atembenuke ndi kusiya njira yake yoipa ndi zochita zake zoipa+ kuti mupitirize kukhala m’dziko limene Yehova anakupatsani, inuyo ndi makolo anu. Anakupatsani dzikoli kuti chikhale cholowa chanu kwa nthawi yaitali.+
6 Ndipo musatsatire milungu ina kuti muziitumikira ndi kuigwadira. Mukachita zimenezo mudzandikhumudwitsa chifukwa cha mafano anu amene mudzapanga, ndipo ineyo ndidzakugwetserani tsoka.’+
7 “‘Koma simunandimvere,’ watero Yehova, ‘ndipo munachita zimenezo n’cholinga chondikhumudwitsa ndi mafano anu. Zimenezi zakubweretserani tsoka.’+
8 “Choncho Yehova wa makamu wanena kuti, ‘“Popeza simunamvere mawu anga,
9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ watero Yehova, “ndipo ndikuitananso Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mtumiki wanga.+ Ndikuitana anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu okhala mmenemo, komanso kuti aukire mitundu yonse yokuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani, ndi kukusandutsani chinthu chodabwitsa chimene azidzachiimbira mluzu+ ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale.+
10 Ndidzathetsa phokoso lachikondwerero ndi phokoso lakusangalala m’malowo.+ Ndidzathetsanso mawu osangalala a mkwati ndi a mkwatibwi.+ Simudzamvekanso kupera kwa mphero+ ndipo simudzaonekanso kuwala kwa nyale.+
11 Dziko lonseli lidzakhala bwinja, chinthu chodabwitsa, ndipo mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka 70.”’+
12 “‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwanira,+ ndidzabwezera mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo zolakwa zawo.+ Ndidzabwezera zolakwa za dziko la Akasidi+ ndipo dziko lawolo lidzakhala mabwinja mpaka kalekale,’+ watero Yehova.
13 Mawu anga onse amene ndinanena motsutsana ndi dzikolo ndidzawakwaniritsa. Ndidzakwaniritsa zonse zolembedwa m’buku ili, zimene Yeremiya wanenera kuti zidzachitikira mitundu yonse.+
14 Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu otchuka+ agwiritsa ntchito anthu anga monga antchito awo.+ Chotero ndidzawabwezera mogwirizana ndi zochita zawo ndiponso mogwirizana ndi ntchito za manja awo.’”+
15 Yehova Mulungu wa Isiraeli anandiuza kuti: “Landira chikho ichi chimene chili m’dzanja langa. Mmenemu muli vinyo wa mkwiyo ndipo ukamwetse mitundu yonse imene ndikukutumizako.+
16 Iwo akamwe ndi kudzandira uku ndi uku ndipo akakhale ngati anthu amisala chifukwa cha lupanga limene ndikuwatumizira pakati pawo.”+
17 Choncho ndinatenga chikho chija chimene chinali m’dzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako.+
18 Mitunduyo ndi iyi: Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake. Ndinawamwetsa kuti mizinda yawo ikhale bwinja, chinthu chodabwitsa+ chimene anthu azidzachiimbira mluzu, ndiponso kuti ikhale yotembereredwa. Zimenezi zatsala pang’ono kuchitika.+
19 Ndinamwetsanso Farao mfumu ya Iguputo, atumiki ake, akalonga ake ndi anthu ake onse,+
20 khamu lonse la anthu a mitundu yosiyanasiyana, mafumu onse a dziko la Uzi,+ mafumu onse a dziko la Afilisiti,+ Asikeloni,+ Gaza,+ Ekironi+ ndi otsala onse a ku Asidodi,+
21 Edomu,+ Mowabu+ ndi ana a Amoni,+
22 mafumu onse a Turo,+ mafumu onse a Sidoni+ ndi mafumu a pachilumba cha m’nyanja.
23 Ndinamwetsanso Dedani,+ Tema,+ Buza, onse odulira ndevu zawo zam’mbali,+
24 mafumu onse a Aluya,+ mafumu onse a anthu a mitundu yosiyanasiyana amene amakhala m’chipululu,
25 mafumu onse a Zimiri, mafumu onse a Elamu,+ mafumu onse a Amedi,+
26 mafumu onse akumpoto, akutali ndi apafupi, mmodzi ndi mmodzi wa iwo, ndipo ndinamwetsanso maufumu ena onse a padziko lapansi. Mfumu ya Sesaki+ nayonso idzamwa pambuyo pa onsewa.
27 “Ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Imwani, muledzere, musanze ndi kugwa osadzukanso+ chifukwa cha lupanga limene ndikukutumizirani pakati panu.”’+
28 Ngati angakakane kulandira chikhochi m’manja mwako kuti amwe ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Mumwabe basi.+
29 Ndipo taonani! pobweretsa tsoka, ndiyamba ndi mzinda wotchedwa ndi dzina langa.+ Kodi inuyo mukufuna kuti musalandire chilango?”’+
“‘Chilangochi sichikuphonyani pakuti ndikuitana lupanga kuti liukire anthu onse okhala padziko lapansi,’ watero Yehova wa makamu.
30 “Ndiyeno iweyo, unenere mawu onsewa, ndipo anthuwo uwauze kuti, ‘Yehova adzabangula ngati mkango ali kumwamba,+ ndipo adzafuula ali kumalo ake oyera kumene amakhala.+ Iye adzabanguliradi malo ake okhalapo a padziko lapansi. Adzaimbira anthu onse okhala padziko lapansi nyimbo yofanana ndi imene anthu oponda mphesa amaimba.’+
31 “‘Phokoso lidzamveka kumalekezero a dziko lapansi, pakuti Yehova akufuna kuimba mlandu mitundu ya anthu.+ Iye mwini adzalimbana ndi anthu onse powaweruza.+ Anthu oipa adzawapha ndi lupanga,’+ watero Yehova.
32 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Taonani! Tsoka likuyenda kuchokera mu mtundu wina kupita mu mtundu wina,+ ndipo mkuntho wamphamvu udzafika kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
33 Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi.+ Sadzawalira maliro, kuwasonkhanitsa pamodzi, kapena kuwaika m’manda.+ Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.’+
34 “Fuulani, ndipo lirani abusa inu!+ Gubuduzikani pafumbi+ inu anthu otchuka pakati pa gulu la nkhosa,+ chifukwa masiku a kuphedwa ndi kubalalitsidwa kwanu afika+ ndipo mudzagwa ndi kuphwanyika ngati chiwiya chosiririka!+
35 Abusa alibe malo othawirako, ndipo njira yothawira ya anthu otchuka pakati pa gulu la nkhosa yatha.+
36 Tamverani! Kulira kwa abusa ndi anthu otchuka pakati pa gulu la nkhosa, chifukwa Yehova akuwononga malo awo odyetserako nkhosa.
37 Malo okhalako amtendere asanduka opanda chamoyo chilichonse chifukwa cha mkwiyo woyaka moto wa Yehova.+
38 Iye watuluka m’malo ake okhalamo ngati mkango wamphamvu wolusa.+ Dziko lawo lasanduka chinthu chodabwitsa chifukwa cha lupanga loopsa komanso chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto.”+