Yeremiya 23:1-40

23  “Tsoka abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pamalo anga odyetsera ziweto!”+ watero Yehova.  Yehova Mulungu wa Isiraeli wadzudzula abusa amene akuweta anthu ake kuti: “Inu mwabalalitsa nkhosa zanga. Mukupitiriza kuzimwaza ndipo simukuzisamalira.”+ “Tsopano ndikutembenukira kwa inu chifukwa cha zochita zanu zoipazo,”+ watero Yehova.  “Ine ndidzasonkhanitsa pamodzi nkhosa zanga zotsala kuchokera m’mayiko onse kumene ndinazibalalitsira+ ndipo ndidzazibwezeretsa kumalo awo kumene zimadyera.+ Nkhosazo zidzaberekana ndi kuchuluka.+  Ndidzapatsa nkhosazo abusa ndipo adzaziweta.+ Sizidzaopanso kanthu kapena kugwidwa ndi mantha aakulu,+ ndipo palibe imene idzasowa,” watero Yehova.  “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+  M’masiku a mfumu imeneyi, Yuda adzapulumutsidwa,+ ndipo Isiraeli adzakhala mwabata.+ Dzina la mfumuyi lidzakhala Yehova Ndiye Chilungamo Chathu.”+  “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene sadzalumbiranso kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo.’+  Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a m’nyumba ya Isiraeli ndi kuwabweretsa kuno kuchokera m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene ndinawabalalitsira’ ndipo adzakhala m’dziko lawo.”+  Mtima wanga wasweka mkati mwanga chifukwa cha aneneri. Mafupa anga onse ayamba kunjenjemera. Ndakhala ngati munthu woledzera,+ komanso mwamuna wamphamvu amene wagonjetsedwa ndi vinyo, chifukwa cha Yehova komanso chifukwa cha mawu ake oyera. 10  Dzikoli ladzaza+ ndi anthu achigololo+ ndipo chifukwa cha matemberero, dziko likulira maliro+ ndipo malo a m’chipululu odyetsera ziweto auma.+ Zochita za anthuwa ndi zoipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo mopanda chilungamo. 11  “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa+ ndipo m’nyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ watero Yehova. 12  “Choncho, njira zawo zidzawakhalira ngati malo oterera+ amdima ndipo adzawakankhira m’njirazo moti adzagwa.”+ “Pakuti ndidzawagwetsera tsoka, tsiku la chilango chawo lidzafika,”+ watero Yehova. 13  “Ndaona zosayenera mwa aneneri a ku Samariya.+ Iwo atumikira ngati aneneri a Baala+ ndipo asocheretsa anthu anga, Aisiraeli.+ 14  Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndaona zinthu zoopsa.+ Iwo achita chigololo+ ndi kuchita zinthu mwachinyengo.+ Alimbikitsa anthu ochita zoipa kuti aliyense asafooke ndi kusiya+ kuchita zoipa zake. Kwa ine, onsewo akhala ngati Sodomu+ ndipo anthu okhala mumzindawu akhala ngati Gomora.”+ 15  Choncho Yehova wa makamu wadzudzula aneneriwo kuti: “Ndiwadyetsa chitsamba chowawa ndipo ndiwamwetsa madzi apoizoni.+ Chifukwa kuchokera mwa aneneri a ku Yerusalemu mpatuko+ wafalikira m’dziko lonse.” 16  Yehova wa makamu wanena kuti: “Musamvere mawu a aneneri amene akulosera kwa anthu inu.+ Akukulimbikitsani kuchita zinthu zopanda pake.+ Iwo akulankhula masomphenya a mumtima mwawo+ osati ochokera m’kamwa mwa Yehova.+ 17  Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+ 18  Ndani waimirira pagulu la anthu amene Yehova amawakonda+ kuti azindikire ndi kumva mawu ake?+ Ndani watchera khutu kuti amvetsere mawu ake?+ 19  Taonani! Mphepo yamkuntho yochokera kwa Yehova idzawomba. Mkwiyo wake udzawomba ngati kamvulumvulu wamphamvu.+ Udzawomba pamitu ya anthu oipawo.+ 20  Mkwiyo wa Yehova sudzatha kufikira atachita zofuna za mtima wake+ ndi kuzikwaniritsa.+ M’masiku otsiriza, anthu inu mudzalingalira zimenezi ndipo mudzazimvetsa.