Yeremiya 32:1-44

32  Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya m’chaka cha 10 cha ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda.+ Chimenechi chinali chaka cha 18 cha Nebukadirezara.+  Pa nthawi imeneyo, magulu ankhondo a mfumu ya Babulo anali atazungulira Yerusalemu.+ Ndipo mneneri Yeremiya anali atamutsekera m’nyumba imene inali m’Bwalo la Alonda.+ Bwalo limeneli linali pafupi ndi nyumba ya mfumu ya Yuda.  Anam’tsekera kumeneko chifukwa Zedekiya mfumu ya Yuda sanafune kuti Yeremiya azinenera,+ moti anamuuza kuti: “N’chifukwa chiyani ukulosera+ kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ine ndikupereka mzinda uwu m’manja mwa mfumu ya Babulo moti iulanda,+  ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m’manja mwa Akasidi, pakuti adzaperekedwa ndithu m’manja mwa mfumu ya Babulo moti adzalankhulana ndi kuonana maso ndi maso ndi mfumuyo?”’+  Ukuloseranso kuti, ‘Mfumu ya Babulo idzatenga Zedekiya kupita naye ku Babulo ndipo adzakhala komweko kufikira nditamucheukira,’+ watero Yehova. Ukunenanso kuti, ‘ngakhale kuti anthu inu mukupitiriza kumenyana ndi Akasidi simudzapambana.’ N’chifukwa chiyani ukulosera zimenezi?”+  Ndiyeno Yeremiya anati: “Yehova wandiuza kuti,  ‘Kukubwera Hanameli mwana wa Salumu m’bale wa bambo ako, kudzakuuza kuti: “Ugule munda wanga wa ku Anatoti+ chifukwa iweyo ndi amene uli ndi ufulu wogula mundawo.”’”+  Ndiyeno Hanameli mwana wa m’bale wa bambo anga analowa m’Bwalo la Alonda+ ndipo anandipeza mogwirizana ndi mawu a Yehova. Pamenepo iye anati: “Gula munda wanga wa ku Anatoti,+ m’dziko la Benjamini,+ pakuti iweyo ndi amene uli ndi ufulu woulandira monga cholowa ndiponso uli ndi ufulu wougula. Uugule ndithu.” Atatero ndinadziwa kuti mawu amenewa anali a Yehova.+  Zitatero ndinagula munda wa Hanameli+ mwana wa m’bale wa bambo anga. Mundawu unali ku Anatoti.+ Ndinamuyezera ndalama zake+ ndipo zinakwana masekeli* 7 ndi ndalama 10 zasiliva. 10  Ndinalemba chikalata cha pangano+ ndi kuikapo chidindo,+ ndipo ndinaitana mboni+ kuti zidzasaine chikalatacho. Kenako ndinamuyezera+ ndalamazo pasikelo. 11  Ndiyeno mogwirizana ndi malamulo ndi malangizo, ndinatenga chikalata cha pangano chomata ndi chosamata.+ 12  Kenako ndinapereka chikalata cha pangano chogulira mundawo kwa Baruki+ mwana wa Neriya+ mwana wa Maseya. Ndinamupatsa chikalata chimenechi pamaso pa Hanameli mwana wa m’bale wa bambo anga, pamaso pa mboni zimene zinasaina chikalatacho+ ndi pamaso pa Ayuda onse amene anali m’Bwalo la Alonda.+ 13  Ndiyeno ndinalamula Baruki anthu onse akumva, kuti: 14  “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Tenga zikalata zimenezi, chikalata cha pangano chomata chogulira munda, ndi chikalata chosamatacho.+ Zimenezi uziike m’mbiya kuti zikhale kwa nthawi yaitali.’ 15  Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘M’dziko lino anthu adzagula nyumba, minda ndi minda ya mpesa.’”+ 16  Nditapereka chikalata chimenechi kwa Baruki+ mwana wa Neriya,+ ndinapemphera+ kwa Yehova kuti: 17  “Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+ Inuyo ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu yanu+ ndi dzanja lanu lotambasula.+ Nkhaniyi si yovuta kwa inu.+ 18  Inu mumasonyeza anthu masauzande ambiri kukoma mtima kosatha.+ Mumabwezera zolakwa za abambo kwa ana awo.*+ Inu ndinu Mulungu woona, wamkulu+ ndi wamphamvu,+ ndipo dzina lanu+ ndinu Yehova wa makamu.+ 19  Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+ 20  Inu munachita zizindikiro ndi zozizwitsa m’dziko la Iguputo. Zimene munachitazo zikudziwikabe mpaka pano mu Isiraeli ndiponso pakati pa anthu onse.+ Munachita zimenezo kuti mudzipangire dzina mofanana ndi zimene mukufuna kuchita posachedwapa.+ 21  Inu munatulutsa anthu anu Aisiraeli m’dziko la Iguputo+ pogwiritsa ntchito zizindikiro, zozizwitsa,+ dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi zinthu zochititsa mantha kwambiri.+ 22  “Patapita nthawi munawapatsa dziko lino, limene munalumbirira makolo awo kuti mudzawapatsa,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 23  Iwo analowa m’dzikoli ndi kulitenga kukhala lawo,+ koma sanamvere mawu anu ndi kuyenda motsatira malamulo anu.+ Zinthu zonse zimene munawalamula kuti achite sanachite,+ chotero mwawagwetsera masoka onsewa.