Yeremiya 11:1-23

11  Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa:  “Imvani mawu a pangano langa, anthu inu! “Anthu a ku Yuda komanso okhala mu Yerusalemu ukawauze+ mawu amenewa.  Ukanene kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Munthu aliyense wosamvera mawu a m’pangano limeneli ndi wotembereredwa.+  Makolo anu ndinawalamula kumvera mawu amenewa pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo,+ pamene ndinali kuwatulutsa m’ng’anjo yachitsulo.+ Ndinawalamula kuti, ‘Muzimvera mawu anga, ndipo muzichita zinthu motsatira malamulo onse amene ndakupatsani.+ Mukatero mudzakhaladi anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu,+  kuti ndikwaniritse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu+ kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ monga mmene zilili lero.’”’” Pamenepo ine ndinayankha kuti: “Zikhale momwemo,* inu Yehova.”  Yehova anapitiriza kundiuza kuti: “Lalikira mawu onsewa m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu+ kuti, ‘Anthu inu, imvani mawu a pangano langa, ndipo muchite zimene akunena.+  Inetu ndinalangiza makolo anu pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo+ ndipo ndikupitiriza kutero. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwalangiza kuti: “Muzimvera mawu anga.”+  Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu.+ M’malomwake aliyense wa iwo anapitiriza kuumitsa mtima wake woipawo.+ Choncho ndinawalanga mogwirizana ndi mawu onse amene ndinanena m’pangano langa, amene ndinawalamula kuti awasunge, koma sanawasunge.’”  Yehova anandiuzanso kuti: “Zadziwika kuti anthu a mu Yuda komanso okhala mu Yerusalemu akukonza chiwembu chondipandukira.+ 10  Iwo abwerera ku zolakwa zimene makolo awo+ anachita kalekale. Makolowo anakana kumvera mawu anga, m’malomwake anayamba kutsatira milungu ina kuti aitumikire.+ A m’nyumba ya Isiraeli ndi a m’nyumba ya Yuda aphwanya pangano langa limene ndinachita ndi makolo awo.+ 11  Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndiwagwetsera tsoka+ limene sadzatha kulithawa.+ Iwo adzandiitana kuti ndiwathandize, koma sindidzawamvera.+ 12  Ndipo mizinda ya Yuda komanso anthu okhala mu Yerusalemu adzapita kukapempha thandizo kwa milungu imene akuifukizira nsembe zautsi.+ Koma milungu imeneyo sidzawapulumutsa pa nthawi ya tsoka lawo.+ 13  Pakuti milungu yako, iwe Yuda,+ yafanana ndi mizinda yako kuchuluka kwake. Ndipo chinthu chochititsa manyazi+ mwachimangira maguwa ansembe, anthu inu. Mwachimangira maguwa ansembe ochuluka mofanana ndi misewu ya mu Yerusalemu. Mwamanga maguwa ansembe kuti muzifukizira Baala nsembe zautsi.’+ 14  “Tsopano iwe, usawapempherere anthu awa, ndipo usawalirire kwa ine mochonderera. Usawaperekere pemphero,+ chifukwa ine sindidzamvetsera pamene iwo akundiitana chifukwa cha tsoka limene lawagwera.+ 15  “Kodi anthu anga okondedwa akufuna chiyani m’nyumba yanga+ pamene ambiri a iwo akuchita zoipa zoterezi?+ Kodi nyama yopatulika imene amaipereka nsembe idzawapulumutsa tsoka lawo likadzafika?+ Kodi iwo adzakondwera pa nthawi imeneyo?+ 16  Yehova wakutchulani dzina+ lakuti, ‘Mtengo waukulu wa maolivi wa masamba ambiri obiriwira, wokongola, wobala zipatso komanso wooneka bwino.’ Koma pali phokoso lamphamvu ndipo mtengowo auyatsa moto, komanso adani athyola nthambi zake.+ 17  “Yehova wa makamu, Wokubzalani,+ wanena kuti tsoka lidzakugwerani chifukwa cha zoipa zimene a m’nyumba ya Isiraeli+ ndi a m’nyumba ya Yuda achita ndi kundikhumudwitsa nazo pofukizira Baala nsembe zautsi.”+ 18  Yehova wandidziwitsa. Pa nthawiyo, inu Mulungu, munandionetsa zochita zawo.+ 19  Ndipo ine ndinali ngati mwana wa nkhosa wamphongo wokondedwa mwapadera, amene akupita kukaphedwa.+ Ine sindinadziwe kuti andikonzera ziwembu+ ndi kunena kuti: “Tiyeni tiwononge mtengowu pamodzi ndi zipatso zake. Tiyeni timuchotse m’dziko la anthu amoyo,+ kuti dzina lake lisakumbukikenso.” 20  Koma Yehova wa makamu amaweruza mwachilungamo.+ Amafufuza impso ndi mtima.+ Inu Mulungu, ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango, pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+ 21  Choncho Yehova wanena motsutsana ndi anthu a ku Anatoti+ amene akufuna moyo wako, ndipo akunena kuti: “Usanenere m’dzina la Yehova,+ ngati ukufuna kuti tisakuphe.” 22  Yehova wa makamu wanena kuti: “Tsopano ndikuwapatsa chilango. Anyamata adzafa ndi lupanga.+ Ana awo aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala yaikulu.+ 23  Ndipo sipadzapezeka wotsala pakati pawo, chifukwa ndidzadzetsa tsoka pa anthu a ku Anatoti,+ m’chaka chimene ndidzawapatsa chilango.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.