Yeremiya 5:1-31
5 Pitani mukayendeyende m’misewu ya mu Yerusalemu kuti mukaone, mukafufuze m’mabwalo ake ndi kudziwa ngati mungapezeke munthu,+ ngati muli aliyense wochita chilungamo,+ kapena aliyense wokhulupirika.+ Ngati mungamupeze munthu woteroyo, ndidzaukhululukira mzinda umenewu.
2 Ngakhale atalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo!” adzakhala akulumbira mwachinyengo.+
3 Inu Yehova, kodi maso anu sakulakalaka kuona munthu wokhulupirika?+ Mwawalanga+ koma sanamve kupweteka.+ Ngakhale kuti munatsala pang’ono kuwafafaniza onse,+ iwo sanaphunzirepo* kanthu.+ Anaumitsa nkhope zawo ngati thanthwe.+ Ndipo anakana kubwerera kwa inu.+
4 Ine ndinati: “Ndithudi, amenewa ndi anthu onyozeka. Anachita zinthu mopusa, pakuti anakana njira ya Yehova. Anakana chilamulo cha Mulungu wawo.+
5 Ndidzapita kwa akuluakulu ndi kulankhula nawo,+ pakuti mosakayikira aganizira njira ya Yehova ndi chilamulo cha Mulungu wawo.+ Ndithudi onsewo athyola goli la Mulungu ndipo mosakayikira adula zomangira za Mulungu.”+
6 N’chifukwa chake mkango wa m’nkhalango wawaukira, mmbulu wa m’chipululu ukupitirizabe kuwawononga+ ndipo kambuku* akukhalabe tcheru pa mizinda yawo.+ Aliyense wotuluka m’mizindayo amakhadzulidwakhadzulidwa, chifukwa zolakwa zawo zachuluka ndipo zochita zawo za kusakhulupirika zawonjezeka kwambiri.+
7 Kodi ndingakukhululukire bwanji zinthu zimenezi? Ana ako aamuna andisiya ndipo amalumbira+ pa zinthu zina osati Mulungu.+ Ndinali kuwapatsa zofuna zawo+ koma anapitiriza kuchita chigololo+ ndipo anali kupita kunyumba ya hule m’magulumagulu.
8 Iwo akhala ngati mahatchi amphongo achilakolako champhamvu chofuna kukwera, okhala ndi mavalo amphamvu. Aliyense amamemesa* mkazi wa mnzake.+
9 “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova.+ “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu wa anthu amakhalidwe oterewa?”+
10 “Bwerani mudzaukire mizere yake ya mitengo ya mpesa ndi kuiwononga,+ koma anthu inu musaifafaniziretu.+ M’chotsereni mphukira zake zamasamba ambiri chifukwa si za Yehova.+
11 Pakuti a m’nyumba ya Isiraeli ndi a m’nyumba ya Yuda andichitiradi zachinyengo,” watero Yehova.+
12 “Iwo akana Yehova, ndipo akunena kuti, ‘Iye kulibe.+ Ndipo ife tsoka silidzatigwera. Sitidzaona lupanga lililonse kapena njala yaikulu.’+
13 Aneneri nawonso akulankhula zopanda pake ndipo mwa iwo mulibe mawu a Mulungu.+ Iwo adzakhala opanda pake ngati mawu awo omwewo.”
14 Chotero Yehova, Mulungu wa makamu wanena kuti: “Pakuti iwo akunena zimenezi, ndichititsa mawu anga m’kamwa mwako kukhala ngati moto+ koma anthu awa adzakhala ngati nkhuni ndipo motowo udzawanyeketsa.”+
15 “Tsopano anthu inu, ndikukubweretserani mtundu wa anthu akutali,+ inu a m’nyumba ya Isiraeli,” watero Yehova. “Umenewu ndi mtundu umene wakhalapo kwa nthawi yaitali,+ mtundu wakale, mtundu umene chilankhulo chawo simuchidziwa ndipo simungamve ndi kuzindikira zimene akulankhula.
16 Kachikwama kawo koikamo mivi kali ngati manda otseguka. Onse ndi amuna amphamvu.+
17 Iwo adzadya zokolola zanu ndi mkate wanu.+ Amuna amenewo adzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi. Adzadya nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu. Adzadya mtengo wanu wa mpesa ndi mtengo wanu wa mkuyu.+ Iwo adzagwetsa ndi lupanga mizinda yanu imene mumaidalira, yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.”
18 Yehova wanena kuti: “Ngakhale masiku amenewo sindidzakufafanizani nonse anthu inu.+
19 Ndiyeno mudzanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu watichitira zonsezi?’+ Pamenepo ukawayankhe kuti, ‘Popeza mwandisiya ine Mulungu wanu ndipo mwapita kukatumikira mulungu wachilendo m’dziko lanu, mudzatumikiranso alendo m’dziko limene si lanu.’”+
20 Mukanene izi m’nyumba ya Yakobo ndi kuzilengeza mu Yuda kuti:
21 “Tsopano tamverani izi anthu opusa inu, anthu opanda nzeru mumtima mwanu,+ amene muli ndi maso koma simukuona,+ muli ndi makutu koma simukumva.+
22 ‘Kodi simundiopa?’+ watero Yehova. ‘Kapena kodi simukumva ululu waukulu chifukwa cha ine?+ Ine ndinaika mchenga kukhala malire a nyanja, malire okhalapo mpaka kalekale amene nyanjayo singadutse. Ngakhale kuti mafunde amawinduka sangadutse malirewo ndipo ngakhale amachita phokoso sangawapitirire.+
23 Koma anthu awa ali ndi mtima wouma ndi wopanduka. Achoka panjira yanga ndipo akuyenda m’njira yawo.+
24 Mumtima mwawo sananene kuti: “Tsopano tiyeni tiope Yehova Mulungu wathu,+ amene amatigwetsera mvula. Amatigwetsera mvula yoyamba ndi yomalizira pa nyengo yake,+ ndipo amaonetsetsa kuti tili ndi milungu yoikidwiratu imene timakolola.”+
25 Zolakwa zanu ndi zimene zachititsa kuti zinthu zimenezi zithe ndipo machimo anu akutsekerezerani zabwino.+
26 “‘Zili choncho, chifukwa pakati pa anthu anga papezeka anthu oipa.+ Iwo amawabisalira ndi kuwayang’anitsitsa ngati mmene wosaka mbalame amachitira.+ Awatchera msampha wowononga pakuti iwo amagwira anthu.
27 Nyumba zawo zadzaza chinyengo+ ngati mmene mbalame zimadzazira m’chikwere.* N’chifukwa chake iwo alemera ndipo apeza chuma chambiri.+
28 Iwo anenepa+ ndipo matupi awo asalala. Achitanso zinthu zoipa zosawerengeka. Iwo sanaweruze mlandu wa munthu aliyense mwachilungamo,+ ngakhale mlandu wa mwana wamasiye,*+ pofuna kuti zinthu ziwayendere bwino.+ Iwo sanachitire chilungamo munthu wosauka.’”
29 “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova. “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu wa anthu amakhalidwe oterewa?+
30 Chinthu chodabwitsa, chinthu choopsa, chafika m’dziko:+
31 Aneneri akulosera monama,+ ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo.+ Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Ndipo kodi anthu inu mudzachita chiyani pamapeto pake?”+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “nyalugwe.”
^ Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”