Yeremiya 36:1-32

36  Ndiyeno m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti:  “Tenga mpukutu+ ndi kulembamo mawu onse+ amene ndakuuza okhudza chilango chimene ndidzapatsa Isiraeli, Yuda+ ndi mitundu yonse ya anthu.+ Ulembe mawu onse amene ndakuuza kuchokera nthawi imene ndinalankhula nawe m’masiku a Yosiya kufikira lero.+  Mwina anthu a m’nyumba ya Yuda adzamva za masoka onse amene ndikufuna kuwagwetsera+ ndipo aliyense abwerera ndi kusiya njira yake yoipa.+ Akatero, ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndi machimo awo.”+  Ndiyeno Yeremiya anaitana Baruki+ mwana wa Neriya kuti adzamuuze mawu onse amene Yehova anauza Yeremiyayo ndi kuti Baruki alembe mawuwo mumpukutu.+  Pamenepo Yeremiya anauza Baruki kuti: “Ine anditsekera ndipo sindingathe kukalowa m’nyumba ya Yehova.+  Choncho iweyo upite kukawerenga mokweza mawu a mumpukutu. Ukawerenge mawu amene walembamo, mawu a Yehova+ amene ndakuuza. Ukawerenge mokweza pamaso pa anthu onse m’nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya.+ Ukawerengenso pamaso pa anthu onse a ku Yuda amene akubwera kuchokera m’mizinda yawo.+  Mwina ukatero Yehova adzamva pempho lawo lakuti awakomere mtima+ ndipo aliyense adzabwerera kusiya njira yake yoipa,+ chifukwa Yehova wanena kuti adzasonyeza anthu awa mkwiyo wake waukulu ndi ukali wake.”+  Choncho Baruki+ mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamulamula, kuti apite kunyumba ya Yehova kukawerenga mokweza mawu a Yehova olembedwa mumpukutumo.+  Ndiyeno m’chaka chachisanu cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 9,+ analengeza kuti anthu onse a mu Yerusalemu ndi anthu onse amene anali kubwera ku Yerusalemu kuchokera m’mizinda ya Yuda asale kudya pamaso pa Yehova.+ 10  Tsopano Baruki anayamba kuwerenga mpukutuwo mokweza pamaso pa anthu onse. Anayamba kuwerenga mawu onse a Yeremiya panyumba ya Yehova. Anachita izi m’chipinda chodyera+ cha Gemariya+ mwana wa Safani+ wokopera Malemba,+ m’bwalo lakumtunda, pakhomo la chipata chatsopano cha nyumba ya Yehova.+ 11  Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani,+ anamva mawu onse a Yehova amene anali mumpukutumo. 12  Pamenepo anapita kunyumba ya mfumu, kuchipinda chodyera cha mlembi, kumene akalonga onse anali atakhala pansi. Kumeneko kunali Elisama+ mlembi, Delaya+ mwana wa Semaya, Elinatani+ mwana wa Akibori,+ Gemariya+ mwana wa Safani,+ Zedekiya mwana wa Hananiya ndi akalonga ena onse. 13  Atafika kumeneko Mikaya+ anawauza mawu onse amene anamva pamene Baruki anawerenga mokweza mumpukutu pamaso pa anthu onse.+ 14  Zitatero, akalonga onse anatumiza Yehudi+ mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusa, kukaitana Baruki+ kuti: “Tenga mpukutu umene wawerenga mokweza pamaso pa anthu onse ndipo ubwere nawo kuno.” Pamenepo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo ndi kupita kwa iwo.+ 15  Ndiyeno akalongawo anamuuza kuti: “Khala pansi, ndipo uwerenge mokweza kuti timve.” Choncho Baruki+ anawawerengera mpukutuwo mokweza. 16  Tsopano atamva mawu onsewa anayang’anana mwamantha, ndipo anauza Baruki kuti: “Ndithu, tikauza mfumu mawu onsewa.”+ 17  Kenako anafunsa Baruki kuti: “Tiuze, zatheka bwanji kuti ulembe mawu onsewa kuchokera pakamwa pake?”