Yeremiya 43:1-13
43 Ndiyeno Yeremiya atamaliza kuuza anthu onse mawu onse a Yehova Mulungu wawo, amene Yehova Mulungu anatuma Yeremiya kukawauza,+
2 Azariya mwana wa Hoshaya,+ Yohanani+ mwana wa Kareya ndi anthu enanso odzikuza+ anauza Yeremiya kuti: “Ukunena zabodza. Yehova Mulungu wathu sanakutume kudzatiuza+ kuti, ‘Musapite ku Iguputo kuti mukakhale kumeneko monga alendo.’+
3 Koma Baruki+ mwana wa Neriya ndiye akukulimbikitsa kunena zinthu zofuna kutipweteketsa ndi cholinga chotipereka m’manja mwa Akasidi kuti atiphe kapena kutitenga kupita ku ukapolo ku Babulo.”+
4 Chotero Yohanani mwana wa Kareya, akuluakulu onse a magulu ankhondo ndi anthu onse sanamvere mawu a Yehova+ kuti apitirize kukhala m’dziko la Yuda,+
5 moti Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo anatenga otsala a Yuda amene anabwerera kuchokera ku mitundu yonse ya anthu kumene anathawira kuti akhale m’dziko la Yuda kwa kanthawi kochepa.+
6 Anatenga amuna amphamvu, akazi awo, ana aang’ono, ana aakazi a mfumu+ ndiponso aliyense amene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu analola kuti akhale ndi Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani.+ Anatenganso mneneri Yeremiya ndi Baruki+ mwana wa Neriya.
7 Pamapeto pake anafika ku Iguputo+ chifukwa sanamvere mawu a Yehova ndipo patapita nthawi anakafika ku Tahapanesi.+
8 Tsopano pamene Yeremiya anali ku Tahapanesi, Yehova anamuuza kuti:
9 “Tenga miyala ikuluikulu ndipo ukaibise m’dothi limene anamangira chiunda cha njerwa chimene chili pakhomo la nyumba ya Farao ku Tahapanesi. Ukachite zimenezi amuna onse achiyuda akuona.+
10 Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Inetu ndikuitana Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ mtumiki wanga,+ ndipo ndidzaika mpando wake wachifumu pamwamba penipeni pa miyala iyi imene ndaibisa. Iye adzamanga hema wake waulemerero pamwamba pa miyala imeneyi.
11 Nebukadirezara adzabwera kudzathira nkhondo dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo. Woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+
12 Nyumba za milungu ya Iguputo ndidzaziyatsa moto.+ Nebukadirezara adzatentha milunguyo ndi kuitenga kupita nayo kudziko lina. Monga mmene m’busa savutikira kuvala chovala chake,+ Nebukadirezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo ndi kuchokako atapambana.
13 Iye adzaphwanyaphwanya zipilala za ku Beti-semesi,* mzinda umene uli ku Iguputo. Ndipo nyumba za milungu ya Iguputo adzazitentha.”’”
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “Nyumba ya Dzuwa.”