Yeremiya 7:1-34
7 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa:
2 “Imirira pachipata cha nyumba ya Yehova, ndi kulengeza kuti,+ ‘Tamverani mawu a Yehova nonsenu okhala mu Yuda, amene mumalowa pazipata izi kuti mukagwadire Yehova.
3 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Konzani njira zanu ndiponso zochita zanu kuti zikhale zabwino, ndipo ndidzachititsa anthu inu kukhalabe m’dziko lino.+
4 Musamakhulupirire mawu achinyengo+ ndi kunena kuti, ‘Nyumba izi ndizo kachisi wa Yehova, inde ndi kachisi wa Yehova, ndithudi ndi kachisi wa Yehova!’
5 Ngati mungakonze njira zanu ndi zochita zanu kuti zikhale zabwino, mukamaweruza molungama pakati pa munthu ndi mnzake,+
6 ngati simudzapondereza mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye,+ komanso ngati simudzakhetsa magazi a munthu wopanda mlandu m’dziko lino,+ ndiponso ngati simudzatsatira milungu ina, zimene zingakubweretsereni tsoka,+
7 inenso ndidzachititsa kuti mukhalebe m’dziko lino, dziko limene ndinapatsa makolo anu, ndipo mudzakhalamo mpaka kalekale.”’”+
8 “Inu mukukhulupirira mawu achinyengo, koma simudzapezapo phindu lililonse.+
9 Kodi mungamabe,+ kupha,+ kuchita chigololo,+ kulumbira monama,+ kufukiza nsembe zautsi kwa Baala+ ndi kutsatira milungu ina imene simunali kuidziwa,+
10 kenako n’kubwera kudzaima pamaso panga m’nyumba iyi, imene yatchedwa ndi dzina langa+ n’kumanena kuti, ‘Ndithudi tidzapulumutsidwa,’ ngakhale mukuchita zinthu zonyansa zonsezi?
11 Kodi nyumba iyi, imene yatchedwa ndi dzina langa,+ mwayamba kuiona ngati phanga la achifwamba?+ Inetu ndaona zimene mukuchita,” watero Yehova.+
12 “‘Pitani ku Silo,+ kumalo kumene poyamba kunali dzina langa,+ ndipo mukaone zimene ndinachitira malowo chifukwa cha kuipa kwa anthu anga Aisiraeli.+
13 Tsopano chifukwa chakuti mwapitiriza kuchita ntchito zimenezi,’ watero Yehova, ‘ndipo ndinali kukulankhulani nthawi zonse, kudzuka m’mamawa ndi kukulankhulani,+ koma inu osamva,+ kukuitanani koma inu osandiyankha,+
14 ndidzachita zofanana ndi zimene ndinachita ku Silo.+ Ndidzachita zimenezi panyumba imene ikutchedwa ndi dzina langa,+ imene inu mukuidalira,+ ndiponso malo amene ndinapatsa inu ndi makolo anu.
15 Ine ndidzakuthamangitsani, kukuchotsani pamaso panga,+ ngati mmene ndinathamangitsira abale anu onse, mbadwa zonse za Efuraimu.’+
16 “Tsopano iwe usawapempherere anthu awa, kapena kuwalirira kwa ine mochonderera. Usawaperekere pemphero, kapena kuwapemphera mochonderera,+ chifukwa ine sindidzakumvetsera.+
17 Kodi sukuona zimene akuchita m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu?+
18 Ana aamuna akutola nkhuni, abambo akuyatsa moto ndipo akazi akukanda ufa kuti apange makeke okapereka nsembe kwa ‘mfumukazi yakumwamba.’+ Ndipo akuthira pansi nsembe zachakumwa+ kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.+
19 ‘Kodi iwo akukhumudwitsa ine?’ watero Yehova.+ ‘Kodi iwo sakudzikhumudwitsa okha kuti achite manyazi pankhope zawo?’+
20 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani! Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zikutsanulidwa pamalo awa,+ pamunthu, pachiweto, pamtengo wakuthengo,+ ndi pachipatso chilichonse chochokera m’nthaka yawo, ndipo udzayaka moti sudzazimitsidwa.’+
21 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Wonjezerani nsembe zanu zopsereza zathunthuzo pansembe zanu zinazo ndipo muzidye nokha.+
22 Chifukwatu makolo anu, pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo, sindinawauze kapena kuwalamula kuti azipereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.+
23 Koma ndinawalamula kuti: “Muzimvera mawu anga,+ ndipo ndidzakhala Mulungu wanu,+ inuyo mudzakhala anthu anga. Muziyenda m’njira+ imene ndidzakulamulani, kuti zinthu zikuyendereni bwino.”’+
24 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu,+ ndipo anapitiriza kuyenda mwa zofuna zawo, mwa kuuma kwa mtima wawo woipawo,+ mwakuti anali kuyenda mobwerera m’mbuyo osati mopita patsogolo,+
25 kuchokera tsiku limene makolo anu anatuluka m’dziko la Iguputo kufikira lero.+ Ndinapitiriza kukutumizirani atumiki anga onse aneneri, tsiku ndi tsiku ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza.+
26 Koma iwo sanandimvere kapena kutchera khutu lawo.+ M’malomwake anapitiriza kuumitsa khosi lawo,+ ndipo anachita zinthu zoipa kuposa makolo awo.+
27 “Ukawauze mawu onsewa,+ ngakhale kuti sadzakumvera. Ukawaitane ngakhale kuti sadzakuyankha.+
28 Ukawauze kuti, ‘Uwu ndiwo mtundu umene anthu ake sanamvere mawu a Yehova Mulungu wawo,+ ndipo sanamvere chilango.*+ Palibe munthu wokhulupirika pakati pawo, ndipo satchulanso n’komwe za kukhulupirika.’+
29 “Meta tsitsi lako lalitalilo ndi kulitaya.+ Ukwere pamapiri opanda mitengo ndi kuimba nyimbo yoimba polira pamenepo,+ pakuti Yehova wakana+ ndi kusiya mbadwo wa anthu amene wawakwiyira.+
30 ‘Pakuti ana a Yuda achita zinthu zoipa m’maso mwanga,’ watero Yehova. ‘Aika zinthu zawo zonyansa m’nyumba yotchedwa ndi dzina langa kuti aiipitse.+
31 Iwo amanga malo okwezeka ku Tofeti,+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ kuti azitentha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuchita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’+
32 “‘Chotero taonani! Masiku akubwera,’ watero Yehova, ‘pamene sadzatchulanso malowo kuti Tofeti ndiponso chigwa cha mwana wa Hinomu, koma adzawatchula kuti chigwa chopherako anthu.+ Iwo adzaika anthu m’manda ku Tofeti mpaka sikudzakhala malo okwanira.+
33 Mitembo ya anthu awa idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi cha zilombo zakutchire, ndipo sipadzakhala woziopsa.+
34 Pamenepo ndidzathetsa phokoso lachikondwerero, phokoso lachisangalalo, mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi+ m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu pakuti dzikoli lidzakhala litawonongedwa.’”+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”