Yeremiya 14:1-22

14  Mawu amene Yehova anauza Yeremiya pa nkhani ya chilala+ ndi awa:  Yuda akulira maliro+ ndipo zipata zake zagwetsedwa.+ Zagwetsedwa pansi+ ndipo kulira kwa Yerusalemu kwamveka kumwamba.+  Anthu otchuka atuma anthu wamba kukatunga madzi.+ Anthu wambawo afika kuzitsime koma sanapeze madzi.+ Abwerera ndi ziwiya zopanda kanthu. Achita manyazi+ ndipo akhumudwa moti aphimba mitu yawo.+  Alimi achita manyazi moti aphimba mitu yawo chifukwa chakuti m’dzikomo simunagwe mvula+ ndipo nthaka yawonongeka.+  Mbawala yaikazi yabereka mwana mthengo, koma yamusiya chifukwa kulibe msipu.  Mbidzi+ zangoima chilili m’mapiri opanda kanthu. Zikupuma mwawefuwefu ngati mimbulu. Maso awo achita mdima chifukwa kulibe msipu.+  Ngakhale kuti zolakwa zathu n’zoonekeratu, inu Yehova, chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu,+ pakuti zochita zathu zosonyeza kusakhulupirika zachuluka+ ndipo takuchimwirani.+  Inu chiyembekezo cha Isiraeli,+ Mpulumutsi wake+ pa nthawi ya nsautso,+ n’chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo m’dzikoli? N’chifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wapaulendo amene wapatuka kuti agone usiku umodzi wokha?+  N’chifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru ndiponso ngati munthu wamphamvu amene sangathe kupulumutsa anthu ake?+ Komatu inu Yehova muli pakati pathu,+ ndipo ife tatchedwa ndi dzina lanu.+ Musatisiye. 10  Ponena za anthu awa Yehova wati: “Iwo akukonda kuyendayenda+ ndipo sanalamulire mapazi awo.+ Choncho Yehova sakukondwera nawo,+ moti adzakumbukira zolakwa zawo ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.”+ 11  Yehova anapitiriza kundiuza kuti: “Usapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.+ 12  Pamene akusala kudya ine sindikumvetsera kuchonderera kwawo.+ Pamene akupereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zambewu ine sindikukondwera nazo,+ ndipo ndiwawononga ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.”+ 13  Pamenepo ndinati: “Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Lupanga silidzakukanthani, ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni m’malo ano.’”+ 14  Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera monama m’dzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula, kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo anthu inu, ndiwo masomphenya onama, maula, mawu opanda pake+ ndi chinyengo cha mumtima mwawo.+ 15  Choncho Yehova wanena kuti: ‘Kunena za aneneriwo amene akulosera m’dzina langa ngakhale kuti sindinawatume, amenenso akunena kuti lupanga kapena njala sizidzafika m’dziko lino, ndidzawawononga ndi lupanga ndiponso njala.+ 16  Anthu amene akuwauza maulosi awowo, mitembo yawo idzatayidwa m’misewu ya Yerusalemu chifukwa cha njala ndi lupanga. Sipadzakhala wowaika m’manda, iwowo, akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi+ chifukwa ndidzawatsanulira tsoka pamutu pawo.’+ 17  “Ndiyeno uwauze kuti, ‘Maso anga atulutse misozi usiku ndi usana ndipo asasiye kutulutsa misozi,+ pakuti pamveka kugunda kwakukulu ndipo namwali, mwana wamkazi wa anthu anga wawonongedwa.+ Iye wawonongedwa ndi chilonda chachikulu cha mkwapulo chosachiritsika.+ 18  Ndipo ndikapita kunja kwa mzinda, ndikuona anthu ophedwa ndi lupanga.+ Komanso ndikalowa mkati mwa mzinda ndikuona matenda obwera chifukwa cha njala.+ Aneneri ndi ansembe, onse ayenda njira zosiyanasiyana kupita kudziko limene sakulidziwa.’”+ 19  Kodi Yuda mwamukaniratu,+ kapena kodi mukunyansidwa ndi Ziyoni?+ N’chifukwa chiyani mwatikantha popanda wotichiritsa?+ Anthu anali kuyembekezera mtendere, koma palibe chabwino chimene chachitika. Anali kuyembekezera nthawi yochiritsidwa, koma taonani, kukuchitika zoopsa zokhazokha.+ 20  Inu Yehova, ife tikuvomereza kuipa kwathu ndi kulakwa kwa makolo athu.+ Inde, takuchimwirani.+ 21  Koma chifukwa cha dzina lanu, musatisiye.+ Musanyazitse mpando wanu wachifumu waulemerero.+ Kumbukirani pangano lanu limene munachita ndi ife ndipo musaliphwanye.+ 22  Kodi pakati pa mafano opanda pake a mitundu ya anthu pali fano lililonse+ limene lingagwetse mvula? Kapena kodi kumwamba pakokha kungagwetse mvula yamvumbi?+ Kodi si inu Yehova Mulungu wathu+ amene mumachititsa zimenezi? Chiyembekezo chathu chili mwa inu chifukwa ndinu amene mumachititsa zonsezi.+

Mawu a M'munsi