+ 21  “Ine sindinatumize aneneriwo, koma okha anathamanga. Ine sindinalankhule nawo, koma okha analosera.+ 22  Ngati iwo akanaima pagulu la anthu amene ndimawakonda,+ akanachititsa anthu anga kumva mawu anga, ndipo akanabweza anthu anga panjira zawo zoipa komanso pa zochita zawo zoipa.”+ 23  Yehova wanena kuti: “Kodi ine ndine Mulungu amene amangokhala pafupi, osati Mulungu amenenso ali kutali?”+ 24  “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova. “Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova. 25  “Ndamva zimene aneneri akulosera monama m’dzina langa+ kuti, ‘Ndalota maloto! Ndalota maloto!’+ 26  Kodi aneneri amene akulosera monamawa, amene akunenera chinyengo cha mumtima mwawo, adzakhala ndi chinyengo chimenechi mumtima mwawo kufikira liti?+ 27  Iwo akuganiza zochititsa anthu anga kuiwala dzina langa pogwiritsa ntchito maloto amene aneneriwo amauzana nthawi zonse,+ monga mmene makolo awo anaiwalira dzina langa chifukwa cha Baala.+ 28  Mneneri amene walota maloto anene maloto akewo. Koma amene ndamuuza mawu anga, alankhule mawu angawo moona.”+ “Kodi mapesi a tirigu angafanane ndi tirigu weniweniyo?”+ watero Yehova. 29  Yehova wanena kuti: “Kodi mawu anga safanana ndi moto?+ Kodi safanana ndi nyundo imene imaphwanya thanthwe?”+ 30  “Chotero ndikutsutsana ndi aneneriwo+ chifukwa aliyense wa iwo akuba mawu anga kwa mnzake,”+ watero Yehova. 31  Yehova wanena kuti: “Ine ndikutsutsana ndi aneneriwo chifukwa akugwiritsa ntchito lilime lawo ndi kunena kuti, ‘Awa ndi mawu ochokera kwa Mulungu!’”+ 32  “Ine ndikutsutsana ndi aneneri amene akulota maloto onama, amene akunena malotowo ndi kusocheretsa anthu anga ndi bodza lawo+ komanso ndi kudzitama kwawo,”+ watero Yehova. “Koma ine sindinawatume kapena kuwalamula kuchita zimenezo. Choncho sadzachita zopindulitsa anthu awa,”+ watero Yehova. 33  “Anthu awa, aneneri, kapena ansembe akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga* wa Yehova ukuti chiyani?’+ uwayankhe kuti, ‘“Anthu inu ndinu katundu wolemetsa!+ Ndipo ndidzakusiyani,”+ watero Yehova.’ 34  Mneneri, wansembe, kapena aliyense amene akunena kuti, ‘Uthenga uwu ndi katundu wolemetsa wa Yehova!’ ndidzatembenukira kwa iye ndi kwa nyumba yake.+ 35  Aliyense wa inu akuuza mnzake ndi m’bale wake kuti, ‘Kodi Yehova wayankha kuti chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani?’+ 36  Koma anthu inu musanenenso kuti uthenga wa Yehova ndi katundu wolemetsa,+ pakuti mawu a aliyense wa inu ndi katundu wake wolemetsa,+ pakuti mwasintha mawu a Mulungu wathu wamoyo,+ Yehova wa makamu. 37  “Mneneri umufunse kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani?+ 38  Ndipo mukapitiriza kunena kuti, “Uthenga uwu ndi katundu wolemetsa wa Yehova!” Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti mukunenabe kuti, ‘Mawu a Yehova ndi katundu wolemetsa,’ pamene ine ndinakuuzani kuti ‘Musamanene kuti: “Mawu a Yehova ndi katundu wolemetsa!”’ 39  tsopano ine ndikukusiyani nokhanokha anthu inu.+ Ndikusiya inuyo ndi mzinda umene ndinapatsa inu ndi makolo anu. Ndikuchita zimenezi kuti musakhalenso pamaso panga.+ 40  Ndidzaika chitonzo pa inu mpaka kalekale ndipo mudzanyozeka mpaka kalekale. Zimenezi sizidzaiwalika.”’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kulemera.” Mawu achiheberi otanthauza “katundu wolemetsa” ali ndi matanthauzo awiri. Panopa m’lembali akutanthauza uthenga wamphamvu wochokera kwa Mulungu, koma pamalo otsatira m’lemba lomweli akutanthauza kuti anthuwo anali katundu wolemetsa kwa Mulungu. Choncho poyankha, Yeremiya anagwiritsa ntchito mawuwa chifukwa cha matanthauzo ake awiriwa.