+ 24  Taonani! Anthu abwera kumzinda uno ndipo amanga ziunda zomenyerapo nkhondo+ kuti aulande,+ moti uperekedwa m’manja mwa Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu.+ Anthu adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri.+ Zimene munanena zachitika ndipo ndi izi mukuzionazi.+ 25  Koma inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, mwandiuza kuti, ‘Gula mundawu ndi ndalama+ pamaso pa mboni,’+ ngakhale kuti mzindawu uperekedwa m’manja mwa Akasidi.”+ 26  Pamenepo Yehova anauza Yeremiya kuti: 27  “Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse.+ Kodi kwa ine pali nkhani ina iliyonse yovuta?+ 28  Choncho Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikupereka mzinda uwu m’manja mwa Akasidi ndi m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo, ndipo aulanda.+ 29  Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu abwera kudzayatsa moto mzindawu kuti upseretu.+ Ayatsanso nyumba zawo chifukwa pamadenga ake amafukizirapo nsembe zautsi kwa Baala ndipo amathira nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.’+ 30  “‘Ana a Isiraeli ndi ana a Yuda akhala akuchita zoipa pamaso panga kuyambira pa ubwana wawo.+ Ana a Isiraeli akundikhumudwitsa ndi ntchito za manja awo,’+ watero Yehova. 31  ‘Mzinda uwu wakhala chinthu chondikwiyitsa+ ndi chondipsetsa mtima kuyambira pamene unamangidwa kufikira lero. Choncho ndiuchotsa pamaso panga,+ 32  chifukwa cha zoipa zonse zimene ana a Isiraeli+ ndi ana a Yuda+ achita ndi kundikhumudwitsa nazo.+ Achita zimenezi pamodzi ndi mafumu awo,+ akalonga awo,+ ansembe awo,+ aneneri awo,+ amuna a mu Yuda ndi anthu onse okhala mu Yerusalemu. 33  Iwo anali kundifulatira, sanandiyang’ane.+ Ngakhale kuti ndinali kuwaphunzitsa, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwaphunzitsa, palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anamvetsera kuti alandire mwambo.*+ 34  Iwo anaika zinthu zawo zonyansa m’nyumba imene imatchedwa ndi dzina langa kuti aiipitse.+ 35  Kuwonjezera apo anamangira Baala+ malo okwezeka m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Anachita izi kuti azidutsitsa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto monga nsembe+ kwa Moleki.+ Ine sindinawalamule zimenezi+ ndipo sindinaganizirepo mumtima mwanga kuchita chinthu chonyansa chimenechi,+ kuti Yuda achite tchimo.’+ 36  “Tsopano ponena za mzinda uwu umene anthu inu mukunena kuti uperekedwa ndithu m’manja mwa mfumu ya Babulo kuti uwonongedwe ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri,+ Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, 37  ‘Inetu ndikuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko onse kumene ndinawabalalitsira nditakwiya, kupsa mtima ndiponso ndili ndi ukali waukulu.+ Ndidzawabwezeretsa m’dziko lino ndi kuwachititsa kukhala mwamtendere.+ 38  Iwo adzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+ 39  Ndidzawapatsa mtima umodzi+ ndi kuwachititsa kuyenda m’njira imodzi kuti azindiopa nthawi zonse. Ndidzatero kuti iwo pamodzi ndi ana awo zinthu ziwayendere bwino.+ 40  Ndidzachita nawo pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale+ lakuti sindidzasiya kuwachitira zabwino+ ndipo ndidzawapatsa mtima woti azindiopa kuti asachoke kwa ine.+ 41  Ndidzakondwera nawo ndi kuwachitira zabwino.+ Ndidzawabzala m’dziko lino+ mokhulupirika ndi mtima wanga wonse komanso ndi moyo wanga wonse.’” 42  “Yehova wanena kuti, ‘Monga mmene ndabweretsera anthu awa masoka aakulu onsewa, momwemonso ndidzawabweretsera zabwino zonsezi zimene ndikunena kuti ndidzawabweretsera.+ 43  Anthu adzagula minda m’dziko lino,+ dziko limene anthu inu mudzanena kuti: “Dziko ili ndi bwinja,+ lopanda munthu wokhalamo kapena nyama yoweta. Linaperekedwa m’manja mwa Akasidi.”’+ 44  “‘Anthu adzagula minda ndi ndalama ndipo padzakhala kulemberana zikalata za pangano+ pamaso pa mboni ndi kumata zikalatazo.+ Zimenezi zidzachitika m’dziko la Benjamini,+ m’madera ozungulira Yerusalemu,+ m’mizinda ya Yuda,+ m’mizinda ya m’madera amapiri, m’mizinda ya m’chigwa+ ndi m’mizinda ya kum’mwera.+ Zidzakhala choncho chifukwa chakuti ndidzabwezeretsa anthu ake amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,’+ watero Yehova.”

Mawu a M'munsi

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Mawu ake enieni, “pachifuwa cha ana awo.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.