Yeremiya 31:1-40

31  “Pa nthawi imeneyo ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Isiraeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga,”+ watero Yehova.  Yehova wanena kuti: “Anthu amene anapulumuka ku lupanga, ndinawakomera mtima m’chipululu,+ pamene Isiraeli anali kupita kumalo ake ampumulo.”+  Yehova anabwera kwa ine kuchokera kutali, ndipo anati: “Ine ndakukonda ndipo ndidzakukonda mpaka kalekale.+ N’chifukwa chake ndakukoka mwa kukoma mtima kwanga kosatha.+  Chotero ndidzakumanganso ndipo udzakhazikika,+ iwe namwali wa Isiraeli. Udzanyamula maseche ndi kupita kukavina pamodzi ndi anthu amene akuseka.+  Udzabzala mpesa kumapiri a ku Samariya.+ Obzala mpesawo adzadya zipatso zake.+  Pakuti tsiku lidzafika, pamene alonda amene ali m’mapiri a Efuraimu adzafuula kuti, ‘Nyamukani amuna inu, tiyeni tipite ku Ziyoni, kwa Yehova Mulungu wathu.’”+  Yehova wanena kuti: “Fuulirani Yakobo mosangalala, fuulani kwambiri muli patsogolo pa mitundu ina ya anthu.+ Lengezani zimenezi.+ Tamandani Mulungu ndi kunena kuti, ‘Inu Yehova, pulumutsani anthu anu, otsalira a Isiraeli.’+  Ine ndikuwabweretsa kuchokera kudziko la kumpoto,+ ndipo ndikuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Pakati pawo padzakhala anthu akhungu, olumala, akazi apakati komanso akazi amene atsala pang’ono kubereka.+ Adzabwerera kumalo ano ali mpingo waukulu.+  Adzabwera akulira,+ ndipo ndidzayankha kuchonderera kwawo kuti ndiwakomere mtima. Ndidzawayendetsa kupita kuzigwa za madzi.+ Ndidzawayendetsa m’njira zabwino mmene sadzapunthwa. Pakuti ine ndakhala Tate wa Isiraeli,+ ndipo Efuraimu ndi mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa.”+ 10  Inu mitundu ya anthu, imvani mawu a Yehova, ndipo mulengeze mawuwo pazilumba zakutali,+ kuti: “Amene wamwaza Isiraeli ndiye adzamusonkhanitsanso+ ndipo adzamusunga mmene m’busa amasungira nkhosa zake.+ 11  Pakuti Yehova adzawombola Yakobo,+ ndipo adzamutenganso kumuchotsa m’manja mwa munthu wamphamvu kuposa iyeyo.+ 12  Pamenepo iwo adzabwera ndi kufuula mosangalala pamwamba pa phiri la Ziyoni.+ Nkhope zawo zidzawala chifukwa cha ubwino wa Yehova.+ Zidzawalanso chifukwa cha mbewu, vinyo watsopano,+ mafuta, ana a nkhosa ndi ana a ng’ombe.+ Moyo wawo udzakhala ngati munda wothiriridwa bwino+ ndipo sadzakhalanso ofooka.”+ 13  “Pa nthawi imeneyo, namwali, anyamata ndi amuna achikulire, onse pamodzi adzasangalala ndipo adzavina.+ Ndidzawachotsera chisoni chawo, moti kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo ndipo ndidzawatonthoza ndi kuwasangalatsa.+ 14  Ansembe ndidzawatsitsimutsa ndi chakudya chochuluka,+ ndipo anthu anga ndidzawakhutiritsa ndi ubwino wanga,”+ watero Yehova. 15  “Yehova wanena kuti, ‘Mawu amveka ku Rama.+ Kwamveka kulira mofuula ndiponso momvetsa chisoni.+ Rakele+ akulirira ana ake.+ Iye wakana kutonthozedwa pamene akulirira ana ake,+ chifukwa ana akewo kulibenso.’”+ 16  Yehova wanena kuti: “‘Tonthola, usalire. Usagwetsenso misozi,+ pakuti ulandira mphoto ya ntchito zako,’ watero Yehova, ‘ndipo anawo adzabwerera kuchokera kudziko la mdani.’+ 17  “‘Uli ndi tsogolo labwino+ ndipo ana ako adzabwerera kudziko lawo,’+ watero Yehova.” 18  “Ndamva Efuraimu akudzilirira+ kuti, ‘Mwandidzudzula kuti ndiwongolere.+ Ndinali ngati mwana wa ng’ombe wosaphunzitsidwa.+ Ndithandizeni kubwerera ndipo ndidzabwereradi,+ pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.+ 19  Nditabwerera kwa inu ndinadzimvera chisoni.+ Mutandithandiza kuzindikira ndinadzimenya pantchafu chifukwa cha chisoni.+ Ndinachita manyazi ndipo ndinanyazitsidwa+ chifukwa cha chitonzo cha paubwana wanga.’”+ 20  “Kodi Efuraimu si mwana wanga wamtengo wapatali, kapena mwana wanga wokondedwa?+ Pamlingo umene ndalankhula zomulanga, ndidzakumbukira kumuchitira zabwino pamlingo womwewo.