Yeremiya 50:1-46
50 Yehova ananena mawu okhudza Babulo,+ dziko la Akasidi,+ kudzera mwa mneneri Yeremiya. Iye anati:
2 “Nenani ndi kulengeza zimene zachitika kwa anthu a mitundu ina.+ Imikani mtengo wachizindikiro+ ndipo lengezani zimenezi. Musabise kalikonse amuna inu. Nenani kuti, ‘Babulo walandidwa.+ Beli wachititsidwa manyazi.+ Merodake wachita mantha. Mafano a Babulo achita manyazi.+ Mafano ake onyansawo* achita mantha.’
3 Pakuti mtundu wina wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+ Umenewu ndi mtundu umene wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa, moti m’dzikoli mulibe aliyense wokhalamo.+ Anthu ndiponso ziweto zathawa.+ Zonse zapita.”+
4 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo+ ana a Isiraeli pamodzi ndi ana a Yuda adzabwera,”+ watero Yehova. “Iwo adzayenda akulira+ ndipo adzafunafuna Yehova Mulungu wawo.+
5 Iwo adzafunsira njira yopita ku Ziyoni nkhope zawo zitayang’ana kumeneko.+ Iwo adzanena kuti, ‘Bwerani, tiyeni tidziphatike kwa Yehova mwa kuchita pangano lokhalapo mpaka kalekale limene silidzaiwalika.’+
6 Anthu anga akhala ngati gulu la nkhosa zosakazidwa.+ Abusa awo awayendetsa uku ndi uku.+ Awayendetsa uku ndi uku m’mapiri popanda cholinga.+ Awachotsa paphiri ndi chitunda china kupita paphiri ndi chitunda china. Iwo aiwala malo awo ampumulo.+
7 Anthu anga adyedwa ndi aliyense wowapeza,+ ndipo adani awo anena kuti,+ ‘Sitipalamula mlandu uliwonse, chifukwa iwo achimwira Yehova,+ malo okhalamo chilungamo.+ Achimwira Yehova chiyembekezo cha makolo awo.’”+
8 “Thawani m’Babulo ndipo tulukani m’dziko la Akasidi.+ Mukhale ngati mbuzi zamphongo ndi nkhosa zamphongo zimene zikutsogolera gulu lonse.+
9 Inetu ndikuutsira Babulo mpingo wa mitundu yamphamvu ndi kubweretsa mitunduyo kuchokera kudziko la kumpoto.+ Mitunduyo idzamuukira+ ndi kulanda dziko lake.+ Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a munthu wamphamvu amene amapha ana ndipo mautawo sabwerera osachitapo kanthu.+
10 Dziko la Kasidi lidzatengedwa monga zofunkha.+ Onse ofunkha zinthu zake adzakhutira,”+ watero Yehova.
11 “Anthu inu munali kusangalala,+ ndipo munali kukondwera pamene munali kulanda cholowa changa.+ Munali kudumphadumpha pamsipu ngati ng’ombe yaikazi yosaberekapo+ ndipo munali kulira ngati mahatchi amphongo.+
12 Mayi wa anthu inu wachita manyazi kwambiri.+ Mayi amene anakuberekani wakhumudwa kwambiri.+ Taonani! Iye ndi wosafunika kwenikweni pakati pa mitundu ina, wakhala ngati dera lopanda madzi ndiponso chipululu.+
13 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, m’dzikomo simudzakhalanso anthu+ ndipo dziko lonselo lidzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi Babulo adzayang’ana modabwa ndi kumuimbira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+
14 “Zungulirani Babulo ndi kumuukira kuchokera kumbali zonse,+ inu nonse odziwa kukunga uta.+ Mulaseni+ ndipo musasunge muvi uliwonse, pakuti iye wachimwira Yehova.+
