Yeremiya 19:1-15

19  Yehova wanena kuti: “Pita, ukatenge botolo la mafuta ladothi kwa woumba mbiya+ ndipo ukaitane ena mwa atsogoleri a anthu ndi ena mwa akuluakulu a ansembe.  Ndiyeno ukapite kuchigwa cha mwana wa Hinomu,+ chimene chili pafupi ndi khomo la Chipata cha Mapale.* Kumeneko ukanene mawu onse amene ndikuuze.+  Ukawauze kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova inu mafumu a Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu.+ Yehova wa makamu,+ Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “‘“Ine ndikubweretsa tsoka pamalo ano, ndipo aliyense akadzamva za tsoka limeneli, makutu ake adzalira.+  Zidzatero chifukwa andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Iwo amaperekanso nsembe zautsi kwa milungu ina imene sanali kuidziwa,+ iwowo, makolo awo ndi mafumu a Yuda, ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+  Iwo amangiranso Baala malo okwezeka kuti azitentherapo ana awo aamuna monga nsembe zopsereza zathunthu zoperekedwa kwa Baala.+ Ine sindinawalamule zimenezi kapena kuzitchula,+ ndipo sindinaziganizirepo mumtima mwanga.”’+  “‘Yehova wanena kuti: “Chotero taonani! Masiku akubwera pamene sadzatchulanso malowo kuti Tofeti+ ndiponso chigwa cha mwana wa Hinomu,+ koma adzawatchula kuti chigwa chopherako anthu.  Ndidzasokoneza zolinga za Yuda ndi za Yerusalemu m’malo ano,+ ndipo ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga la adani awo komanso ndi anthu amene akufunafuna moyo wawo.+ Mitembo yawo ndidzaipereka kwa zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire kuti ikhale chakudya chawo.+  Ndidzasandutsa mzindawu kukhala chinthu chodabwitsa kwa ena, chimene azidzachiimbira mluzu.+ Aliyense wodutsa pafupi nawo adzauyang’anitsitsa modabwa ndipo adzaulizira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+  Ndidzawachititsa kudya mnofu wa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. Aliyense adzadya mnzake, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene adani awo ndiponso anthu amene akufuna moyo wawo adzawapanikiza nazo.”’+ 10  “Ukaswe botololo pamaso pa amuna amene akupita nawe. 11  Ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, ndidzaswa anthu awa ndi mzinda uwu ngati mmene munthu amaswera botolo lopangidwa ndi woumba mbiya moti sangathe kulikonzanso.+ Ndipo adzaika maliro ku Tofeti+ mpaka sipadzapezekanso malo oika maliro kumeneko.”’+ 12  “‘Ndi mmene ndidzachitira ndi malo awa ndiponso ndi anthu onse okhala mmenemu. Mzinda uwu ndidzausandutsa kukhala ngati Tofeti,’+ watero Yehova. 13  ‘Nyumba za mu Yerusalemu ndi nyumba za mafumu a Yuda zidzakhala zodetsedwa ngati Tofeti.+ Zimenezi ndi nyumba zonse zimene pamadenga ake anali kufukizirapo nsembe zautsi kwa makamu akumwamba+ ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’”+ 14  Ndiyeno Yeremiya anabwerako ku Tofeti+ kumene Yehova anamutuma kuti akalosere. Kenako anakaima m’bwalo la nyumba ya Yehova ndi kuuza anthu onse kuti:+ 15  “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndikubweretsera mzinda uwu ndi mizinda yake yonse yozungulira masoka onse amene ndinanena, chifukwa anthu ake aumitsa khosi lawo kuti asamvere mawu anga.’”+

Mawu a M'munsi

Chipatachi chiyenera kuti ndi chimene chinali kutchedwa kuti “Chipata cha Milu ya Phulusa.”