Yeremiya 15:1-21

15  Yehova anandiuza kuti: “Ngakhale Mose+ ndi Samueli+ akanaima pamaso panga, anthu awa sindikanawakomera mtima.+ Ndikanawapitikitsa pamaso panga kuti achoke.+  Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘Tichoke kupita kuti?’ ukayankhe kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Woyenera kufa ndi mliri afe ndi mliri! Woyenera kufa ndi lupanga afe ndi lupanga! Woyenera kufa ndi njala yaikulu afe ndi njala yaikulu!+ Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo atengedwe kupita ku ukapolo!”’+  “‘Ndidzawagwetsera masoka a mitundu inayi,’+ watero Yehova. ‘Ndidzawatumizira lupanga kuti liwaphe, agalu kuti akoke mitembo yawo, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga+ ndi zilombo zakutchire kuti ziwadye ndi kuwawononga.  Ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho,+ chifukwa cha zimene Manase, mwana wa Hezekiya, mfumu ya Yuda, anachita mu Yerusalemu.+  Ndani adzakusonyeza chifundo, iwe Yerusalemu? Ndani adzakumvera chisoni+ ndipo ndani adzapatuka ndi kufunsa za moyo wako?’  “‘Iwe wandisiya,’+ watero Yehova. ‘Ukundifulatira ndi kundichokera.+ Choncho nditambasula dzanja langa kuti ndikukanthe ndi kukuwononga.+ Ndatopa nako kukumvera chisoni.+  Ndipeta anthu anga ngati mbewu kuzipata za m’dzikoli. Ndithu, ndiwauluza ndi chifoloko.+ Ndiwaphera ana awo+ ndipo ndiwononga anthu anga chifukwa sanasiye kuchita zinthu zoipa.+  Akazi awo amasiye achuluka kwambiri pamaso panga kuposa mchenga wa kunyanja. Ndibweretsa wowononga kwa mayi ndi mnyamata, dzuwa lili paliwombo.+ Ndiwachititsa kugwidwa ndi mantha ndi kuwasokoneza mwadzidzidzi.+  Mkazi amene wabereka ana 7 wafooka ndipo akupuma movutikira.+ Kwa iye dzuwa lalowa masanasana,+ ndipo lachita manyazi ndi kuthedwa nzeru. Anthu otsala ndidzawapereka kwa adani awo kuti aphedwe ndi lupanga,’+ watero Yehova.” 10  Tsoka ine,+ chifukwa inu mayi anga munabereka ine munthu amene nthawi zonse ndimakangana ndipo ndimalimbana ndi dziko lonse.+ Sindinapereke ngongole komanso sanandikongoze kalikonse, koma anthu onse akunditemberera.+ 11  Yehova wanena kuti: “Ndithu, ndidzakuchitira zinthu zabwino+ ndipo ndidzakuthandiza kuti ndikupulumutse kwa adani ako pa nthawi ya tsoka+ ndi nthawi ya nsautso.+ 12  Kodi munthu angathe kuthyolathyola chitsulo, chitsulo cha kumpoto? Ndiponso kodi angathe kuthyolathyola mkuwa? 13  Ndidzapereka chuma chanu anthu inu ndi zinthu zanu zamtengo wapatali kwa wofunkha+ popanda malipiro. Ndidzatero chifukwa cha machimo anu onse amene munachita m’dziko lanu lonse.+ 14  Ndidzachititsa adani anu kutenga chumacho ndi kupita nacho kudziko limene simukulidziwa,+ pakuti mkwiyo wanga wayatsa moto.+ Ndithu, moto wakuyakirani anthu inu.” 15  Inu Yehova mukudziwa bwino mavuto anga.+ Ndikumbukireni+ ndipo mutembenuke ndi kundiyang’ana kuti mubwezere anthu ondizunza.+ Musandichotsere moyo wanga chifukwa chakuti simupsa mtima mwamsanga.+ Onani chitonzo chimene chili pa ine chifukwa cha dzina lanu.+ 16  Mawu anu anandipeza ndipo ndinawadya.+ Mawu anu amandikondweretsa+ ndi kusangalatsa mtima wanga,+ pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu,+ inu Yehova Mulungu wa makamu.+ 17  Sindinakhale pansi ndi gulu la anthu okonda kuchita nthabwala+ ndi kuyamba kusangalala nawo.+ Ndakhala pansi ndekhandekha chifukwa dzanja lanu lili pa ine,+ chifukwa mwandidzaza ndi mkwiyo.+ 18  N’chifukwa chiyani zopweteka zanga sizikutha+ ndiponso chilonda changa cha mkwapulo sichikupola?+ Chilondacho sichikumva mankhwala. Inu Mulungu, mwakhala ngati kasupe wosachedwa kuuma,+ ndiponso ngati mtsinje wosadalirika.+ 19  Chotero Yehova wanena kuti: “Ukabwerera kwa ine, inenso ndidzakukonda,+ ndipo udzanditumikira.+ Ukasiyanitsa zinthu zamtengo wapatali ndi zinthu zopanda phindu, udzakhala ngati kamwa langa. Anthuwo adzabwera kwa iwe, koma iwe sudzapita kwa iwo.” 20  “Ndakuchititsa kukhala ngati mpanda wamkuwa wolimba kwambiri kwa anthu awa.+ Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzakugonjetsa,+ pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa,”+ watero Yehova. 21  “Ndidzakulanditsa m’manja mwa anthu oipa+ ndipo ndidzakuwombola m’manja mwa anthu ankhanza.”

Mawu a M'munsi