Yeremiya 40:1-16

40  Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya, pamene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anamumasula ku Rama.+ Yeremiya anali womangidwa maunyolo a m’manja pamene Nebuzaradani anamutenga pakati pa anthu a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene anali kupita ku ukapolo ku Babulo.+  Ndiyeno mkulu wa asilikaliyu anatenga Yeremiya ndi kumuuza kuti: “Yehova Mulungu wako ananeneratu za tsoka ili limene lagwera dziko lino.+  Yehova ananena za tsoka limeneli moti anatsimikiza kukwaniritsa zimene ananenazo. Anatero chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamvere mawu ake. Choncho monga mmene ukuoneramu, zimenezi zachitikadi.+  Tsopano taona! Lero ndakumasula maunyolo amene anali m’manja mwako. Ngati ungakonde kutsagana nane ku Babulo tiye, ndipo ndidzakuyang’anira.+ Koma ngati sungakonde kutsagana nane ku Babulo, tsala. Taona! Dziko lonse lili pamaso pako. Pita kulikonse kumene ungaone kuti n’kwabwino, kulikonse kumene ungakonde kupita.”+  Koma Yeremiya anali asanaganize zobwerera pamene Nebuzaradani anamuuza kuti: “Bwerera kwa Gedaliya,+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ amene mfumu ya Babulo yamuika kukhala wolamulira mizinda ya Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu ako ndipo ukapite kulikonse kumene ungakonde kupita.”+ Pamenepo mkulu wa asilikali olondera mfumu anamupatsa chakudya chapaulendo ndi mphatso ndipo anamulola kupita.+  Chotero Yeremiya anapita ku Mizipa+ kukakhala ndi Gedaliya+ mwana wa Ahikamu pakati pa anthu amene anatsala m’dzikolo.  Patapita nthawi, akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali m’madera a kunja kwa mzinda+ pamodzi ndi anthu awo, anamva kuti mfumu ya Babulo yaika Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala wolamulira dzikolo. Anamvanso kuti yamuika kuti azilamulira amuna, akazi, ana ndi anthu onyozeka m’dzikolo amene sanatengedwe kupita ku ukapolo ku Babulo.+  Choncho akuluakulu amenewa anapita kwa Gedaliya ku Mizipa. Mayina awo anali Isimaeli+ mwana wa Netaniya, Yohanani+ ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanumeti, ana a Efai Mnetofa,+ Yezaniya+ mwana wa Amaakati+ pamodzi ndi asilikali awo.+  Gedaliya+ mwana wa Ahikamu+ mwana wa Safani+ analumbira+ pamaso pa akuluakuluwo ndi asilikali awo kuti: “Musaope kutumikira Akasidi. Pitirizani kukhala m’dzikoli n’kumatumikira mfumu ya Babulo ndipo zinthu zikuyenderani bwino.+ 10  Ine ndikhala ku Mizipa+ kuno kuti ndizikuimirani kwa Akasidi amene adzabwera kwa ife. Koma inu, sonkhanitsani vinyo,+ zipatso za m’chilimwe* ndi mafuta ndi kuziika m’ziwiya zanu ndipo muzikhala m’mizinda imene mwaitenga kukhala yanu.” 11  Pamenepo Ayuda onse amene anali kukhala ku Mowabu, amenenso anali kukhala pakati pa ana a Amoni, amene anali ku Edomu ndi ena amene anali m’mayiko ena onse+ anamva kuti mfumu ya Babulo yaika Gedaliya+ mwana wa Ahikamu mwana wa Safani kukhala wolamulira anthu otsala ku Yuda. 12  Ndiyeno Ayuda onse anayamba kubwerera kuchokera kumadera onse kumene anathawira. Anali kubwera m’dziko la Yuda kwa Gedaliya ku Mizipa.+ Iwo anasonkhanitsa vinyo ndi zipatso za m’chilimwe zochuluka kwambiri. 13  Nayenso Yohanani+ mwana wa Kareya+ ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali m’madera a kunja kwa mzinda,+ anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. 14  Iwo anauza Gedaliya kuti: “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni+ watumiza Isimaeli+ mwana wa Netaniya+ kuti adzakuphe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanakhulupirire zimenezo.+ 15  Ndiyeno Yohanani+ mwana wa Kareya anauza Gedaliya pamalo obisika ku Mizipa kuti: “Ndikufuna kupita tsopano lino kukapha Isimaeli mwana wa Netaniya pakuti palibe amene adzadziwa.+ N’chifukwa chiyani iyeyo akufuna kukupha? N’chifukwa chiyani akufuna kuti anthu onse a mu Yuda amene akubwera kwa iwe amwazike, ndi kuti anthu otsala mu Yuda awonongeke?”+ 16  Koma Gedaliya+ mwana wa Ahikamu+ anauza Yohanani mwana wa Kareya kuti: “Usachite zimenezi. Zimene ukunena zokhudza Isimaeli si zoona.”+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.