Yeremiya 34:1-22

34  Yehova analankhula ndi Yeremiya pamene Nebukadirezara mfumu ya Babulo,+ gulu lake lonse lankhondo,+ maufumu onse a padziko lapansi, maulamuliro amene anali m’manja mwake+ ndiponso pamene mitundu yonse ya anthu inali kumenyana ndi mzinda wa Yerusalemu, ndi mizinda yonse yozungulira mzindawo.+ Iye anati:  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Pita ukauze Zedekiya mfumu ya Yuda,+ kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ine ndikupereka mzinda uwu m’manja mwa mfumu ya Babulo+ ndipo idzautentha.+  Iweyo sudzazemba kuti asakugwire chifukwa adzakugwira ndithu ndi kukupereka m’manja mwake.+ Udzaonana ndi mfumu ya Babulo+ maso ndi maso, ndipo idzalankhula nawe ndi kupita nawe ku Babulo.’  Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda,+ imva mawu a Yehova akuti, ‘Ponena za iwe, Yehova wanena kuti: “Sudzafa ndi lupanga.  Udzafa mu mtendere.+ Anthu adzakufukizira zinthu zonunkhira+ ngati mmene anachitira ndi makolo ako, mafumu amene analipo iwe usanabadwe.+ Polira maliro ako adzanena kuti,+ ‘Kalanga ine mbuyanga!’+ pakuti ‘Ine ndalankhula mawu amenewa,’ watero Yehova.”’”’”  Pamenepo mneneri Yeremiya anauza Zedekiya, mfumu ya Yuda, mawu onsewa+ ali ku Yerusalemu.  Anamuuza mawu amenewa pamene magulu ankhondo a mfumu ya Babulo anali kumenyana ndi Yerusalemu ndi mizinda ina yonse ya mu Yuda,+ kuphatikizapo Lakisi+ ndi Azeka.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndipo ndi imene inali isanawonongedwe pamizinda ya mu Yuda.+  Yehova anauza Yeremiya mawu pamene Mfumu Zedekiya inachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti alengeze ufulu,+  kuti aliyense wa iwo amasule wantchito wake wamwamuna kapena wamkazi, mwamuna wachiheberi+ kapena mkazi wachiheberi ndi kumulola kupita kwawo mwaufulu. Anachita izi kuti anthuwo asagwiritsenso ntchito Myuda mnzawo, amene ndi m’bale wawo ngati wantchito wawo.+ 10  Choncho akalonga onse+ anamvera, chimodzimodzinso anthu onse amene anachita pangano kuti aliyense wa iwo alole wantchito wake wamwamuna kapena wamkazi kupita kwawo mwaufulu. Anamvera ndi kuwalola kuchoka kuti asawagwiritsenso ntchito monga atumiki awo.+ 11  Koma pambuyo pake, iwo anatembenuka+ ndi kuyamba kutenganso amuna ndi akazi antchitowo amene anawalola kupita kwawo mwaufulu ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito monga antchito awo aamuna ndi aakazi.+ 12  Pamenepo Yehova anauza Yeremiya mawu, ndipo Yehova anati: 13  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ine ndinachita pangano ndi makolo anu+ pamene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ kumene munali akapolo.+ Ndinapangana nawo kuti: 14  “Kumapeto kwa zaka 7, aliyense wa inu, azimasula m’bale wake,+ Mheberi+ amene anagulitsidwa kwa inu+ ndiponso amene wakutumikirani kwa zaka 6. Muzimulola kuchoka mwaufulu kuti apite kwawo.” Koma makolo anu sanandimvere ndipo sanatchere khutu lawo.+ 15  Koma inu munatembenuka ndi kuchita zolungama pamaso panga mwa kulengeza ufulu, aliyense kwa mnzake. Munachita pangano pamaso panga,+ m’nyumba imene ikutchedwa ndi dzina langa.+ 16  Kenako mwatembenukanso+ ndi kuipitsa dzina langa+ komanso aliyense wa inu watenganso wantchito wake wamkazi ndi wamwamuna amene munawalola kuchoka mwaufulu, zimenenso iwo anagwirizana nazo. Inu mwawatenganso kukhala antchito anu aamuna ndi antchito anu aakazi.’+ 17  “Choncho Yehova wanena kuti, ‘Inu simunamvere mawu anga moti simunapitirize kulengeza ufulu,+ aliyense kwa m’bale wake ndi kwa mnzake. Tsopano ine ndikulengeza ufulu kwa inu,’+ watero Yehova. ‘Inu mudzafa ndi lupanga,+ mliri+ ndi njala yaikulu.+ Ndidzakusandutsani chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho.+ 18  Anthu amene akupatuka pa pangano langa+ mwa kusatsatira mawu a m’pangano limene iwo anachita pamaso panga, ndidzawapereka kwa adani. Iwo anachita pangano limeneli mwakudula pakati+ mwana wa ng’ombe wamphongo ndi kudutsa pakati pake.+ 19  Amene apatuka pa panganoli ndi akalonga a Yuda, akalonga a Yerusalemu,+ nduna za panyumba ya mfumu, ansembe ndi anthu onse a m’dzikoli amene anadutsa pakati pa mwana wa ng’ombe wodulidwa pakatiyo . . . 20  Anthu amenewa ndidzawapereka m’manja mwa adani awo ndi m’manja mwa onse ofuna moyo wawo.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.+ 21  Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda+ ndi akalonga ake ndidzawapereka m’manja mwa adani awo, m’manja mwa anthu ofuna moyo wawo ndiponso m’manja mwa magulu ankhondo a mfumu ya ku Babulo+ amene akubwerera osakuthirani nkhondo.’+ 22  “Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikulamula ndi kubweretsanso adaniwo kumzinda uno.+ Iwo adzamenyana ndi mzindawu ndipo adzaulanda ndi kuutentha.+ Pamenepo, mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa bwinja ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.’”+

Mawu a M'munsi