+ N’chifukwa chake m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha iye.+ Mosalephera ndidzamumvera chisoni,”+ watero Yehova. 21  “Udziikire zizindikiro za mumsewu. Udziikire zikwangwani.+ Ika mtima wako panjirayo, njira imene uyenera kuyendamo.+ Bwerera iwe namwali wa Isiraeli. Bwerera kumizinda yakoyi.+ 22  Kodi udzapatukira uku ndi uku kufikira liti,+ iwe mwana wamkazi wosakhulupirika?+ Yehova walenga chinthu chatsopano padziko lapansi. Chinthucho n’chakuti, mkazi wamba adzakupatira mwamuna wamphamvu.” 23  Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa anthu a mtundu wawo amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina, iwo adzanena mawu awa m’dziko la Yuda ndi m’mizinda yake kuti, ‘Yehova akudalitse iwe+ malo olungama okhalamo,+ iwe phiri lopatulika.’+ 24  Ndipo Yuda ndi mizinda yake yonse adzakhala pamodzi m’dzikolo. Mudzakhalanso alimi ndi anthu oweta ziweto.+ 25  Pakuti ndidzatsitsimutsa wolefuka ndipo ndidzalimbitsa wofooka aliyense.”+ 26  Pamenepo, ndinagalamuka ndi kuyamba kuona. Ndinali nditagona tulo tokoma. 27  “Taonani! Masiku adzafika, pamene ndidzachititsa nyumba ya Isiraeli ndi nyumba ya Yuda kukhalanso ndi anthu ochuluka ndiponso ziweto zochuluka,” watero Yehova.+ 28  “Monga mmene ndakhalira ndikufunafuna mpata+ kuti ndiwazule, kuwagwetsa, kuwapasula, kuwawononga ndi kuwasakaza,+ ndidzakhalanso nawo tcheru kuti ndiwamange ndi kuwabzala,”+ watero Yehova. 29  “Masiku amenewo sadzanenanso kuti, ‘Abambo ndiwo anadya mphesa yosapsa koma mano a ana awo ndiwo anayayamira.’*+ 30  Koma munthu aliyense adzafa chifukwa cha zolakwa zake.+ Mano a munthu aliyense wodya mphesa yosapsa ndiwo adzayayamira.” 31  “Taonani! Masiku adzafika, pamene ndidzachita pangano latsopano+ ndi nyumba ya Isiraeli+ komanso ndi nyumba ya Yuda,”+ watero Yehova. 32  “Koma pangano limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo.+ ‘Pangano langa limenelo analiphwanya+ ngakhale kuti ine ndinali mwamuna wawo,’+ watero Yehova.” 33  “Pangano+ limene ndidzapangane ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa masiku amenewo ndi ili:+ Ndidzaika chilamulo changa mwa iwo+ ndipo ndidzachilemba mumtima mwawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga,”+ watero Yehova. 34  “Munthu sadzaphunzitsanso mnzake kapena m’bale wake+ kuti, ‘Mum’dziwe Yehova!’+ pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu,”+ watero Yehova. “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.”+ 35  Yehova ndiye Wopereka dzuwa kuti liziwala masana,+ woikira mwezi malamulo,+ wopereka nyenyezi+ kuti ziziwala usiku,+ amene amavundula nyanja kuti mafunde ake achite phokoso.+ Wochita zimenezi dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ Iye wanena kuti: 36  “‘Ngati malamulo amenewa angachotsedwe pamaso panga,+ ndiye kuti anthu amene ndi mbewu ya Isiraeli sadzakhala mtundu wokhala pamaso panga nthawi zonse,’+ watero Yehova.” 37  Yehova wanena kuti: “‘Ngati kumwamba kungayezedwe ndipo ngati maziko a dziko lapansi angafufuzidwe,+ inenso ndingakane anthu onse amene ndi mbewu ya Isiraeli chifukwa cha zonse zimene achita,’+ watero Yehova.” 38  “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene anthu adzamangira+ Yehova mzinda kuyambira pa Nsanja ya Hananeli+ mpaka ku Chipata cha Pakona.+ 39  Chingwe choyezera+ chidzachokera kumeneko n’kulunjika kuphiri la Garebi ndipo chidzazungulira mpaka ku Gowa. 40  Chigwa chonse cha mitembo+ ndi cha phulusa+ losakanizika ndi mafuta, masitepe onse mpaka kukafika kuchigwa cha Kidironi,+ mpaka kukona ya Chipata cha Hatchi+ moyang’anana ndi kotulukira dzuwa, zidzakhala zoyera kwa Yehova.+ Mzindawu sudzazulidwa ndipo sudzapasulidwanso mpaka kalekale.”+

Mawu a M'munsi

Mano amayayamira munthu akadya zinthu zowawasa. Ena amati “kuchita dziru.”