Yeremiya 24:1-10
24 Ndiyeno Yehova anandisonyeza madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandisonyeza zimenezi Nebukadirezara mfumu ya Babulo atatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri+ ndi omanga makoma achitetezo kuchokera ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+
2 Nkhuyu zimene zinali m’dengu limodzi zinali zabwino kwambiri ngati nkhuyu zoyamba kucha.+ Koma nkhuyu zimene zinali m’dengu lina zinali zoipa kwambiri moti munthu sakanatha kuzidya chifukwa cha kuipa kwake.
3 Pamenepo Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Yeremiya?” Ndipo ine ndinayankha kuti: “Ndikuona nkhuyu. Nkhuyu zabwino n’zabwino kwambiri, ndipo nkhuyu zoipa n’zoipa kwambiri moti munthu sangadye chifukwa cha kuipa kwake.”+
4 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti:
5 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu otengedwa ku Yuda kupita ku ukapolo kudziko la Akasidi ndidzawaona ngati nkhuyu zabwino zimenezi. Ndidzawatumiza kudziko la Akasidi+ kuchoka m’dziko lino m’njira yabwino.+
6 Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino,+ ndipo ndidzawabwezeretsa kudziko lino.+ Pamenepo ndidzawalimbitsa, osati kuwapasula. Ndidzawabzala, osati kuwazula.+
7 Ndidzawapatsa mtima wodziwa kuti ine ndine Yehova.+ Iwo adzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo pakuti adzabwerera kwa ine ndi mtima wawo wonse.+
8 “‘Chotero mofanana ndi nkhuyu zoipa zija zimene munthu sangadye chifukwa cha kuipa kwake,+ Yehova wanena kuti: “Momwemonso ndidzapereka Zedekiya+ mfumu ya Yuda, akalonga ake ndi anthu onse opulumuka mu Yerusalemu amene atsalira m’dzikoli,+ komanso anthu okhala m’dziko la Iguputo.+
9 Ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho, chifukwa cha masoka aakulu amene ndidzawagwetsera.+ Anthu a mitundu ina adzawatonza, kuwayesa chosereula, kuwanyoza+ ndipo adzakhala otembereredwa+ kulikonse kumene ndidzawabalalitsirako.+
10 Ndidzawatumizira lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri,+ kufikira adzatheratu m’dziko limene ndinawapatsa, iwowo ndi makolo awo.”’”+