Yeremiya 1:1-19

1  Mawu a Yeremiya+ mwana wa Hilikiya,* mmodzi wa ansembe a ku Anatoti,+ m’dera la Benjamini.+  Yeremiya analandira mawu ochokera kwa Yehova m’masiku a Yosiya+ mwana wa Amoni.+ Yosiya anali mfumu ya Yuda, ndipo Yeremiya analandira mawuwo m’chaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiyayo.+  Mawuwo anapitiriza kufika kwa Yeremiya m’masiku a Yehoyakimu+ mfumu ya Yuda, mwana wa Yosiya, mpaka m’chaka cha 11, kumapeto kwa ulamuliro wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, mwana wa Yosiya, pamene anthu a mu Yerusalemu anatengedwa kupita ku ukapolo m’mwezi wachisanu.*+  Ndiyeno Yehova anayamba kulankhula nane kuti:  “Ndisanakuumbe m’mimba,+ ndinakudziwa,+ ndipo usanatuluke m’mimbamo, ndinakusankha kuti uchite ntchito yopatulika.+ Ndinakusankha kuti ukhale mneneri ku mitundu ya anthu.”  Koma ine ndinati: “Haa! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ine sindingathe kulankhula+ chifukwa ndine mwana.”+  Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Usanene kuti, ‘Ndine mwana.’ Koma upite kwa anthu onse amene ndidzakutumako. Ndipo ukanene zonse zimene ndidzakulamula kuti ukanene.+  Usachite mantha chifukwa cha nkhope zawo,+ pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse.’”+  Pamenepo Yehova anatambasula dzanja lake ndi kukhudza pakamwa panga.+ Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Ndaika mawu anga m’kamwa mwako.+ 10  Taona, lero ndakupatsa mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu,+ kuti uzule, ugwetse,+ uwononge ndi kupasula, komanso kuti umange ndi kubzala.”+ 11  Ndiyeno Yehova anapitirizabe kulankhula nane, ndipo anati: “Ukuona chiyani Yeremiya?” Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mphukira ya mtengo wa amondi.”* 12  Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Waona bwino, chifukwa ndikhalabe wogalamuka* kuti ndikwaniritse mawu anga.”+ 13  Kenako Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti: “Ukuona chiyani?” Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mphika wakukamwa kwakukulu umene uli pamoto, ndipo motowo aupemerera kuti uyake kwambiri. Mphikawo wafulatira kumpoto.” 14  Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Tsoka lidzamasulidwa kuchokera kumpoto ndipo lidzagwera anthu onse okhala m’dzikoli.+ 15  Pakuti Yehova wanena kuti,+ ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto. Ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi kukhazikitsa mpando wake wachifumu pazipata za Yerusalemu.+ Iwo adzaukira mpanda wake wonse ndi mizinda yonse ya Yuda.+ 16  Ndipo ine ndidzapereka zigamulo zanga pa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda chifukwa cha zoipa zawo zonse,+ pakuti iwo andisiya ine+ ndipo amafukiza nsembe zautsi kwa milungu ina+ ndi kugwadira ntchito za manja awo.’+ 17  “Koma iwe umange m’chiuno+ ndipo upite kukawauza zonse zimene ndikulamule kuti ukawauze. Usagwidwe ndi mantha chifukwa cha iwo,+ kuopera kuti ndingakuchititse kugwidwa ndi mantha pamaso pawo. 18  Koma ine lero ndakusandutsa mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, mzati wachitsulo ndi makoma amkuwa+ kuti dziko lonseli lisakugonjetse.+ Ndithu kuti mafumu a Yuda, akalonga ake, ansembe ake ndi anthu a m’dzikoli asakugonjetse.+ 19  Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzapambana,+ pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe+ kuti ndikulanditse.’”+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza “Gawo Langa Ndi Yehova.”
Umenewu ndi mwezi wa Abi. Onani Zakumapeto 13.
M’Chiheberi mawu akuti “mtengo wa amondi” amatanthauza “wogalamuka” chifukwa chakuti ndi umodzi mwa mitengo yoyambirira kutulutsa maluwa. Izi zikugwirizana ndi mawu a Yehova pa vesi 12.
Onani mawu a m’munsi pa vesi 11.