Yeremiya 22:1-30
22 Yehova wanena kuti: “Pita kunyumba ya mfumu ya Yuda, ndipo kumeneko ukanene mawu awa.
2 Ukanene kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova, inu mfumu ya Yuda amene mwakhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mumve mawu amenewa inuyo, atumiki anu komanso anthu anu amene amalowa pazipata izi.+
3 Yehova wanena kuti: “Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo, muzilanditsa munthu amene anthu achinyengo akufuna kumulanda katundu wake. Musachitire nkhanza mlendo aliyense wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye* kapena mkazi wamasiye.+ Musawachitire zachiwawa.+ Musakhetse magazi a munthu aliyense wosalakwa m’dziko lino.+
4 Mukatsatiradi mawu amenewa, pazipata za nyumba iyi padzalowa mafumu okhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mfumu iliyonse idzalowa pamodzi ndi atumiki ake ndi anthu ake atakwera magaleta ndi mahatchi.”’+
5 “‘Koma mukapanda kumvera mawu amenewa, ndikulumbira pali ine mwini+ kuti nyumba iyi idzakhala bwinja,’ watero Yehova.+
6 “Ponena za nyumba ya mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Kwa ine, iwe uli ngati Giliyadi ndiponso ngati nsonga ya phiri la ku Lebanoni.+ Ndithudi ndidzakusandutsa chipululu+ ndipo m’mizinda iyi simudzapezeka aliyense wokhalamo.+
7 Ndidzakuutsira owononga+ ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi zida zake.+ Iwo adzadula mitengo yako yabwino kwambiri ya mkungudza+ ndi kuigwetsera pamoto.+
8 Anthu a mitundu yambiri adzadutsa pafupi ndi mzinda uwu ndipo adzafunsana kuti: “N’chifukwa chiyani Yehova anachitira mzinda waukuluwu zinthu zoterezi?”+
9 Ndipo adzanena kuti: “Anauchitira zimenezi chifukwa chakuti anthu a mumzindawu anasiya pangano la Yehova Mulungu wawo+ ndi kuyamba kulambira milungu ina ndi kuitumikira.”’+
10 “Munthu wakufa musamulire kapena kumumvera chisoni anthu inu.+ Lirani munthu amene watengedwa kupita ku ukapolo chifukwa sadzabwererakonso ndipo sadzaonanso dziko lakwawo.
11 Ponena za Salumu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene akulamulira m’malo mwa bambo ake Yosiya,+ amene anachoka m’dziko lino kupita ku ukapolo, Yehova wanena kuti, ‘Sadzabwereranso kwawo,
12 chifukwa akafera kudziko laukapolo kumene amutengera ndipo dziko lino sadzalionanso.’+
13 “Tsoka amene akumanga nyumba yake+ komanso zipinda zake zam’mwamba mopanda chilungamo mwa kugwiritsa ntchito anthu kwaulere, osawapatsa malipiro.+
14 Iye akunena kuti, ‘Ndimanga nyumba yaikulu ndi zipinda zikuluzikulu zam’mwamba.+ Ndikulitsa mawindo ake ndipo ndiyala matabwa a mkungudza+ ndi kupaka utoto wofiira.’+
15 Kodi upitiriza kulamulira chifukwa chakuti matabwa a mkungudzawa akukuchititsa kukhala wapamwamba kuposa ena? Kodi bambo ako sanali kudya, kumwa ndi kuchita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo?+ Chifukwa chochita zimenezi zinthu zinawayendera bwino.+
16 Anali kunenera mlandu anthu osautsika ndi osauka.+ Chifukwa chochita zimenezi zinthu zinayenda bwino. ‘Kodi sanachite zimenezi chifukwa chakuti anali kundidziwa?’ watero Yehova.
17 ‘Ndithudi, maso ako ndi mtima wako sizikulakalaka china chilichonse koma phindu lachinyengo,+ anthu osalakwa kuti ukhetse magazi awo+ komanso kuba mwachinyengo ndi kulanda.’
18 “Choncho ponena za Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Sadzamulira monga mmene anthu amachitira kuti: “Kalanga ine m’bale wanga! Kalanga ine mlongo wanga!” Sadzamulira kuti: “Kalanga ine mbuye wanga! Kalanga ine, onani mmene ulemerero wake wathera!”+
19 Adzaikidwa m’manda ngati mmene amaikira bulu wamphongo.+ Adzamukoka kudutsa naye pazipata za Yerusalemu ndi kukamutaya kunja.’+
20 “Pita ku Lebanoni+ kuti ukalire kumeneko, ndipo ukafuule ku Basana.+ Ukalirenso ku Abarimu+ chifukwa amene anali kukukonda kwambiri agonjetsedwa.+
21 Ndinalankhula nawe pamene unali pa ufulu,+ koma iwe unandiyankha kuti, ‘Sindidzamvera.’+ Wakhala ukuchita zimenezi kuyambira uli wachinyamata, moti sunamvere mawu anga.+
22 Mphepo idzaweta abusa ako onse+ ndipo anthu onse amene akukukonda kwambiri adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ Pa nthawi imeneyo udzachita manyazi ndipo udzanyazitsidwadi chifukwa cha tsoka limene lidzakugwere.+
23 Inu okhala mu Lebanoni,+ amene mukuwetedwa m’nyumba zamitengo ya mkungudza,+ mudzausadi moyo zowawa za pobereka zikadzakugwerani,+ mukadzamva ululu ngati wa mkazi amene akubereka.”+
24 “‘Pali ine, Mulungu wamoyo,’ watero Yehova, ‘ngakhale iwe Koniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, utakhala mphete yodindira+ kudzanja langa lamanja, ndidzakuvula!+
25 Ndipo ndidzakupereka m’manja mwa anthu ofunafuna moyo wako,+ m’manja mwa amene umawaopa, m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ndiponso m’manja mwa Akasidi.+
26 Iwe ndi mayi ako+ amene anakubereka, ndidzakuponyani kudziko lina limene anthu inu simunabadwireko ndipo mudzafera kumeneko.+
27 Ndidzakuponyani kudziko limene mitima yanu idzalakalaka kubwererako, koma simudzabwererako.+
28 Kodi munthu uyu Koniya+ wangokhala chiwiya chonyozeka, chophwanyika+ komanso chosasangalatsa?+ N’chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuyenera kugwetsedwa ndi kuponyedwa kudziko limene sakulidziwa?’+
29 “Iwe dziko lapansi, dziko lapansi, dziko lapansi, tamvera mawu a Yehova.+
30 Yehova wanena kuti, ‘Lembani kuti munthu uyu alibe ana,+ munthu wamphamvu amene zinthu sizidzamuyendera bwino m’masiku a moyo wake. Pakuti mwa ana ake onse, palibe ndi mmodzi yemwe amene zinthu zidzamuyendera bwino.+ Palibe ngakhale mmodzi amene adzakhala pampando wachifumu wa Davide+ ndi kulamulira mu Yuda.’”
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”