Yeremiya 45:1-5

45  Mneneri Yeremiya analankhula ndi Baruki+ mwana wa Neriya pa nthawi imene Barukiyo anali kulemba mawu a Yeremiya m’buku.+ Chimenechi chinali chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Yeremiyayo anati:  “Ponena za iwe Baruki, Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti,  ‘Iwe wanena kuti: “Tsoka ine!+ pakuti Yehova wawonjezera chisoni pa zopweteka zanga. Ndatopa ndi kuusa moyo* kwanga ndipo malo ampumulo sindikuwapeza.”’+  “Umuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Taona! Zimene ndamanga, ndikuzigwetsa, ndipo zimene ndabzala, ndikuzizula. Ndichita zimenezi m’dziko lonse.+  Koma iwe, ukufunafunabe zinthu zazikulu.+ Leka kuzifunafuna.”’+ “‘Anthu onse ndikuwagwetsera tsoka+ ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako monga chofunkha chako kulikonse kumene ungapite,’ watero Yehova.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.