Yeremiya 12:1-17

12  Inu Yehova, ndinu Mulungu wolungama.+ Ndikabweretsa dandaulo kwa inu, ndipo ndikalankhula za chiweruzo chanu, mumachita chilungamo. Koma n’chifukwa chiyani anthu oipa, zinthu zikuwayendera bwino?+ N’chifukwa chiyani onse ochita chinyengo amakhala opanda nkhawa iliyonse?  Munawabzala ndipo iwo anazika mizu. Akupitirizabe kukula ndi kubala zipatso. Amakutchulani pafupipafupi, koma impso zawo zili kutali kwambiri ndi inu.+  Inu Yehova, mumandidziwa bwino.+ Mumandiona ndipo mumasanthula mtima wanga kuti muone ngati uli wokhulupirika kwa inu.+ Apatuleni ngati nkhosa zimene zikukaphedwa,+ ndipo aikeni padera kuyembekezera tsiku lokaphedwa.  Kodi dzikoli lifotabe mpaka liti?+ Kodi zomera za m’minda yonse ziumabe mpaka liti?+ Chifukwa chakuti anthu a m’dzikoli ndi oipa, zilombo zakutchire ndi zolengedwa zouluka zinachoka.+ Pakuti anthuwo akuti: “Iye sakuona zimene zidzatichitikira m’tsogolo.”  Pakuti unali kuthamanga ndi anthu oyenda pansi ndipo anali kukutopetsa, ndiye ungapikisane bwanji ndi mahatchi?+ Kodi ukumva kukhala wotetezeka m’dziko lamtendere?+ Ndiye udzatani ukadzakhala m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano?+  Abale ako komanso anthu a m’nyumba ya bambo ako akuchitira chinyengo,+ ndipo mofuula akukunenera zinthu zoipa ali kumbuyo kwako. Usawakhulupirire m’pang’ono pomwe, ngakhale kuti akukuuza mawu abwino.+  “Ndasiya nyumba yanga.+ Ndasiya cholowa changa.+ Wokondedwa wanga ndamupereka m’manja mwa adani ake.+  Wokondedwa wangayo, amene ndi cholowa changa, wakhala ngati mkango kwa ine m’nkhalango ndipo wandibangulira. N’chifukwa chake ndadana naye.+  Cholowa changa+ chili ngati mbalame yanthenga zamitundumitundu, yodya nyama. Mbalame zodya nyama zaizungulira.+ Bwerani, sonkhanani pamodzi inu nyama zonse zam’tchire. Bwerani ndi anzanu kuti mudzaidye.+ 10  Abusa ambiri+ awononga munda wanga wa mpesa.+ Apondaponda cholowa changa.+ Cholowa changa chosiririka+ achisandutsa bwinja moti palibe aliyense amene akukhalamo. 11  Cholowa changacho achisandutsa bwinja+ moti chafota ndipo chawonongeka.+ Dziko lonse lakhala bwinja ndipo palibe aliyense amene zikumukhudza.+ 12  Anthu ofunkha adutsa m’njira zonse zodutsidwadutsidwa za m’chipululu. Lupanga la Yehova likuwononga anthu kuchokera kumalekezero a dziko kukafika kumalekezero ena a dziko.+ Palibe mtendere kwa munthu aliyense. 13  Afesa tirigu koma akolola minga.+ Agwira ntchito mpaka kudwala nayo, koma osapeza phindu lililonse.+ Iwo adzachita manyazi ndi zokolola zawo chifukwa mkwiyo waukulu wa Yehova udzawayakira.” 14  Yehova wanena kuti: “Anthu onse oipa amene ndinayandikana nawo + amene akukhudza cholowa chimene ndinapatsa anthu anga Aisiraeli kuti chikhale chawo,+ ndikuwazula pamalo awo.+ Ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pawo.+ 15  Ndiyeno ndikadzawazula ndidzawachitiranso chifundo+ moti ndidzawabwezeretsa. Ndidzabwezeretsa aliyense pacholowa chake, ndiponso pamalo ake.”+ 16  “Ndiyeno anthu a mitundu ina akadzaphunzira njira za anthu anga ndi kulumbira m’dzina langa+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo!’ monga mmene iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira m’dzina la Baala,+ anthu a mitundu inawo adzakhazikika pakati pa anthu anga.+ 17  Koma akadzapanda kumvera, ine ndidzazula anthu a mitundu imeneyo. Ndidzawazula ndi kuwawononga,”+ watero Yehova.

Mawu a M'munsi