Yeremiya 48:1-47

48  Ponena za Mowabu+ Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti:+ “Tsoka Nebo+ chifukwa wafunkhidwa! Mzinda wa Kiriyataimu+ walandidwa ndipo anthu ake achita manyazi. Anthu okhala m’malo okwezeka achitetezo achita manyazi ndipo achita mantha.+  Mowabu sakutamandidwanso.+ Anthu a ku Hesiboni+ amukonzera chiwembu ndipo akunena kuti: ‘Bwerani amuna inu, tiyeni tifafanize Mowabu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’+ “Inunso anthu a ku Madimeni khalani chete. Lupanga likukutsatirani.  Ku Horonaimu+ kwamveka kulira kofuula, kufunkha ndi chiwonongeko chachikulu.  Mowabu wawonongeka.+ Kulira kwa ana ake kwamveka.  Anthu akupita ku Luhiti+ akulira. Akupita akulira kwambiri. Amene akutsika kuchokera ku Horonaimu akufuula mowawidwa mtima chifukwa amva za chiwonongeko.+  “Thawani. Pulumutsani moyo wanu+ ndipo mukhale ngati mtengo umene uli wokhawokha m’chipululu.+  Inu mudzagwidwa ndi adani chifukwa mukudalira ntchito zanu ndi chuma chanu.+ Kemosi+ adzatengedwa kupita ku ukapolo+ pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake.+  Wofunkha adzalowa mumzinda uliwonse+ ndipo sipadzapezeka mzinda wopulumuka.+ Zigwa ndi malo athyathyathya adzawonongedwa ndithu, izi ndi zimene Yehova wanena.  “Anthu inu perekani chizindikiro cha pamsewu kwa anthu a ku Mowabu pakuti adzachoka pamene dziko lawo likusanduka bwinja.+ Mizinda yake idzasanduka chinthu chodabwitsa ndipo simudzapezeka aliyense wokhalamo.+ 10  “Wotembereredwa ndi munthu wozengereza kugwira ntchito imene Yehova wamupatsa.+ Wotembereredwa ndi munthu wopewa kukhetsa magazi ndi lupanga lake. 11  “Anthu a ku Mowabu akhala mosatekeseka kuyambira pa unyamata wawo+ ndipo akukhalabe mosatekeseka ngati vinyo wansenga.+ Iwo sanatsanulidwepo kuchoka m’chiwiya china kupita m’chiwiya china ndipo sanapitepo ku ukapolo. N’chifukwa chake kukoma kwawo sikunawonjezeke ndipo fungo lawo silinasinthe. 12  “‘Choncho masiku adzafika,’ watero Yehova, ‘ndipo ndidzawatumizira anthu opendeketsa mitsuko ndipo adzawapendeketsa.+ Iwo adzawatsanula m’ziwiya zawo ndipo adzaswa mitsuko yawo ikuluikulu kukhala mapalemapale. 13  Amowabuwo adzachita manyazi ndi Kemosi,+ monga mmene anthu a m’nyumba ya Isiraeli achitira manyazi ndi Beteli, mzinda umene anali kuudalira.+ 14  N’chifukwa chiyani anthu inu mukunena kuti: “Ndife amuna amphamvu+ ndi anyonga oyenera kumenya nkhondo”?’ 15  “‘Mowabu wafunkhidwa, ndipo munthu wina adzaukira mizinda yake.+ Anyamata osankhidwa a m’mizindayo apita kokaphedwa,’+ yatero Mfumu imene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ 16  “Tsoka la Amowabu lili pafupi, ndipo likubwera mofulumira kwambiri.+ 17  Onse owazungulira, onse odziwa dzina lawo adzawamvera chisoni.+ Anthu inu nenani kuti, ‘Ndodo yamphamvu ndiponso yokongola yathyoka!’+ 18  “Tsika pamalo ako aulemerero ndipo ukhale ndi ludzu, iwe mwana wamkazi wokhala+ ku Diboni+ chifukwa wowononga Mowabu wabwera kudzakuukira. Iye adzasandutsa bwinja malo ako a mipanda yolimba kwambiri.+ 19  “Ima chilili ndi kuona zimene zikuchitika m’njira, iwe mkazi wokhala ku Aroweli.+ Funsa mwamuna ndi mkazi amene akuthawa. Uwafunse kuti, ‘Chachitika n’chiyani?’+ 20  Anthu a ku Mowabu achita manyazi pakuti agwidwa ndi mantha aakulu.+ Lirani mofuula. Amuna inu, lengezani ku Arinoni+ kuti Mowabu wafunkhidwa. 21  Chiweruzo chafika padziko lathyathyathya.+ Chafika ku Holoni, Yahazi,+ Mefaata,+ 22  Diboni,+ Nebo,+ Beti-dibilataimu, 23  Kiriyataimu,+ Beti-gamuli, Beti-meoni,+ 24  Kerioti,+ Bozira+ ndi mizinda yonse ya m’dziko la Mowabu, yakutali ndi yapafupi. 25  “‘Nyanga* ya Mowabu yadulidwa+ ndipo dzanja lake lathyoledwa,’+ watero Yehova. 26  ‘Muledzeretseni+ anthu inu chifukwa wadzikuza pamaso pa Yehova.+ Mowabu wadzigwetsa ndipo wagubuduka m’masanzi ake,+ ndipo wakhaladi chinthu chotonzedwa. 