Yeremiya 8:1-22
8 “Pa nthawi imeneyo,” watero Yehova, “anthu adzatulutsa m’manda mafupa a mafumu a Yuda, a akalonga awo, a ansembe, a aneneri ndi a anthu amene anali mu Yerusalemu.+
2 Mafupawo adzawamwaza poyera ndipo dzuwa, mwezi, ndi makamu onse akumwamba zidzawala pa iwo. Zinthu zimenezi ndi zimene iwo anali kuzikonda, kuzitumikira, kuzitsatira,+ kuzipembedza, ndi kuziweramira.+ Mafupawo sadzasonkhanitsidwa pamodzi kapena kuikidwa m’manda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.”+
3 “Onse otsala a banja loipali, kulikonse kumene ndidzawabalalitsira,+ adzaona kuti ndi bwino kufa kusiyana ndi kukhala moyo,”+ watero Yehova wa makamu.
4 “Ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi iwo adzagwa osadzukanso?+ Kodi mmodzi akabwerera, winanso sangabwerere?+
5 N’chifukwa chiyani anthu a mu Yerusalemu ali osakhulupirika ndipo akhalabe osakhulupirika kwa nthawi yaitali chonchi? Iwo akupitiriza kuchita zachinyengo+ ndipo akana kubwerera.+
6 Ine ndinali tcheru+ ndipo ndinali kuwamvetsera.+ Zimene iwo anali kunena sizinali zoona. Panalibe munthu wolapa zoipa zimene anachita,+ amene ananena kuti, ‘Kodi ndachitiranji zimenezi?’ Aliyense akubwerera kunjira imene anthu ambiri akuitsatira,+ ngati hatchi imene ikuthamangira kunkhondo.
7 Ngakhale dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu.+ Ndipo njiwa,+ namzeze* ndi pumbwa,* iliyonse mwa mbalame zimenezi imadziwa nyengo yobwerera kumene yachokera. Koma anthu anga sakudziwa chiweruzo cha Yehova.”’+
8 “‘Anthu inu munganene bwanji kuti: “Ndife anzeru, ndipo tili ndi chilamulo cha Yehova”?+ Ndithudi, zolembera zachinyengo+ za alembi zagwiritsidwa ntchito mwachinyengo.
9 Anthu anzeru achita manyazi.+ Achita mantha ndipo adzagwidwa. Taonani! Iwo akana mawu a Yehova. Kodi ali ndi nzeru yotani tsopano?+
10 Choncho akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena, ndipo minda yawo ndidzaipereka kwa anthu ena.+ Pakuti kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu aliyense wa iwo akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+
11 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa mwana wamkazi wa anthu anga ponena kuti: “Kuli mtendere! Kuli mtendere!” pamene kulibe mtendere.+
12 Kodi iwo anachita manyazi chifukwa anachita zinthu zonyansa?+ Iwo sanachite manyazi ngakhale pang’ono, komanso sanali kudziwa n’komwe kuchita manyazi.+
“‘Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa. Pa nthawi yowalanga+ adzapunthwa,’ watero Yehova.+
13 “‘Pokolola ndidzawafafaniza,’ watero Yehova.+ ‘Mumtengo wa mpesa simudzapezeka mphesa,+ mumtengo wa mkuyu simudzapezeka nkhuyu, ndipo masamba adzafota. Zinthu zimene ndimawapatsa zidzawadutsa.’”
14 “N’chifukwa chiyani tikungokhala? Sonkhanani pamodzi, ndipo tiyeni tilowe m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ kuti tikafere kumeneko. Pakuti Yehova Mulungu wathu watiweruza kuti tife,+ ndipo akutipatsa madzi apoizoni kuti timwe+ chifukwa tachimwira Yehova.
15 Tinali kuyembekezera mtendere, koma panalibe chabwino chilichonse.+ Tinali kuyembekezera kuchiritsidwa, koma m’malomwake tinali kuona zinthu zochititsa mantha.+
16 Mahatchi ake akumveka kupuma mwawefuwefu ali ku Dani.+ Dziko lonse layamba kugwedezeka chifukwa cha phokoso la kulira kwa mahatchi ake amphongo.+ Adani akubwera kudzawononga dziko ndi zonse zokhala mmenemo, mzinda ndi onse okhala mmenemo.”
17 “Inetu ndikutumiza njoka pakati panu, njoka zapoizoni,+ zimene simungaziimbire nyimbo kuti muziseweretse,+ ndipo zidzakulumani ndithu,” watero Yehova.
18 Ndagwidwa ndi chisoni chosatha.+ Mtima wanga wadwala.
19 Pakumveka mawu olirira thandizo a mwana wamkazi wa anthu anga ali kudziko lakutali.+ Iye akuti: “Kodi Yehova sali mu Ziyoni?+ Kapena kodi mfumu ya Yerusalemu mulibe mmenemo?”+
“N’chifukwa chiyani andikhumudwitsa ndi mafano awo ogoba, ndiponso milungu yawo yachilendo yopanda pake?”+
20 “Nthawi yokolola yadutsa, ndipo nyengo ya chilimwe yatha. Koma ife sitinapulumutsidwe!”+
21 Ndasweka mtima+ chifukwa cha kuwonongeka+ kwa mwana wamkazi wa anthu anga. Ndine wachisoni. Ndadabwa kwambiri.+
22 Kodi mu Giliyadi+ mulibe mafuta a basamu? Kapena kodi mulibe wochiritsa mmenemo?+ N’chifukwa chiyani nanga mwana wamkazi wa anthu anga sakuchira?+
Mawu a M'munsi
^ Mbalame imeneyi ena amati “nyapwere.”
^ Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”