Yeremiya 42:1-22

42  Kenako akuluakulu onse a magulu ankhondo, Yohanani+ mwana wa Kareya, Yezaniya+ mwana wa Hoshaya+ ndi anthu onse osasiyapo aliyense, anapita  kwa mneneri Yeremiya ndi kumuuza kuti: “Chonde, tikomere mtima ndipo utipempherere kwa Yehova Mulungu wako.+ Pempherera anthu onse amene atsalawa chifukwa amene tatsala tilipo ochepa monga mmene ukutioneramu, ngakhale kuti tinalipo anthu ambiri.+  Ndipo Yehova Mulungu wako atiuze njira yoti tiyendemo ndi zoti tichite.”+  Pamenepo mneneri Yeremiya anawayankha kuti: “Ndamva zimene mwanenazo. Ndipemphera kwa Yehova Mulungu wanu malinga ndi zimene mwapempha.+ Ndipo mawu aliwonse amene Yehova angakuyankheni ndidzakuuzani.+ Sindidzakubisirani kalikonse.”+  Ndiyeno iwo anauza Yeremiya kuti: “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika, ndipo atilange+ ngati sitidzachita ndendende mogwirizana ndi mawu onse amene Yehova Mulungu wako angakutume kwa ife.+  Kaya mawu a Yehova Mulungu wathu ndi otikomera kapena otiipira, ife tidzamvera mawuwo. Tidzatero kuti zinthu zitiyendere bwino chifukwa chomvera mawu a Yehova Mulungu wathu.”+  Tsopano patapita masiku 10, Yehova analankhula ndi Yeremiya.+  Kenako Yeremiya anaitana Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali naye. Anaitananso anthu ena onse osasiyapo aliyense.+  Iye anawauza kuti: “Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli kukamupempha kuti akukomereni mtima.+ Tsopano iye wanena kuti, 10  ‘Ngati mungakhalebe m’dziko lino,+ ndidzakulimbitsani osati kukupasulani, ndidzakubzalani osati kukuzulani,+ pakuti ndidzakumverani chisoni chifukwa cha tsoka limene ndakugwetserani.+ 11  Musachite mantha ndi mfumu ya Babulo imene mukuiopayo.’+ “‘Mfumu imeneyi musachite nayo mantha,+ chifukwa ine ndili ndi inu kuti ndikupulumutseni ndi kukulanditsani m’manja mwake,’+ watero Yehova. 12  Ndidzakuchitirani chifundo moti mfumuyo idzakumverani chifundo ndi kukubwezerani kudziko lanu.+ 13  “‘Koma ngati munganene kuti: “Ayi! Ife sitikhala m’dziko lino,” kumene ndi kusamvera mawu a Yehova Mulungu wanu,+ 14  ndipo mukapitiriza kunena kuti: “Ife tikupita kukakhala ku Iguputo,+ kumene sitidzaona nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga komanso kumene sitidzasowa chakudya, moti tikupita kukakhala kudziko limenelo,”+ 15  mverani mawu a Yehova, inu otsala a Yuda. Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ngati mwatsimikiza mtima kukakhala ku Iguputo ndipo mwalowadi m’dzikolo ndi kukhala kumeneko monga alendo,+ 16  ndiye kuti lupanga limene mukuliopa lidzakupezani ku Iguputo+ komweko ndipo njala yaikulu imene mukuithawa idzakutsatirani ku Iguputoko+ moti mudzafera komweko.+ 17  Amuna onse amene atsimikiza mtima kukakhala ku Iguputo monga alendo ndiwo adzafa ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri.+ Pakati pawo sipadzapezeka wopulumuka kapena wothawa chifukwa ndidzawagwetsera tsoka.”’+ 18  “Yehova Mulungu wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Monga mmene ndinasonyezera anthu okhala mu Yerusalemu+ mkwiyo ndi kupsa mtima kwanga, inunso ndidzakusonyezani mkwiyo wanga chifukwa chakuti mwakakhala ku Iguputo. Mudzakhala otembereredwa ndipo mudzakhala chinthu chodabwitsa ndi chotonzedwa,+ moti malo ano simudzawaonanso.’+ 19  “Yehova wakutsutsani inu otsala a Yuda. Musapite ku Iguputo.+ Ine ndikuchitira umboni lero+ 20  kuti mwachimwira miyoyo yanu.+ Zili choncho chifukwa inu mwandituma kwa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu ndipo udzatiuze zilizonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndipo ife tidzachita zomwezo.’+ 21  Koma inu simudzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu kapena chilichonse chimene wandituma chimene ndakuuzani lero.+ 22  Tsopano dziwani kuti, ndithu mudzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu ndi mliri m’dziko limene mukulakalaka kukalowamo kuti mukakhale monga alendo kumeneko.”+

Mawu a M'munsi