+ 18  Pamenepo Baruki anawauza kuti: “Iye anali kundiuza mawu onsewa ndipo ine ndinali kulemba mumpukutuwu ndi inki.”+ 19  Zitatero, akalongawo anauza Baruki kuti: “Pita, iweyo ndi Yeremiya mukabisale ndipo munthu aliyense asadziwe kumene mwapita.”+ 20  Akalongawo anasiya mpukutuwo m’chipinda chodyera+ cha Elisama+ mlembi. Kenako analowa m’bwalo+ kuti akaonane ndi mfumu, ndipo anayamba kuuza mfumu nkhani yonse yokhudza mpukutuwo. 21  Mfumu itamva zimenezi inatuma Yehudi+ kuti akatenge mpukutuwo. Iye anakatenga mpukutuwo m’chipinda chodyera cha Elisama+ mlembi,+ moti Yehudiyo anayamba kuwerenga mokweza pamaso pa mfumu ndi akalonga onse amene anaimirira pafupi ndi mfumuyo. 22  Pa nthawiyi mfumu inali itakhala m’nyumba imene inali kukhala m’nyengo yozizira,+ ikuwotha moto wa mumbaula.+ Umenewu unali mwezi wa 9.*+ 23  Ndiyeno zimene zinali kuchitika n’zakuti, Yehudi akawerenga zigawo zitatu kapena zinayi za mpukutuwo, mfumu inali kudula mpukutuwo ndi mpeni wa mlembi ndi kuponya chidutswacho pamoto umene unali mumbaula. Inachita izi kufikira mpukutu wonsewo itauponya pamotopo.+ 24  Iwo sanachite mantha+ ndipo mfumu ndi atumiki ake onse amene anali kumvetsera mawu amenewa sanang’ambe zovala zawo.+ 25  Ngakhale kuti Elinatani,+ Delaya+ ndi Gemariya+ anachonderera mfumu kuti isatenthe mpukutuwo, mfumuyo sinawamvere.+ 26  Komanso mfumu inalamula Yerameeli mwana wa mfumu, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti akagwire Baruki mlembi ndi mneneri Yeremiya,+ koma Yehova anawabisa.+ 27  Mfumu itatentha mpukutu umene unali ndi mawu amene Baruki+ analemba mouzidwa ndi Yeremiya,+ Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti: 28  “Tenga mpukutu wina ndipo ulembemo mawu onse amene anali mumpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda yatentha.+ 29  Ponena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Iwe watentha mpukutu+ ndi kunena kuti, ‘N’chifukwa chiyani walemba mumpukutuwu+ kuti: “Mfumu ya Babulo idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndipo simudzapezeka nyama ndi munthu wokhalamo”?’+ 30  Choncho ponena za chilango chimene adzapatsa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Sipadzapezeka mwana wake aliyense wokhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mtembo wake adzautaya kunja+ kumene udzakhala padzuwa lotentha masana ndipo usiku udzakhala kunja kozizira. 31  Ine ndidzaimba mlandu Yehoyakimu,+ ana ake ndi atumiki ake chifukwa cha zolakwa zawo.+ Anthu amenewa komanso anthu okhala mu Yerusalemu ndi anthu a mu Yuda ndidzawagwetsera masoka onse amene ndanena.+ Ngakhale kuti ndawauza za masoka onsewa iwo sanamvere.’”’”+ 32  Pamenepo Yeremiya anatenga mpukutu wina ndi kuupereka kwa Baruki mlembi,+ mwana wa Neriya. Baruki analembamo mawu onse amene Yeremiya anamuuza,+ mawu onse amene anali mumpukutu umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha.+ Mumpukutumo anawonjezeramo mawu ena ambiri ofanana ndi a mumpukutu woyamba uja.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mwezi wa Kisilevu, dzina la mwezi wa 9 pakalendala yachiyuda imene anali kuigwiritsa ntchito atabwera kuchokera ku ukapolo. Mweziwu unali kuyamba chakumapeto kwa November mpaka pakati pa December. Onani Zakumapeto 13.