15 Mufuulireni mfuu yankhondo kuchokera kumbali zonse.+ Wagwetsa manja ake+ ndipo zipilala zake zagwa. Mipanda yake yagwetsedwa,+ pakuti Yehova akumubwezera.+ Mubwezereni, ndipo monga mmene iye anachitira, inunso muchitireni zomwezo.+
16 Iphani munthu wofesa mbewu mu Babulo,+ ndiponso amene akugwira chikwakwa nthawi yokolola. Aliyense adzabwerera kwa anthu a mtundu wake, ndipo aliyense adzathawira kudziko lakwawo chifukwa choopa lupanga loopsa.+
17 “Isiraeli ndi nkhosa yosochera.+ Mikango ndi imene yamuchititsa kuthawa.+ Poyamba, mfumu ya Asuri inadya Isiraeli,+ ndipo ulendo uno Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo yakukuta mafupa ake.+
18 Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ine ndikulanga mfumu ya Babulo ndi dziko lake ngati mmene ndinalangira mfumu ya Asuri.+
19 Isiraeli ndidzamubwezeretsa kumalo ake odyerako msipu+ moti adzadya msipu paphiri la Karimeli+ ndi ku Basana.+ Iye adzakhutira m’madera amapiri a Efuraimu+ ndi Giliyadi.’”+
20 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa+ koma sichidzapezeka,” watero Yehova. “Machimo a Yuda+ adzafufuzidwa koma sadzapezeka, pakuti ine ndidzakhululukira anthu amene ndawasiya amoyo.”+
21 “Ukirani dziko la Merataimu. Liukireni+ ndipo muukirenso anthu a ku Pekodi.+ Apululeni ndi kuwawonongeratu. Chitani zonse zimene ndakulamulani,” watero Yehova.+
22 “Mukumveka phokoso lankhondo m’dzikomo ndi kuwonongeka kwakukulu.+
23 Taonani! Nyundo yophwanyira mitundu+ ya anthu padziko lonse lapansi yathyoledwa ndipo yawonongeka.+ Taonani! Babulo wakhala chinthu chodabwitsa pakati pa mitundu ina.+
24 Iwe Babulo ndinakutchera msampha ndipo wakodwa koma iwe sunadziwe.+ Unapezeka ndi kugwidwa chifukwa unali kulimbana ndi Yehova.+
25 “Yehova watsegula nkhokwe yake ya zida ndipo akutulutsamo zida zake zodzudzulira mwamphamvu.+ Akutero chifukwa chakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ ali ndi ntchito yoti achite m’dziko la Akasidi.+
26 Lowani m’dziko lake kuchokera kudera lakutali.+ Tsegulani nkhokwe zake.+ Muunjikeni pamodzi ngati mmene anthu amaunjikira milu ya tirigu+ ndipo mumuwonongeretu.+ M’dzikomo musapezeke aliyense wotsala.+
27 Iphani ng’ombe zake zonse zazing’ono zamphongo.+ Zonse zipite kokaphedwa.+ Tsoka kwa iwo, chifukwa tsiku lawo lafika. Nthawi yoti alangidwe yafika.+
28 “Kukumveka phokoso la anthu amene akuthawa komanso amene apulumuka m’dziko la Babulo+ kuti akanene ku Ziyoni za chilango chimene Yehova Mulungu wathu akubwezera.+ Iye akubwezera kuwonongedwa kwa kachisi wake.+
29 “Babulo muitanireni oponya mivi ndi uta, onse okunga uta.+ Mangani misasa momuzungulira. Pasapezeke wothawa.+ Mubwezereni zimene anachita.+ Muchitireni zonse zimene iye anachita.+ Iye wachita zinthu modzikuza pamaso pa Yehova, pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+
30 Choncho anyamata ake adzaphedwa m’mabwalo a mizinda yake,+ ndipo tsiku limenelo amuna ake onse ankhondo adzaphedwa,”+ watero Yehova.
31 “Taona! Iwe Babulo Wodzikuza,+ ndikukuthira nkhondo,”+ watero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.+ “Pakuti tsiku lako lifika, nthawi imene ndiyenera kukulanga.
