Yeremiya 46:1-28
46 Yehova anauza mneneri Yeremiya uthenga wokhudza mitundu ya anthu.+
2 Uthenga umenewu unali wopita ku Iguputo+ ndipo unali kukhudza gulu lankhondo la Farao Neko, mfumu ya Iguputo,+ amene anali kumtsinje wa Firate ku Karikemisi.+ Nebukadirezara mfumu ya Babulo anagonjetsa mfumu imeneyi m’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Uthengawo unali wakuti:
3 “Amuna inu, tengani zishango zanu zazikulu ndi zazing’ono ndipo konzekerani kumenya nkhondo.+
4 Inu asilikali okwera pamahatchi, mangani mahatchi anu ndi kukwerapo, ndipo muvale zisoti zanu ndi kukhala okonzeka. Pukutani mikondo yanu ing’onoing’ono. Valani zovala zanu zamamba achitsulo.+
5 “‘N’chifukwa chiyani akuoneka kuti agwidwa ndi mantha? Akubwerera, ndipo amuna awo amphamvu aphwanyika ndi kukhala zidutswazidutswa. Iwo athawadi ndipo sanacheuke.+ Zochititsa mantha zili paliponse,’+ watero Yehova.
6 ‘Munthu waliwiro ndi munthu wamphamvu asayese dala kuthawa.+ Iwo apunthwa ndi kugwa.+ Zimenezi zachitikira kumpoto+ m’mphepete mwa mtsinje wa Firate.’
7 “Ndani uyu amene akubwera ngati mtsinje wa Nailo, kapena ngati mitsinje ya madzi ambiri amene akuwinduka?+
8 Dziko la Iguputo likubwera ngati mtsinje wa Nailo,+ ndipo likubwera ngati madzi owinduka a m’mitsinje.+ Dzikolo likunena kuti, ‘Ndipita ndipo ndiphimba dziko lapansi. Ndiwononga mzinda ndi onse okhala mumzindawo.’+
9 Inu mahatchi pitani. Inu magaleta thamangani ndi liwiro lalikulu! Lolani amuna amphamvu kuti apite. Lolani Kusi+ ndi Puti+ amene amadziwa kugwiritsira ntchito chishango kuti apite. Lolaninso Aludi+ amene amadziwa kukunga ndi kuponya uta kuti apite.
10 “Limeneli ndi tsiku la Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa ndipo ndi tsiku lobwezera chilango kwa adani ake.+ Lupanga lidzadya adaniwo ndi kukhuta ndipo lidzamwa magazi awo kufikira litathetsa ludzu lake. Lidzatero pakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ ali ndi nsembe imene akufuna kupereka+ m’dziko la kumpoto, m’mphepete mwa mtsinje wa Firate.+
11 “Iwe namwali, mwana wamkazi wa Iguputo,+ pita ku Giliyadi kuti ukatenge mafuta a basamu.+ Wachulukitsa njira zochiritsira zosathandiza koma sudzachiritsidwa.+
12 Mitundu ya anthu yamva zochititsa manyazi zimene zakuchitikira+ ndipo kulira kwako kwamveka m’dziko lonse.+ Amuna amphamvu apunthwitsana ndi kugwetsana.+ Onse agwera limodzi.”
13 Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza kubwera kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo kudzaukira dziko la Iguputo.+ Iye anati:
14 “Nenani zimenezi mu Iguputo amuna inu. Lengezani zimenezi ku Migidoli,+ ku Nofi+ ndi ku Tahapanesi.+ Nenani kuti, ‘Imani chilili. Konzekani.+ Pakuti lupanga lidzawononga chilichonse chokuzungulirani.+
15 N’chifukwa chiyani anthu anu amphamvu akokoloka?+ Iwo sanachirimike pakuti Yehova wawathamangitsa.+
16 Ambiri mwa iwo akupunthwa ndi kugwa. Ndipo akuuzana kuti: “Imirira, tiye tibwerere kwa anthu a mtundu wathu ndi kudziko la abale athu chifukwa takumana ndi lupanga loopsa.”’
17 Kumeneko asilikali anu akunena kuti, ‘Farao mfumu ya Iguputo akungoopseza ndi pakamwa chabe.+ Iye wathetsa nthawi ya chikondwerero.’+
18 “‘Pali ine Mulungu wamoyo, Nebukadirezara adzabwera ndi kuonekera ngati phiri la Tabori+ pakati pa mapiri ena, ndiponso ngati phiri la Karimeli+ m’mphepete mwa nyanja,’ yatero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+
19 ‘Longedza katundu wopita naye ku ukapolo,+ iwe mwana wamkazi wokhala+ mu Iguputo. Pakuti mzinda wa Nofi+ udzakhala chinthu chodabwitsa ndipo adzautentha, moti simudzapezeka aliyense wokhalamo.+
20 Iguputo ndi ng’ombe yaikazi yokongola kwambiri imene sinaberekepo. Udzudzu wovutitsa ndi wowononga wochokera kumpoto udzabwera kuti umuwononge.+
21 Kuwonjezera apo, asilikali amene wawalemba ganyu ali ngati ana a ng’ombe onenepa,+ koma iwonso agonja+ ndipo onse athawa. Sanathe kulimba+ pakuti tsiku lawo la tsoka ndiponso nthawi ya kulangidwa kwawo yafika.’+
22 “‘Mawu ake ali ngati mawu a njoka imene ikuthawa.+ Pakuti adani adzafika mwamphamvu ndipo adzabwera kwa iye ali ndi nkhwangwa ngati anthu otola nkhuni.*
23 Adaniwo ndi ochuluka kwambiri kuposa dzombe+ ndipo ndi osawerengeka, moti adzadula nkhalango+ yake chifukwa sangathe kudutsamo,’ watero Yehova.
24 ‘Mwana wamkazi+ wa Iguputo adzachitadi manyazi, ndipo adzaperekedwa m’manja mwa anthu a kumpoto.’+
25 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndilanga Amoni+ wa ku No,+ Farao, Iguputo pamodzi ndi milungu yake+ ndi mafumu ake.+ Ndilanga Farao ndi onse amene amamukhulupirira.’+
26 “‘Ndidzapereka anthu a ku Iguputo m’manja mwa anthu amene akufuna moyo wawo, m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ ndi m’manja mwa atumiki ake. Kenako anthu adzakhalanso m’dzikolo monga mmene zinalili kale,’+ watero Yehova.
27 “‘Koma iwe Yakobo mtumiki wanga, usaope ndipo usagwidwe ndi mantha, iwe Isiraeli.+ Pakuti ine tsopano ndikukupulumutsa kuchokera kutali. Mbewu yako ndikuipulumutsa kuchokera m’dziko limene iwo anali akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndi kukhala mwabata ndiponso mosatekeseka, popanda womuopsa.+
28 Chotero, iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, pakuti ine ndili ndi iwe.+ Ine ndidzafafaniza mitundu yonse ya anthu kumene ndakubalalitsirako,+ koma iwe sindidzakufafaniza.+ Ngakhale zili choncho, ndidzakulanga pamlingo woyenera,+ ndipo ndithu sindidzakusiya osakulanga,’+ watero Yehova.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “odula nkhuni.”