Yeremiya 10:1-25
10 Anthu inu, a m’nyumba ya Isiraeli, imvani zimene Yehova wanena zokutsutsani.
2 Yehova wanena kuti: “Musaphunzire njira za anthu a mitundu ina ngakhale pang’ono,+ ndipo musamaope zizindikiro zakumwamba, chifukwa anthu a mitundu ina amachita mantha ndi zizindikirozo.+
3 Miyambo ya anthu amenewa+ ndi yopanda pake, chifukwa mmisiri amagwetsa mtengo+ m’nkhalango ndi kusema fano pogwiritsa ntchito sompho.+
4 Akatero amakongoletsa fanolo ndi siliva komanso golide.+ Kenako amatenga nyundo ndi kukhomerera mafanowo pansi ndi misomali kuti asagwe.+
5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+
6 Ndithudi palibe aliyense wofanana ndi inu Yehova.+ Inu ndinu wamkulu, ndipo dzina lanu ndi lalikulu ndi lamphamvu.+
7 Kodi ndani amene sangakuopeni,+ inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa, chifukwa chakuti pakati pa anzeru onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+
8 Onse pamodzi ndi opanda nzeru ndiponso opusa.+ Mtengo umangowalimbikitsa kuchita zachabechabe.+
9 Siliva wosulidwa kukhala mapalemapale amachokera ku Tarisi+ ndipo golide amachokera ku Ufazi.+ Zonsezi zimakonzedwa mwaluso, ndipo ndi ntchito ya manja a mmisiri wa zitsulo. Mafanowo amawaveka zovala zaulusi wabuluu ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. Nawonso angokhala ntchito ya amisiri aluso.+
10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+
11 Mitunduyo mukaiuze izi anthu inu: “Milungu+ imene sinapange kumwamba ndi dziko lapansi+ ndi imene idzawonongedwe padziko lapansi, pansi pa thambo.”
12 Mulungu woona ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake,+ amene mwanzeru zake+ anakhazikitsa dziko limene anthu amakhalamo. Iye ndi amenenso anayala kumwamba mwa kuzindikira kwake.+
13 Mawu ake amapangitsa madzi akumwamba kuchita mkokomo,+ ndipo amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Iye wapanganso zipata zotulukirapo mvula+ ndipo amatulutsa mphepo yamkuntho m’nkhokwe zake.+
14 Munthu aliyense wachita zinthu mopanda nzeru kwambiri moti ndi zoonekeratu kuti sakudziwa kalikonse.+ Mmisiri wa zitsulo aliyense adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+ Pakuti chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonama+ ndipo mafano amenewa alibe moyo.+
15 Iwo ndi achabechabe, ntchito yoyenera kutonzedwa.+ Mulungu akadzatembenukira kwa iwo, adzawawononga.+
16 Koma Mulungu wa Yakobo+ sali ngati mafanowa. Iye ndi amene anapanga china chilichonse.+ Isiraeli ndiye ndodo ya cholowa chake.+ Dzina la Mulunguyo ndi Yehova wa makamu.+
17 Iwe mkazi wokhala m’masautso,+ sonkhanitsa ndi kunyamula katundu wako.+
18 Yehova wanena kuti: “Tsopano nditaya kutali anthu okhala padziko lapansi,+ ndipo ndiwachititsa kuvutika mtima kuti adziwe masautso awo.”+
19 Tsoka ine chifukwa cha kuwonongedwa kwanga!+ Chilonda changa cha mkwapulo chakhala chosachiritsika. Ndipo ndanena kuti: “Ndithudi amenewa ndi matenda anga ndipo ndidzakhalabe nawo.+
20 Hema wanga wafunkhidwa, ndipo zingwe zanga zonse zomangira hemayo aziduladula.+ Ana anga aamuna achoka ndi kundisiya ndipo kulibenso.+ Komanso palibe wotambasula kapena kudzutsa hema wanga.
21 Abusa achita zinthu mopanda nzeru,+ ndipo sanayese n’komwe kufunafuna Yehova.+ N’chifukwa chake sanachite zinthu mozindikira, ndipo ziweto zawo zonse zabalalika.”+
22 Tamvetserani nkhani imene yamveka! Kugunda kwakukulu kukumveka kuchokera kudziko la kumpoto,+ ndipo kudzasandutsa mizinda ya Yuda kukhala mabwinja, malo obisalamo mimbulu.+
23 Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.+
24 Ndikonzeni, inu Yehova. Koma mundikonze ndi chiweruzo chanu+ osati mutakwiya+ chifukwa mungandifafanize.+
25 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu+ amene akunyalanyazani,+ ndi pa mafuko amene sakuitana padzina lanu.+ Pakuti iwo adya Yakobo.+ Amudya ndipo akupitirizabe kumuwononga.+ Malo ake okhalamo awasandutsa bwinja.+