Yeremiya 27:1-22

27  Kuchiyambi kwa ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya,+ mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti akanene mawu akuti:  “Yehova wandiuza kuti, ‘Upange zomangira ndiponso magoli,+ ndipo uzivale m’khosi mwako.+  Kenako, uzitumize kwa mfumu ya Edomu,+ mfumu ya Mowabu,+ mfumu ya ana a Amoni,+ mfumu ya Turo+ ndi mfumu ya Sidoni.+ Upatsire amithenga amene akubwera ku Yerusalemu kudzaonana ndi Zedekiya mfumu ya Yuda.  Ukatero, uwalamule kuti akauze ambuye awo kuti: “‘“Mukauze ambuye anu kuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli,+ wanena kuti,  ‘Ine ndinapanga dziko lapansi,+ anthu+ ndi nyama+ zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu+ ndiponso dzanja langa lotambasula.+ Ndipo dzikoli ndalipereka kwa amene ndikufuna.+  Tsopano ndapereka mayiko onsewa m’manja mwa mtumiki wanga+ Nebukadinezara, mfumu ya Babulo.+ Ndamupatsanso nyama zakutchire kuti zimutumikire.+  Choncho mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo,+ mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pamenepo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamugwiritsa ntchito ngati wantchito wawo.’+  “‘“‘Ndiyeno mtundu uliwonse wa anthu ndi ufumu umene sudzatumikira Nebukadinezara mfumu ya Babulo, umenenso sudzaika khosi lake m’goli la mfumu ya Babulo, ine ndidzaulanga ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri+ kufikira nditaufafaniza kudzera mwa Nebukadinezara,’+ watero Yehova.  “‘“‘Anthu inu musamvere aneneri,+ ochita zamaula, olota maloto,+ ochita zamatsenga ndi obwebweta+ amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Anthu inu simudzatumikira mfumu ya Babulo.”+ 10  Pakuti anthu amenewa akulosera monama kwa inu. Ndipo mukawamvera mudzatengedwa kuchoka m’dziko lanu kupita kudziko lakutali. Ine ndidzakubalalitsani ndipo inu mudzatheratu.+ 11  “‘“‘Mtundu wa anthu umene udzaika khosi lake m’goli la mfumu ya Babulo ndi kuitumikira, ndidzauchititsa kukhala mwamtendere m’dziko lawo, ndipo adzalima minda ndi kukhalabe m’dzikomo,’ watero Yehova.”’”+ 12  Zedekiya+ mfumu ya Yuda ndinamuuza mawu onsewa+ kuti: “Ikani makosi anu m’goli la mfumu ya Babulo ndi kuitumikira. Mutumikire mfumuyo ndi anthu ake, kuti mukhalebe ndi moyo.+ 13  Kodi iweyo ndi anthu ako muferenji ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri?+ Izi ndi zimene Yehova wanena kuti zidzachitikira mtundu umene sukutumikira mfumu ya Babulo. 14  Anthu inu musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zonama.+ 15  “‘Ine sindinawatume,’ watero Yehova, ‘koma iwo akulosera m’dzina langa monama, ndipo mukawamvera ndidzakubalalitsani.+ Inu pamodzi ndi aneneri amene akulosera kwa inuwo mudzatha.’”+ 16  Ndiyeno ndinalankhula ndi ansembe ndi anthu ena onsewa kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Musamvere mawu a aneneri anu amene akulosera kwa inu kuti: “Taonani! Ziwiya za m’nyumba ya Yehova zibwezedwa kuchokera ku Babulo posachedwapa!”+ Pakuti iwo akulosera kwa inu monama.+ 17  Musawamvere. Tumikirani mfumu ya Babulo kuti mukhale ndi moyo.+ Kodi mzinda uwu ukhale bwinja chifukwa chiyani?+ 18  Koma ngati iwo ndi aneneri, ndipo Yehova wawauza mawu, iwo achonderere kwa Yehova wa makamu+ kuti ziwiya zimene zinatsala m’nyumba ya Yehova, m’nyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babulo.’ 19  “Yehova wa makamu wanena mawu okhudza zipilala,+ thanki ya madzi,*+ zotengera zamawilo+ ndi ziwiya zotsala mumzinda uwu,+ 20  zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anasiya pamene anatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, pamodzi ndi olemekezeka onse a Yuda ndi Yerusalemu, kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu.+ 21  Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza ziwiya zimene zinatsala m’nyumba ya Yehova, m’nyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu+ kuti, 22  ‘“Ziwiya zimenezi zidzapita ku Babulo+ ndipo zidzakhala kumeneko kufikira ine nditazikumbukira,”+ watero Yehova. “Ndipo ndidzazibweretsa ndi kuzibwezeretsa pamalo ano.”’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “nyanja.”