27  “‘Kodi Isiraeli sanasanduke chinthu chotonzedwa kwa inu?+ Kapena kodi anapezeka pakati pa mbala zenizeni?+ Inu munali kupukusa mitu moipidwa pamene munali kumunenera zinthu zoipa. 28  “‘Inu anthu okhala ku Mowabu, chokani mumzinda ndi kukakhala pathanthwe.+ Khalani ngati njiwa imene imamanga chisa chake pakhomo la dzenje m’matanthwemo.’”+ 29  “Tamva za kunyada kwa Mowabu.+ Iye ndi wodzikuza kwambiri. Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake, kudzikuza kwake ndi kudzitukumula kwa mtima wake.”+ 30  “‘Ine ndadziwa za mkwiyo wake,’ watero Yehova, ‘ndipo kudzikuza kwakeko sikudzaphula kanthu.+ Iye sadzachita zonena zake zopanda pakezo.+ 31  N’chifukwa chake Mowabu ndidzamukuwira, ndipo ndidzafuulira Mowabu yense.+ Anthu adzalirira amuna a ku Kiri-haresi.+ 32  “‘Iwe mtengo wa mpesa wa ku Sibima+ ndidzakulirira kuposa mmene ndingalirire Yazeri.+ Mphukira zako zosangalala zawoloka nyanja. Zafika kunyanja, ku Yazeri.+ Munthu wofunkha waukira zipatso zako za m’chilimwe*+ ndi mphesa zimene wakolola.+ 33  Kusangalala ndi kukondwera zachotsedwa m’munda wa zipatso ndiponso m’dziko la Mowabu.+ Ndachititsa kuti vinyo asapezeke moponderamo mphesa.+ Palibe amene adzapondaponda mphesa akufuula mosangalala. Padzamveka kufuula koma osati kwachisangalalo.’”+ 34  “‘Kulira kochokera ku Hesiboni+ kudzamveka ku Eleyale+ ndi ku Yahazi.+ Kulira kochokera ku Zowari+ kudzamveka ku Horonaimu+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Madzi a ku Nimurimu+ nawonso adzawonongedwa. 35  Ndidzachititsa kuti m’dziko la Mowabu musapezeke aliyense wobweretsa nsembe kumalo okwezeka komanso wofukiza nsembe yautsi kwa mulungu wake,’+ watero Yehova. 36  ‘Choncho mtima wanga udzachitira Mowabu phokoso ngati zitoliro.+ Mtima wanga udzachitira phokoso amuna a ku Kiri-haresi+ ngati zitoliro. Chotero zinthu zochuluka zimene wapanga zidzawonongeka.+ 37  Mutu uliwonse wametedwa mpala,+ ndipo ndevu zonse n’zometa.+ M’manja monse ndi mochekekachekeka,+ ndipo anthu onse amanga ziguduli m’chiuno mwawo.’”+ 38  “‘Anthu akulira pamadenga onse a nyumba za ku Mowabu ndi m’mabwalo ake onse.+ Akulira chifukwa ndaphwanya Mowabu ngati chiwiya chimene sichikundikondweretsa,’+ watero Yehova. 39  ‘Mowabu wachita mantha. Lirani mofuula anthu inu! Mowabu watembenuka ndipo wachita manyazi.+ Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka ndi chochititsa mantha kwa onse omuzungulira.’” 40  “Yehova wanena kuti, ‘Taonani! Monga mmene chiwombankhanga chimatsikira ndi kugwira chakudya chake,+ wina adzatambasula mapiko ake ndi kugwira Mowabu.+ 41  Matauni adzalandidwa. Malo ake odalirika adzalandidwa. Pa tsikulo, mitima ya amuna amphamvu a ku Mowabu idzakhala ngati mtima wa mkazi amene akumva zowawa za pobereka.’”+ 42  “‘Mowabu adzawonongedwa ndipo sadzakhalanso mtundu wa anthu+ chifukwa wadzikweza pamaso pa Yehova.+ 43  Mantha, dzenje ndi msampha zili pa iwe munthu wokhala ku Mowabu,’+ watero Yehova. 44  ‘Aliyense wothawa chifukwa cha mantha adzagwera m’dzenje. Aliyense wotuluka m’dzenjemo adzagwidwa mumsampha.’+ “‘Pakuti ine ndidzachititsa kuti chaka chopereka chilango kwa anthu a ku Mowabu chifike,’+ watero Yehova. 45  ‘Anthu othawa aima chilili mumthunzi wa Hesiboni ndipo alibe mphamvu. Moto udzachokera ku Hesiboni+ ndipo malawi a moto adzachokera ku Sihoni+ ndi kutentha Mowabu m’mutu, m’mphepete mwa makutu, komanso paliwombo pa ana osokoneza.’+ 46  “‘Tsoka iwe Mowabu!+ Anthu a Kemosi+ awonongedwa. Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina. 47  M’masiku otsiriza ndidzasonkhanitsa Amowabu onse amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,’+ watero Yehova. ‘Apa ndi pamene pathera ziweruzo za Mowabu.’”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.