Yeremiya 49:1-39
49 Ponena za ana a Amoni+ Yehova wanena kuti: “Kodi Isiraeli alibe ana aamuna, kapena kodi alibe wolandira cholowa? N’chifukwa chiyani Malikamu+ watenga Gadi+ kukhala cholowa chake? N’chifukwa chiyani anthu olambira Malikamu akukhala m’mizinda ya Isiraeli?”+
2 “‘Choncho taonani! Masiku adzafika,’ watero Yehova, ‘ndipo Raba,+ umene ndi mzinda wa ana a Amoni, ndidzaulizira chizindikiro chakuti kukubwera nkhondo.+ Ndipo mzindawu udzasanduka bwinja ndi mulu wadothi.+ Midzi yake yozungulira+ idzatenthedwa.’+
“‘Isiraeli adzatenga dziko la anthu amene analanda dziko lake,’+ watero Yehova.
3 “‘Fuula+ iwe Hesiboni+ pakuti mzinda wa Ai wafunkhidwa zinthu zake! Lirani inu midzi yozungulira Raba. Valani ziguduli.+ Lirani mokuwa ndi kuyendayenda m’makola amiyala chifukwa Malikamu adzatengedwa kupita ku ukapolo+ pamodzi ndi ansembe ndi akalonga ake onse.+
4 Bwanji umadzitama chifukwa cha zigwa zako, zigwa zoyenda madzi,+ iwe mwana wamkazi wosakhulupirika? Iwe ukudalira chuma chako,+ ponena kuti: “Ndani angabwere kwa ine?”’”+
5 “Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa+ wanena kuti, ‘Ine ndikukubweretsera chinthu chochititsa mantha+ kuchokera kwa anthu onse okuzungulira. Ndiponso anthu inu mudzabalalitsidwa, aliyense kulowera kwake,+ ndipo sipadzapezeka wosonkhanitsa pamodzi anthu othawawo.’”
6 “‘Pambuyo pake ndidzasonkhanitsa ana a Amoni+ amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,’ watero Yehova.”
7 Ponena za Edomu, Yehova wa makamu wanena kuti: “Kodi nzeru+ zinatha ku Temani?+ Kodi anthu ozindikira sakuperekanso malangizo anzeru? Kodi nzeru zawo zavunda?+
8 Thawani!+ Bwererani! Pitani kumalo otsika kuti mukakhale kumeneko,+ inu okhala ku Dedani!+ Pakuti Esau ndidzamugwetsera tsoka pa nthawi yomulanga.+
9 Kodi okolola mphesa atabwera kwa iwe sadzasiyako zina zoti ena akunkhe? Ndipotu akuba atakubwerera usiku, adzangowononga zokhazo zimene akufuna.+
10 Koma ine ndidzawononga zinthu zonse za Esau ndi kumusiya alibiretu kalikonse.+ Ndidzavundukula malo ake obisika+ moti munthu sadzatha kubisala.+ Mbadwa zake, abale ake ndi anthu oyandikana naye adzafunkhidwa,+ ndipo Esau sadzakhalaponso.+
11 Asiyeni ana anu amasiye.*+ Ine ndidzawasiya amoyo ndipo akazi anu amasiye adzandikhulupirira.”+
12 Yehova wanena kuti: “Taonani! Ngakhale kuti sanazolowere kumwa za m’kapu, iwo adzamwa ndithu.+ Kodi iwe udzasiyidwa osapatsidwa chilango? Ayi, sudzasiyidwa osapatsidwa chilango pakuti udzamwa ndithu za m’kapumo.”+
13 “Ine ndalumbira pa dzina langa+ kuti Bozira+ adzakhala chinthu chodabwitsa, chotonzedwa ndiponso malo owonongedwa.+ Iye adzakhala wotembereredwa ndipo mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka kalekale,”+ watero Yehova.
14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova ndipo nthumwi yatumidwa kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti: “Sonkhanani, muukireni ndi kumuthira nkhondo.”+
15 “Taona! Ndakuchepetsa pakati pa mitundu ina, ndipo ndakupeputsa pakati pa anthu.+
16 Iwe unachititsa anthu kunjenjemera ndiponso unali ndi mtima wodzikuza,+ koma zimenezi zakunyenga, iwe amene ukukhala m’malo obisika a m’thanthwe pamwamba pa phiri. Ngakhale kuti umamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga+ ndidzakugwetsa kuchoka pamenepo,”+ watero Yehova.
17 “Edomu adzakhala chinthu chodabwitsa.+ Aliyense wodutsa pafupi naye adzamuyang’anitsitsa modabwa ndi kumuimbira mluzu chifukwa cha miliri yonse imene idzamugwera.+
18 Monga mmene Sodomu ndi Gomora pamodzi ndi midzi yapafupi inawonongedwera,+ Edomu adzawonongedwanso moti palibe munthu amene adzakhalanso m’dzikolo. Mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo,”+ watero Yehova.