32 Pa tsiku limenelo Babulo Wodzikuza ameneyu adzapunthwa ndi kugwa+ ndipo sipadzapezeka wina womudzutsa.+ Mizinda imene iye amalamulira ndidzaiyatsa moto, ndipo motowo udzawononganso madera onse ozungulira mizindayo.”+
33 Yehova wa makamu wanena kuti: “Ana a Isiraeli ndi ana a Yuda, onse akuponderezedwa. Anthu onse amene agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina akuwakakamira+ ndipo sakuwalola kubwerera kwawo.+
34 Wowawombola ndi wamphamvu,+ dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ Iye sadzalephera kuwaweruzira mlandu wawo+ kuti apumitse dziko lawo+ ndiponso kusokoneza mtendere wa anthu okhala m’Babulo.”+
35 “Lupanga lidzawononga Akasidi,”+ watero Yehova, “lidzawononganso anthu okhala m’Babulo,+ akalonga ake+ ndi anthu ake anzeru.+
36 Lupanga lidzawononga anthu olankhula zinthu zopanda pake.+ Anthu amenewo adzachita zinthu mopanda nzeru.+ Lupanga lidzawononga anthu amphamvu a m’Babulo,+ moti adzagwidwa ndi mantha.+
37 Lupanga lidzawononga mahatchi awo,+ magaleta awo ankhondo ndi khamu lonse la anthu a mitundu yosiyanasiyana amene ali pakati pawo+ ndipo adzakhala ngati akazi.+ Lupanga lidzawononga chuma chake+ ndipo chidzafunkhidwa.
38 Madzi ake adzawonongedwa ndipo adzauma.+ Dziko limeneli ndi la zifaniziro zogoba,+ ndipo anthu ake amachita zinthu mosaganiza chifukwa cha masomphenya awo ochititsa mantha.
39 Choncho nyama za m’madera opanda madzi, nyama zokonda kulira mokuwa ndi nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+ Simudzakhalanso munthu mmenemo ndipo mzindawo sudzapezekanso ku mibadwomibadwo.”+
40 “Monga mmene Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora+ pamodzi ndi midzi yake yapafupi,+ dzikolo lidzawonongedwanso moti palibe munthu amene adzakhalanso mmenemo. Mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo,”+ watero Yehova.
41 “Taona! Mtundu wa anthu ukubwera kuchokera kumpoto. Mtundu wamphamvu+ ndi mafumu akuluakulu+ adzautsidwa kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
42 Iwo amadziwa kuponya mivi ndi uta komanso nthungo.+ Amenewo ndi anthu ankhanza ndipo sadzakumvera chifundo.+ Phokoso lawo lili ngati phokoso la nyanja yowinduka.+ Adzakwera pamahatchi+ ndi kukuzungulira mogwirizana n’cholinga choti akuthire nkhondo, iwe mwana wamkazi wa Babulo.+
43 “Mfumu ya Babulo yamva za iwo,+ ndipo yataya mtima ndi kulefuka.+ Ikuda nkhawa ndipo ikumva zowawa ngati mkazi amene akubereka.+
44 “Taona! Wina adzabwera ngati mkango kuchokera m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano.+ Iye adzafika pamalo otetezeka odyetsera nkhosa koma m’kanthawi kochepa ndidzathamangitsa eni malowo.+ Ndidzasankha ndi kuika woyang’anira malowo,+ pakuti ndani angafanane ndi ine,+ ndipo ndani angalimbane ndi ine,+ komanso ndi m’busa uti tsopano amene angatsutsane nane?+
45 Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha+ kuchitira Babulo+ ndiponso zimene waganiza kuti achitire dziko la Akasidi.+ Ndithudi chilombo chidzakokera ana a nkhosa uku ndi uku,+ ndipo chidzawononga malo awo okhala chifukwa cha anthuwo.+
46 Dziko lapansi lidzagwedezeka chifukwa cha phokoso la kugwidwa kwa Babulo,+ ndipo kulira kudzamveka pakati pa mitundu ya anthu.”+
Mawu a M'munsi
^ Mawu amene ali m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”