Yeremiya 17:1-27

17  “Tchimo la Yuda lalembedwa ndi chitsulo chogobera.+ Lalembedwa ndi cholembera cha dayamondi m’mitima+ yawo ndi panyanga za guwa lansembe.+  Ngakhale ana awo aamuna akumbukira maguwa awo ansembe ndi mizati yawo yopatulika imene ili pansi pa mtengo waukulu wamasamba ambiri obiriwira, pamwamba pa zitunda zazitali+  ndi pamapiri. Katundu wanu ndi chuma chanu chonse ndidzazipereka kuti anthu azifunkhe.+ Ndidzapereka malo anu okwezeka chifukwa cha tchimo limene lachitika m’madera anu onse.+  Mwa kufuna kwanu munataya cholowa chimene ndinakupatsani.+ Inenso ndidzakuchititsani kutumikira adani anu m’dziko limene simunalidziwe.+ Anthu inu, ndakuyatsani ndi mkwiyo wanga+ ndipo moto wake udzayakabe mpaka kalekale.”  Yehova wanena kuti: “Wotembereredwa ndi munthu aliyense wokhulupirira mwa munthu aliyense wochokera kufumbi.+ Wotembereredwa ndi munthu amene amadalira mphamvu za dzanja la munthu,+ komanso amene mtima wake wapatuka kuchoka kwa Yehova.+  Adzakhala ngati mtengo umene uli pawokhawokha m’chipululu ndipo zabwino zikadzafika sadzatha kuziona.+ Iye adzakhala m’malo ouma a m’chipululu m’dziko la nthaka yamchere, kumene sikukhala anthu.+  Wodala ndi munthu aliyense amene amakhulupirira Yehova, amene amadalira Yehova.+  Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi. Kutentha kukadzafika iye sadzadziwa, koma masamba ake adzachuluka ndi kukhala obiriwira.+ Pa nthawi ya chilala+ sadzada nkhawa kapena kusiya kubala zipatso.  “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.*+ Ndani angaudziwe? 10  Ine Yehova ndimafufuza mtima+ ndi kusanthula impso.+ Munthu aliyense ndimamuchitira zinthu monga mwa zochita zake,+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+ 11  Munthu wopeza chuma mopanda chilungamo+ ali ngati nkhwali imene yasonkhanitsa mazira amene sinaikire. Chuma chakecho adzachisiya asanakwanitse ngakhale hafu ya zaka za moyo wake,+ ndipo pamapeto pake adzaonekera kuti ndi wopusa.”+ 12  Mpando waulemerero wa Mulungu ndi wokwezeka kuyambira pa chiyambi.+ Ndipo mpando umenewu ndiwo malo athu opatulika.+ 13  Inu Yehova, chiyembekezo cha Isiraeli,+ onse amene akukusiyani adzachita manyazi.+ Mayina a anthu onse okupandukirani+ adzalembedwa pafumbi chifukwa asiya Yehova magwero a madzi amoyo.+ 14  Ndichiritseni inu Yehova, ndipo ndidzachiradi.+ Ndipulumutseni ndipo ndidzapulumukadi,+ pakuti ine ndimatamanda inu.+ 15  Taonani! Ena akunena kuti: “N’chifukwa chiyani mawu a Yehova sanakwaniritsidwebe?+ Tsopanotu akwaniritsidwe.” 16  Koma ine sindinaleke kukutsatirani monga m’busa wanu. Ndipo sindinalakalake kuti tsiku loopsa lifike. Inu Mulungu, mukudziwa mawu otuluka pakamwa panga chifukwa ndinawalankhula pamaso panu. 17  Musakhale chinthu choopsa kwa ine.+ Inu ndinu pothawirapo panga pa tsiku la tsoka.+ 18  Anthu amene amandizunza achite manyazi+ koma musalole kuti ineyo ndichite manyazi.+ Anthuwo agwidwe ndi mantha aakulu koma musalole kuti ine ndigwidwe ndi mantha aakulu. Agwetsereni tsoka+ ndipo muwaphwanye kuwirikiza kawiri.+ 19  Yehova wandiuza kuti: “Pita ukaime pachipata cha ana a anthu pamene mafumu a Yuda amalowera ndi kutulukira. Kenako ukaimenso pazipata zina zonse za Yerusalemu.+ 20  Ndipo ukawauze kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova inu mafumu a Yuda ndi inu nonse okhala mu Yuda komanso inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumalowera pazipata izi.+ 21  Yehova wanena kuti: “Samalani moyo wanu.+ Katundu aliyense amene mukufuna kulowa naye pazipata za Yerusalemu musamunyamule pa tsiku la sabata.+ 22  Musatulutse katundu aliyense kuchokera m’nyumba zanu pa tsiku la sabata ndipo musamagwire ntchito iliyonse.+ Tsiku la sabata muziliona kukhala lopatulika monga mmene ndinalamulira makolo anu.+ 23  Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu+ moti anapitiriza kuumitsa khosi+ lawo kuti asamve ndi kulandira mwambo.”’*+ 24  “‘“Ndipo mukadzandimvera,”+ watero Yehova, “mwa kusalowa ndi katundu pazipata za mzindawu pa tsiku la sabata+ ndi kuona tsiku la sabata kukhala lopatulika mwa kusagwira ntchito iliyonse pa tsikuli,+ 25  pazipata za mzindawu padzalowa mafumu ndi akalonga+ okhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mafumuwo pamodzi ndi akalonga awo adzalowa atakwera magaleta ndi mahatchi. Adzalowa pamodzi ndi anthu a mu Yuda komanso anthu okhala mu Yerusalemu ndipo mumzindawu mudzakhala anthu mpaka kalekale. 26  Anthu adzabwera kuchokera m’mizinda ya Yuda, m’madera ozungulira Yerusalemu, m’dziko la Benjamini,+ kuchigwa,+ m’dera lamapiri+ komanso kuchokera kum’mwera.*+ Iwo adzabweretsa kunyumba ya Yehova nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe zina,+ nsembe zambewu,+ lubani*+ ndi nsembe zoyamikira.+ 27  “‘“Koma ngati simudzamvera mawu anga akuti muziona tsiku la sabata kukhala lopatulika ndi kuti musamanyamule katundu+ kulowa naye pazipata za Yerusalemu pa tsiku la sabata, ine ndidzatentha ndi moto zipata za mzindawu.+ Motowo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Yerusalemu+ ndipo sudzazimitsidwa.”’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndi wosowa pogwira,” ndi “woopsa.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “ku Negebu.”