Yeremiya 29:1-32

29  Awa ndi mawu a m’kalata imene mneneri Yeremiya anatumiza kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu otsala pakati pa anthu amene anali ku ukapolo, kwa ansembe ndi kwa aneneri. Kalatayi inapitanso kwa anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu.+  Pamene analemba kalata imeneyi, mfumu Yekoniya,+ mayi a mfumu,+ nduna za panyumba ya mfumu, akalonga a Yuda ndi Yerusalemu,+ amisiri ndi omanga makoma achitetezo+ anali atatengedwa kupita ku ukapolo kuchokera ku Yerusalemu.  Yeremiya anatumiza kalata imeneyi kudzera mwa Elasa mwana wa Safani+ ndi Gemariya mwana wa Hilikiya amene Zedekiya+ mfumu ya Yuda anawatuma ku Babulo kwa Nebukadinezara mfumu ya Babulo. Kalatayo inali ndi mawu akuti:  “Kwa anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo, amene Mulungu anawapititsa ku ukapolo ku Babulo+ kuchokera ku Yerusalemu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, akuti,  ‘Mangani nyumba ndi kukhalamo. Limani minda ndi kudya zipatso zake.+  Tengani akazi ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi.+ Ana anu aamuna muwapezere akazi ndipo ana anu aakazi muwakwatitse kwa amuna kuti nawonso abereke ana aamuna ndi ana aakazi. Muchulukane, musakhale ochepa ayi.  Komanso mzinda umene ndakuchititsani kukhalamo monga akapolo, muziufunira mtendere. Muziupempherera kwa Yehova, pakuti mzindawo ukakhala pa mtendere inunso mudzakhala pa mtendere.+  Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Aneneri anu komanso anthu ochita zamaula amene ali pakati panu asakunyengeni+ ndipo musamvere anthu amene akufotokoza maloto awo amene alota.+  Pakuti ‘zimene akukuuzanizo akulosera m’dzina langa monama. Ine sindinawatume,’+ watero Yehova.”’” 10  “Yehova wanena kuti, ‘Zaka 70 zikadzakwanira muli ku Babulo ndidzakucheukirani anthu inu,+ ndipo ndidzakwaniritsa lonjezo langa lokubwezeretsani kumalo ano.’+ 11  “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira+ zokupatsani mtendere osati masoka,+ kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’+ watero Yehova. 12  ‘Mudzaitanira pa ine komanso mudzabwera ndi kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.’+ 13  “‘Inu mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza+ chifukwa mudzandifunafuna ndi mtima wanu wonse.+ 14  Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ watero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kumayiko ena ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera m’mitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndakubalalitsirani,’+ watero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani ndi kukupititsani ku ukapolo.’+ 15  “Koma inu mwanena kuti, ‘Yehova watiutsira aneneri ku Babulo.’ 16  “Kwa mfumu imene ikukhala pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso anthu onse okhala mumzinda uwu, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo,+ Yehova akuti, 17  ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ine ndikutumizira anthu amene anatsala ku Yuda lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri+ ndipo ndidzawachititsa kukhala ngati nkhuyu zophulika zimene munthu sangazidye chifukwa cha kuipa kwake.”’+ 18  “‘Ndidzawathamangitsa ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri, ndipo ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho.+ Ndidzawachititsa kukhala chinthu chotembereredwa, chodabwitsa, chochilizira mluzu ndiponso chotonzedwa pakati pa mitundu yonse ya anthu a kumene ndidzawabalalitsirako.+ 19  Ndidzawachitira zimenezi chifukwa chakuti sanamvere mawu anga amene ndinali kuwatumizira kudzera mwa atumiki anga aneneri. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kutumiza atumiki angawo,’+ watero Yehova. “‘Inunso simunandimvere,’+ watero Yehova. 20  “Choncho nonsenu amene muli ku ukapolo,+ amene ndinakuchotsani ku Yerusalemu ndi kukutumizani ku Babulo, imvani mawu awa a Yehova.+ 21  Ponena za Ahabu mwana wa Kolaya ndi Zedekiya mwana wa Maaseya amene akulosera m’dzina langa monama pakati panu,+ Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu amenewa ndikuwapereka m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo, ndipo adzawapha inu mukuona.+ 22  Anthu onse a ku Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo, potemberera ena azidzatchula za Zedekiya ndi Ahabu kuti: “Yehova akuchititse kukhala ngati Zedekiya ndi Ahabu+ amene mfumu ya Babulo inawawotcha pamoto!”+ 23  Zimenezi zidzawachitikira chifukwa chakuti akhala akuchita zinthu zopanda nzeru mu Isiraeli,+ ndipo akupitiriza kuchita chigololo ndi akazi a anzawo.+ Komanso akupitiriza kulankhula zonama m’dzina langa. Iwo akulankhula mawu amene sindinawalamule kuti akanene.+ “‘“Ine ndikuzidziwa zimenezi ndipo ndine mboni yake,”+ watero Yehova.’” 24  “Ndiyeno Semaya+ wa ku Nehelamu umuuze kuti, 25  ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Iwe watumiza makalata m’dzina lako+ kwa anthu onse amene ali ku Yerusalemu, kwa Zefaniya+ mwana wa Maaseya, wansembe, ndi kwa ansembe onse. Makalatawo ndi onena kuti, 26  ‘Yehova wakuika kukhala wansembe m’malo mwa Yehoyada wansembe kuti ukhale woyang’anira wamkulu m’nyumba ya Yehova+ ndi kuti umange munthu aliyense wamisala+ amene akuchita zinthu ngati mneneri. Munthu woteroyo umuike m’matangadza, miyendo, manja ndi mutu womwe.+ 27  Nanga n’chifukwa chiyani sunadzudzule Yeremiya wa ku Anatoti,+ amene akuchita zinthu ngati mneneri pakati panu?+ 28  N’chifukwa chake iye watitumizira kalata ku Babulo kuno yonena kuti: “Mukhala akapolo kumeneko kwa nthawi yaitali. Mangani nyumba ndi kukhalamo. Limani minda ndi kudya zipatso zake,+ . . .”’”’” 29  Pamenepo Zefaniya+ wansembe anawerengera mneneri Yeremiya kalata imeneyi. 30  Ndiyeno Yehova anauza Yeremiya kuti: 31  “Anthu onse amene ali ku ukapolo uwatumizire uthenga+ wakuti, ‘Ponena za Semaya wa ku Nehelamu, Yehova wanena kuti: “Pakuti Semaya walosera kwa anthu inu, ngakhale kuti ine sindinamutume, ndipo wayesa kukuchititsani kukhulupirira zinthu zonama,+ 32  Yehova wanena kuti, ‘Ine ndilanga Semaya+ wa ku Nehelamu ndi ana ake.’+ “‘“‘Sipadzapezeka mwamuna wochokera m’banja lake pakati pa anthu awa.+ Ndipo sadzaona zabwino zimene ndichitire anthu anga,+ chifukwa zimene walankhulazo ndi kupandukira Yehova kwenikweni,’+ watero Yehova.”’”

Mawu a M'munsi