Yeremiya 13:1-27
13 Yehova wandiuza kuti: “Pita ukatenge lamba wansalu ndipo ukamumange m’chiuno mwako, koma asakakhudze madzi.”
2 Choncho ndinapita kukatenga lambayo mogwirizana ndi mawu a Yehova ndipo ndinamumanga m’chiuno mwanga.
3 Ndiyeno Yehova analankhulanso nane kachiwiri kuti:
4 “Tenga lamba wabweretsayo amene wamumanga m’chiuno ndipo upite kumtsinje wa Firate.+ Kumeneko ukabise lambayo mumng’alu wa m’phanga.”
5 Pamenepo ndinanyamuka ndi kukabisa lambayo pafupi ndi mtsinje wa Firate monga mmene Yehova anandilamulira.
6 Ndiyeno patapita masiku ambiri Yehova anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kumtsinje wa Firate ndipo ukatenge lamba amene ndinakulamula kuti ukabise kumeneko.”
7 Choncho ndinapita kumtsinje wa Firate ndipo ndinakumba pamalo amene ndinabisapo lambayo ndi kumutenga. Koma nditamuona, anali atawonongeka moti sakanagwiranso ntchito iliyonse.
8 Pamenepo Yehova anandiuzanso kuti:
9 “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi lamba ameneyu, ndidzawononga kunyada kwa Yuda+ ndiponso kunyada kwakukulu kwa Yerusalemu.
10 Anthu oipa amenewa akukana kumvera mawu anga.+ Iwo akupitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndipo akutsatira milungu ina kuti aitumikire ndi kuigwadira.+ Anthu amenewa adzakhala ngati lamba ameneyu amene sangagwirenso ntchito iliyonse.’
11 ‘Ine ndinachititsa nyumba yonse ya Isiraeli ndi nyumba yonse ya Yuda kundimamatira+ mofanana ndi mmene lamba amagwirira m’chiuno mwa munthu,’ watero Yehova. ‘Ndinachita zimenezi kuti iwo akhale anthu anga,+ akhale dzina langa lotchuka,+ anditamande ndi kukhala chinthu changa chokongola. Koma iwo sanandimvere.’+
12 “Tsopano uwauze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Mtsuko uliwonse waukulu amadzazamo vinyo.”’+ Ukakawauza zimenezi, iwo adzakufunsa kuti, ‘Kodi ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse waukulu amadzazamo vinyo?’
13 Pamenepo ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikuledzeretsa+ anthu onse a m’dzikoli, mafumu amene akukhala pampando wa Davide,+ ansembe, aneneri ndi onse okhala mu Yerusalemu.
14 Ndipo ndidzawombanitsa munthu ndi mnzake, abambo ndi ana awo pa nthawi imodzi,”+ watero Yehova. “Sindidzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni. Ndithu sindidzakhala ndi chifundo choti ndisawawononge.”’+
15 “Tamverani anthu inu. Tcherani khutu. Musadzikweze+ pakuti Yehova ndi amene wanena zimenezi.+
16 Patsani Yehova Mulungu wanu ulemerero+ asanachititse mdima,+ komanso mapazi anu asanapunthwe pamapiri madzulo dzuwa litalowa.+ Mudzayembekeza kuwala+ koma iye adzabweretsa mdima,+ ndipo adzachititsa mdima wandiweyani.+
17 Ndipo ngati simudzamvera mawu ake+ ndidzalira ndi kugwetsa misozi m’malo obisika chifukwa cha kunyada kwanu. Maso anga adzatulutsa misozi+ chifukwa chakuti nkhosa+ za Yehova zidzakhala zitagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.
18 “Uza mfumu ndi mayi a mfumu+ kuti, ‘Khalani pamalo apansi,+ pakuti chisoti chanu chaulemerero chidzachotsedwa pamutu panu ndi kuikidwa pansi.’+
19 Mizinda ya kum’mwera yatsekedwa moti palibe amene akuitsegula. Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo. Watengedwa wathunthu kupita ku ukapolo.+
20 “Kweza maso ako kuti uone anthu amene akubwera kuchokera kumpoto.+ Kodi nkhosa zimene anakupatsa, nkhosa zako zokongolazo zili kuti?+
21 Kodi udzanenanji wina akadzatembenukira kwa iwe+ ngakhale kuti iweyo unamuchititsa kukhala bwenzi lako lapamtima, limene unali kukondana nalo kwambiri kuyambira pa chiyambi?+ Kodi zowawa za pobereka ngati za mkazi amene akubereka mwana sizidzakugwira?+
22 Ukadzanena mumtima mwako kuti,+ ‘N’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zandigwera?’+ pamenepo udzadziwe kuti wavulidwa siketi yako+ ndipo zidendene zako zazunzidwa chifukwa zolakwa zako zachuluka.
23 “Kodi Mkusi*+ angasinthe khungu lake, kapena kodi kambuku angasinthe mawanga ake?+ Ngati angathe kuchita zimenezi, ndiye kuti inunso amene munaphunzitsidwa kuchita zinthu zoipa mungathe kuchita zinthu zabwino.+
24 Choncho ndidzakumwazani+ ngati mapesi amene akuuluka ndi mphepo kuchokera m’chipululu.+
25 Limeneli ndilo gawo lako, malo ako amene ndakuyezera,”+ watero Yehova, “chifukwa chakuti wandiiwala+ ndipo ukupitirizabe kukhulupirira zinthu zachinyengo.+
26 Ndidzakuvula siketi yako ndi kukuphimba nayo kumaso, moti udzachita manyazi.+
27 Chigololo chako,+ kumemesa* kwako,+ khalidwe lako lotayirira la uhule, zonsezi zidzaonekera. Ndaona zinthu zako zonyansa pamapiri kuthengo.+ Tsoka kwa iwe Yerusalemu! Sungakhale woyera.+ Kodi udzakhalabe wosayera kufikira liti?”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “Mwitiyopiya.”
^ Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.