Yeremiya 9:1-26

9  Ndikanakonda kuti m’mutu mwanga mukhale madzi ambiri ndiponso kuti maso anga akhale magwero a misozi.+ Pamenepo ndikanalira usana ndi usiku chifukwa cha anthu ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga.+  Ndikanakonda kukhala ndi malo a m’chipululu ogona anthu apaulendo.+ Pamenepo ndikanasiya anthu anga ndi kuwachokera, pakuti onsewo ndi achigololo,+ gulu la anthu ochita zachinyengo.+  Iwo amakunga lilime lawo ngati uta kuti aponye chinyengo,+ koma iwo si okhulupirika m’dzikoli. “Iwo anali kuchita zoipa motsatizanatsatizana ndipo anandinyalanyaza,”+ watero Yehova.  “Aliyense wa inu asamale ndi mnzake,+ ndipo musakhulupirire m’bale aliyense.+ Pakuti munthu aliyense amalanda malo a m’bale wake,+ ndipo munthu aliyense amakhala akuyendayenda kunenera mnzake miseche.+  Aliyense amapusitsa mnzake+ ndipo salankhula choonadi ngakhale pang’ono. Aphunzitsa lilime lawo kulankhula chinyengo.+ Iwo adzitopetsa okha ndi kuchita zinthu zoipa.+  “Iwe wakhala pakati pa chinyengo.+ Chifukwa cha chinyengo chawo akana kundidziwa ine,”+ watero Yehova.  Choncho, Yehova wa makamu wanena kuti: “Inetu ndikuwasungunula ndipo ndiyenera kuwasanthula.+ Nanga mwana wamkazi wa anthu anga ndingamuchitirenso zotani?+  Lilime lawo ndiwo muvi wophera anthu.+ Limalankhula chinyengo chokhachokha. Munthu aliyense amalankhula mwamtendere ndi mnzake, koma mumtima mwake amakonza chiwembu.”+  “Kodi sindiyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” watero Yehova. “Kapena kodi sindiyenera kubwezera mtundu woterewu?+ 10  Pakuti ndidzalirira mapiri mokweza ndi modandaula+ ndipo ndidzaimba nyimbo yoimba polira, pamene ndikulirira mabusa a m’chipululu. Ndidzalirira zimenezi chifukwa adzakhala atazitentha+ moti palibe munthu amene adzadutsamo. Anthu sadzamva kulira kwa ziweto+ m’mabusamo ndipo zolengedwa zouluka m’mlengalenga ngakhalenso nyama zidzakhala zitathawamo, zitachoka.+ 11  Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, malo opanda wokhalamo.+ 12  “Kodi wanzeru ndani kuti amvetse zimenezi, kapenanso ndani amene Yehova wamulankhula kuti anene zimenezi?+ N’chifukwa chiyani dzikoli lidzawonongedwa ndiponso kutenthedwa n’kukhala ngati chipululu chopanda munthu wodutsamo?”+ 13  Ndiyeno Yehova anayankha kuti: “Chifukwa chakuti iwo asiya chilamulo changa chimene ndinawapatsa kuti chizikhala pamaso pawo, komanso chifukwa chakuti iwo sanamvere mawu anga ndi kuwatsatira,+ 14  koma iwo anapitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndi kutsatira mafano a Baala,+ zinthu zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo.+ 15  Choncho Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndidzadyetsa anthu amenewa chitsamba chowawa,+ ndipo ndidzawamwetsa madzi apoizoni.+ 16  Ndidzawamwaza pakati pa mitundu ya anthu imene iwo kapena makolo awo sanaidziwe.+ Ndidzawakantha ndi lupanga kufikira nditawafafaniza.’+ 17  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chitani zinthu mozindikira anthu inu, ndipo itanani akazi oimba nyimbo zoimba polira kuti abwere.+ Tumizani anthu kuti akaitane akazi odziwa kulira maliro,+ 18  kuti abwere mofulumira ndi kudzatiimbira nyimbo zoimba polira. Maso athu atuluke misozi, madzi atuluke m’maso athu owala.+ 19  Pakuti ku Ziyoni kwamveka anthu akulira mofuula kuti:+ “Tafunkhidwa!+ Tachita manyazi kwambiri! Pakuti tasiya dziko lathu ndiponso chifukwa atigwetsera nyumba zathu.”+ 20  Koma tamverani mawu a Yehova akazi inu, ndipo mutchere khutu ku mawu otuluka m’kamwa mwake. Kenako muphunzitse ana anu aakazi kulira maliro+ ndipo mkazi aliyense aphunzitse mnzake nyimbo yoimba polira.+ 21  Pakuti imfa yatilowera m’nyumba kudzera m’mawindo. Yalowa munsanja zathu zokhalamo kuti mumsewu musapezeke mwana aliyense ndiponso kuti anyamata asapezeke m’mabwalo a mzinda.’+ 22  “Unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Mitembo ya anthu idzangoti mbwee panthaka ngati manyowa. Idzakhala ngati tirigu amene angomumweta kumene koma palibe munthu womusonkhanitsa pamodzi.”’”+ 23  Yehova wanena kuti: “Munthu wanzeru asadzitamande chifukwa cha nzeru zake.+ Munthu wamphamvu asadzitamande chifukwa cha mphamvu zake.+ Munthu wachuma asadzitamande chifukwa cha chuma chake.”+ 24  “Koma amene akudzitamanda adzitamande pa chifukwa chakuti, amamvetsa bwino+ njira zanga ndipo amandidziwa, kuti ine ndine Yehova,+ amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapereka ziweruzo ndi kuchita chilungamo padziko lapansi.+ Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa,”+ watero Yehova. 25  Yehova wanena kuti, “Taona masiku akubwera ndipo ndidzaimba mlandu aliyense wodulidwa koma amene sanachite mdulidwe wa mtima wake.+ 26  Ndidzaimba mlandu Iguputo,+ Yuda,+ Edomu,+ ana aamuna a Amoni+ ndi Mowabu+ ndi onse odulira ndevu zawo zam’mbali amene amakhala m’chipululu.+ Pakuti mitundu yonse ndi yosadulidwa ndipo anthu onse a m’nyumba ya Isiraeli sanachite mdulidwe wa mitima yawo.”+

Mawu a M'munsi