19 “Taona! Wina adzabwera ngati mkango+ kuchokera m’nkhalango zowirira za m’mphepete mwa Yorodano. Iye adzafika pamalo otetezeka+ odyetsera nkhosa koma m’kanthawi kochepa ndidzamuthamangitsa pamalowo.+ Ndidzasankha ndi kuika woyang’anira malowo, pakuti ndani angafanane ndi ine,+ ndipo ndani angalimbane ndi ine,+ komanso ndi m’busa uti tsopano amene angatsutsane nane?+
20 Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha kuchitira Edomu+ ndiponso zimene waganiza kuti achitire anthu okhala ku Temani:+ Ndithudi, chilombo chidzakokera ana a nkhosa uku ndi uku, ndipo chidzawononga malo awo okhala chifukwa cha anthuwo.+
21 Dziko lapansi layamba kugwedezeka chifukwa cha mkokomo wa kugwa kwawo.+ Kukumveka kulira!+ Kulirako kwamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.+
22 Taonani! Wina adzakwera kenako n’kutsika ngati chiwombankhanga chimene chikufuna kugwira chakudya chake.+ Adzatambasulira mapiko ake pa Bozira,+ ndipo pa tsikulo mtima wa amuna amphamvu a ku Edomu udzakhala ngati mtima wa mkazi amene akumva zowawa za pobereka.”+
23 Uthenga wokhudza Damasiko+ ndi wonena kuti: “Hamati+ ndi Aripadi+ achita manyazi chifukwa chakuti amva uthenga woipa. Iwo apasuka+ ndipo nyanja yawinduka, moti singathe kukhala bata.+
24 Damasiko wachita mantha. Watembenuka ndi kuthawa ndipo wapanikizika.+ Iye wagwidwa ndi nkhawa ndiponso zowawa za pobereka ngati zimene zimagwira mkazi amene akubereka.+
25 Kodi zatheka bwanji kuti anthu asachoke mumzinda wotamandika, mudzi wobweretsa chisangalalo?+
26 “Choncho anyamata ake adzaphedwa m’mabwalo ake, ndipo amuna ake ankhondo adzawakhalitsa chete pa tsiku limenelo,”+ watero Yehova wa makamu.
27 “Mipanda ya Damasiko ndidzaiyatsa moto, ndipo motowo udzatentha nsanja zokhalamo za Beni-hadadi.”+
28 Ponena za Kedara+ ndi maufumu a Hazori+ amene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anawapha,+ Yehova wanena kuti: “Nyamukani amuna inu, pitani ku Kedara ndipo mukafunkhe zinthu za ana a Kum’mawa.+
29 Mahema awo,+ nkhosa zawo,+ nsalu za mahema awo ndi zinthu zawo zonse zidzatengedwa.+ Ngamila zawo+ zidzalandidwa. Anthu adzawalirira kuti, ‘Zochititsa mantha zili paliponse!’”+
30 “Thawani, thawirani kutali. Tsikirani kumalo akuya kuti mukakhale kumeneko, inu okhala ku Hazori,”+ watero Yehova. “Pakuti Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ waganiza zokuukirani ndi kukuchitirani zoipa.”
31 “Nyamukani, amuna inu. Pitani kukaukira mtundu wa anthu umene ukukhala mosatekeseka+ ndi mwamtendere!”+ watero Yehova.
“Kumeneko kulibe zitseko ndi mipiringidzo. Anthu ake amakhala kwaokhaokha.+
32 Ngamila zawo+ zidzafunkhidwa ndipo ziweto zawo zochulukazo zidzawonongedwa. Anthu amene amadulira ndevu zawo za m’mbali+ ndidzawabalalitsira kumbali zonse.*+ Ndidzawagwetsera tsoka kuchokera kumadera onse owazungulira,” watero Yehova.
33 “Hazori+ adzakhala malo obisalamo mimbulu+ ndipo adzakhala bwinja mpaka kalekale. Palibe munthu amene adzakhala kumeneko, moti mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo.”+
34 Yehova anauza Yeremiya mawu okhudza Elamu+ kuchiyambi kwa ufumu wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, kuti:
35 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndikuthyola uta wa Aelamu,+ umene ndiwo mphamvu yawo yaikulu.
36 Anthu a ku Elamu ndidzawabweretsera mphepo zinayi kuchokera kumalekezero anayi a kumwamba.+ Ndidzawabalalitsira kumphepo zonsezi+ ndipo sipadzapezeka mtundu wa anthu kumene obalalitsidwa+ a Elamu sadzapitako.’”
37 “Aelamu ndidzawachititsa mantha pamaso pa adani awo ndi pamaso pa anthu amene akufunafuna moyo wawo. Ndidzawabweretsera tsoka, mkwiyo wanga woyaka moto,”+ watero Yehova. “Ndidzawatumizira lupanga kufikira nditawafafaniza.”+
38 “Ndidzaika mpando wanga wachifumu ku Elamu,+ ndipo kumeneko ndidzawononga ndi kuchotsa mfumu ndi akalonga,” watero Yehova.
39 “Ndiyeno m’masiku otsiriza+ ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a ku Elamu amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,”+ watero Yehova.
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “ana anu aamuna opanda abambo.”
^ Mawu ake enieni, “kumphepo zonse,” kutanthauza kumbali zonse kumene mphepo imapita.