Yeremiya 16:1-21

16  Ndiyeno Yehova anapitiriza kundiuza kuti:  “Usakwatire ndipo usakhale ndi ana aamuna kapena ana aakazi m’malo ano.+  Ponena za ana aamuna ndi ana aakazi amene adzabadwa m’malo ano, komanso amayi ndi abambo obereka anawo m’dzikoli, Yehova wanena kuti,+  ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ ndipo sadzawalira maliro+ kapena kuikidwa m’manda+ koma adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Iwo adzafa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.’+  “Yehova wanena kuti, ‘Usalowe m’nyumba imene olira maliro akuchitiramo phwando, ndipo usapite kukalira nawo maliro kapena kuwamvera chisoni.’+ “‘Pakuti anthu awa ndawachotsera mtendere wanga, kukoma mtima kosatha ndi chifundo,’+ watero Yehova.  ‘Anthu onse a m’dzikoli, osasiyapo aliyense, adzafa ndithu. Sadzaikidwa m’manda+ ndipo anthu sadzadziguguda pachifuwa chifukwa cha iwo. Palibe aliyense amene adzadzichekacheka+ kapena kumeta mpala chifukwa cha iwo.+  Ofedwa sadzapatsidwa chakudya chowatonthoza+ ndipo sadzapatsidwa zakumwa kuti awatonthoze pamaliro a bambo awo kapena mayi awo.+  Ndipo usadzalowe m’nyumba yaphwando ndi kukhala nawo pansi kuti udye ndi kumwa.’+  “Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘M’masiku anu ndidzathetsa phokoso lachikondwerero, phokoso lachisangalalo, mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi m’malo ano, inu mukuona.’+ 10  “Ndiyeno ukadzauza anthu awa mawu onsewa, ndipo iwo akadzakufunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova wanena kuti adzatigwetsera tsoka lalikulu limeneli? Kodi talakwa chiyani ndipo tamuchimwira chiyani Yehova Mulungu wathu?’+ 11  Pamenepo udzawayankhe kuti, ‘“N’chifukwa chakuti makolo anu anandisiya,”+ watero Yehova, “ndipo anapitirizabe kutsatira milungu ina, kuitumikira ndi kuigwadira.+ Koma ine anandisiya ndipo sanasunge malamulo anga.+ 12  Ndipo inu mwachita zinthu zoipa kwambiri kuposa makolo anu.+ Aliyense wa inu akupitiriza kuumitsa mtima+ wake woipawo ndipo simukundimvera.+ 13  Choncho ndidzakutayani kunja kukuchotsani m’dziko lino+ ndi kukupititsani kudziko limene inu ngakhalenso makolo anu sanalidziwe.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina+ usana ndi usiku chifukwa sindidzakumverani chifundo.”’ 14  “‘Taonani! Masiku adzafika,’+ watero Yehova, ‘pamene sadzalumbiranso kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo!”+ 15  Koma adzalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa ana a Isiraeli m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene anawabalalitsira!” Ineyo ndidzawabwezeretsa kudziko lawo limene ndinapatsa makolo awo.’+ 16  “‘Inetu ndikuitana asodzi ambiri,’ watero Yehova, ‘ndipo adzawawedza. Kenako ndidzaitana anthu ambiri osaka nyama,+ ndipo adzawasaka m’phiri lililonse, pachitunda chilichonse, ndi m’mapanga a m’matanthwe.+ 17  Pakuti maso anga akuona njira zawo zonse. Anthuwo sanabisike kwa ine, ndipo zolakwa zawo sizinabisike pamaso panga.+ 18  Chotero ndisanawabwezeretse, ndidzawabwezera zolakwa zawo zonse+ ndi machimo awo onse chifukwa choipitsa dziko langa.+ Anadzaza cholowa changa ndi mitembo ya zinthu zawo zochititsa mseru ndiponso zinthu zawo zonyansazo.’”+ 19  Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga, malo anga achitetezo ndi malo anga othawirako pa tsiku la tsoka.+ Mitundu ya anthu idzabwera kwa inu kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+ ndipo idzati: “Ndithudi makolo athu analandira mafano* monga cholowa chawo.+ Analandira zinthu zachabechabe ndi zinthu zosapindulitsa.”+ 20  Kodi munthu wochokera kufumbi angapange milungu? Zimene munthu amapangazo si milungu yeniyeni.+ 21  “Choncho ine ndiwaphunzitsa. Pa nthawi ino yokha ndiwaonetsa dzanja langa ndi mphamvu zanga,+ ndipo adziwa kuti dzina langa ndine Yehova.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chinyengo.”