Yeremiya 3:1-25
3 Pali mawu akuti: “Mwamuna akathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo n’kuchokadi ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, sangabwererenso kwa mwamuna woyamba uja.”+
Kodi dzikoli silinaipitsidwe kale?+
Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+ Kodi m’poyenera kuti ubwererenso kwa ine?+
2 Kweza maso ako ndi kuona njira zodutsidwadutsidwa.+ Ndi pamalo ati pamene amuna sanakugonerepo?+ Unali kukhala m’mbali mwa njira kudikirira okondedwa ako, ngati mmene Mluya amakhalira m’chipululu.+ Ukuipitsa dzikoli ndi zochita zako zauhule komanso kuipa kwako.+
3 Choncho mvula yamvumbi yasiya kugwa,+ ndipo mvula yomalizira siinagwe.+ Ukuchita zinthu mopanda manyazi ngati mkazi amene akuchita uhule.* Palibe chimene chikukuchititsa manyazi.+
4 Tsopano wayamba kundiitana kuti, ‘Atate wanga,+ ndinu bwenzi langa lapamtima kuyambira pa unyamata wanga.+
5 Kodi mukhala wokwiya mpaka kalekale?* Kapena kodi muzingoyang’anira machimo athu mpaka muyaya?’+ Taona! Iwe wanena ndi kuchita zinthu zoipa ndipo wapambana.”+
6 Yehova anapitiriza kulankhula nane m’masiku a Mfumu Yosiya kuti:+ “‘Kodi waona zimene Isiraeli wosakhulupirikayu akuchita?+ Akupita kuphiri lililonse lalitali+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira+ kuti akachite uhule kumeneko.+
7 Pambuyo poti wachita zinthu zonsezi, ine ndinamupempha mobwerezabwereza kuti abwerere kwa ine, koma iye sanabwerere.+ Ndipo Yuda anali kungoyang’anitsitsa zimene m’bale wake wachinyengoyo anali kuchita.+
8 Nditaona zimenezo, ndinam’pitikitsa+ ndipo ndinamupatsa kalata yotsimikizira kuti ukwati watha+ chifukwa chakuti Isiraeli wosakhulupirikayu anachita chigololo. Koma Yuda amene ndi m’bale wake wochita zachinyengo sanachite mantha ndipo nayenso anayamba kuchita uhule.+
9 Iye anayamba kuchita uhule chifukwa choona nkhani imeneyi mopepuka. Anali kuipitsa dzikolo+ ndi kuchita chigololo ndi miyala komanso mitengo.+
10 Ngakhale kuti m’bale wake Yuda amene anali wochita zachinyengoyo anaona zonsezi, iye sanabwerere kwa ine ndi mtima wake wonse+ koma anangobwerera mwachiphamaso,’+ watero Yehova.”
11 Yehova anapitiriza kundiuza kuti: “Isiraeli wosakhulupirikayo wakhala wolungama kuposa Yuda wochita zachinyengoyo.+
12 Pita, ndipo ukalengeze mawu awa kumpoto+ kuti:
“‘Yehova wanena kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyang’anani mokwiya anthu inu+ pakuti ndine wokhulupirika,”+ watero Yehova.+ “Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale.+
13 Koma ganizirani zolakwa zanu chifukwa mwaphwanya malamulo a Yehova Mulungu wanu.+ Anthu inu simunamvere mawu anga, koma munapitiriza kupanga njira zambirimbiri zopita kwa anthu achilendo+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira,”+ watero Yehova.’”
14 “Bwererani inu ana opanduka,”+ watero Yehova. “Ine ndakhala mwamuna wanu anthu inu.+ Ine ndidzakutengani, mmodzi kuchokera mumzinda uliwonse, awiri kuchokera mu fuko lililonse ndipo ndidzakupititsani ku Ziyoni.+
15 Ndidzakupatsani abusa amene mtima wanga wakonda+ ndipo iwo adzakuthandizani kudziwa zinthu zambiri ndiponso kumvetsa bwino zinthu.+
16 Pamenepo mudzabalana ndi kuchuluka m’dzikoli masiku amenewo,” watero Yehova.+ “Iwo sadzafuulanso kuti, ‘Likasa la pangano la Yehova!’+ Sadzaliganiziranso m’mitima yawo, kulikumbukira,+ kapena kulilakalaka ndipo sadzapanganso likasa lina.
17 Pa nthawiyo mzinda wa Yerusalemu adzautcha kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsira+ ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso mitima yawo yoipayo.”+
18 “M’masiku amenewo nyumba ya Yuda idzayenda pamodzi ndi nyumba ya Isiraeli,+ ndipo onse+ adzatuluka m’dziko la kumpoto ndi kulowa m’dziko limene ndinapereka kwa makolo anu monga cholowa chawo.+
19 Ine ndanena kuti, ‘Mokondwera ndinakuikani pakati pa ana anga ndi kukupatsani dziko labwino,+ cholowa chimene mitundu yambiri ya anthu imachisirira!’ Ndipo ndinanenanso kuti, ‘Anthu inu mudzandiitana kuti, “Atate wanga!”+ ndipo mudzandilondola osabwerera.’
20 ‘Ndithudi, monga mmene mkazi amasiyira mwamuna wake+ mwachinyengo, inunso a m’nyumba ya Isiraeli mwandichitira zachinyengo,’+ watero Yehova.”
21 Panjira zodutsidwadutsidwa pamveka mawu a ana a Isiraeli, kulira ndi kuchonderera kwawo. Pakuti iwo akhotetsa njira zawo+ ndipo aiwala Yehova Mulungu wawo.+
22 “Bwererani, inu ana opanduka.+ Ndidzachiritsa kusakhulupirika kwanu.”+
“Ife tabwerera! Tabwera kwa inu, pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+
23 Ndithudi, zitunda ndi chipwirikiti chimene chimachitika m’mapiri+ ndiko kupembedza kwachinyengo.+ Kunena zoona chipulumutso cha Isiraeli chili mwa Yehova Mulungu wathu.+
24 Chinthu chochititsa manyazi+ chadya ntchito yolemetsa ya manja a makolo athu kuyambira tili anyamata. Chadya nkhosa zawo, ng’ombe zawo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.
25 Tagona pansi mwamanyazi+ ndipo manyazi athuwo akupitiriza kutiphimba.+ Zimenezi zakhala choncho chifukwa chakuti ifeyo ndi makolo athu, tachimwira Yehova Mulungu wathu+ ndipo sitinamvere mawu a Yehova Mulungu wathu+ kuyambira tili anyamata mpaka lero.”+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “uli ndi nkhope ya mkazi wochita uhule.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.