Yeremiya 33:1-26
33 Yeremiya atamutsekera m’Bwalo la Alonda,+ Yehova analankhula naye kachiwiri kuti:
2 “Yehova Wopanga+ dziko lapansi, Yehova Woumba+ dzikoli ndi kulikhazikitsa.+ Mulungu amene dzina lake ndi Yehova,+ wanena kuti,
3 ‘Mundiitane ndipo ndidzakuyankhani.+ Nthawi yomweyo ndidzakuuzani zinthu zazikulu ndi zovuta kuzimvetsa zimene simukuzidziwa.’”+
4 “Pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza nyumba za mumzinda uwu ndiponso okhudza nyumba za mafumu a Yuda zimene zagwetsedwa podziteteza ku ziunda zomenyerapo nkhondo ndiponso ku lupanga la adani.+
5 Wanenanso mawu okhudza amuna amene akubwera kudzamenyana ndi Akasidi, ndiponso okhudza malo amene adzaza ndi mitembo ya amuna amene wawapha chifukwa cha mkwiyo wake waukulu,+ amenenso ali oipa kwambiri moti iye wausiya mzindawu chifukwa cha kuipa kwa anthu amenewo.+
6 Iye wanena kuti: ‘Ine ndichiritsa anthu a mumzindawu ndi kuwapatsa thanzi labwino.+ Ndiwachiritsa ndi kuwapatsa mtendere wochuluka ndi choonadi.+
7 Ndibwezeretsa anthu a mu Yuda ndi a mu Isiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndipo ndiwalimbitsa kuti akhale ngati mmene analili poyamba.+
8 Ndiwayeretsa ku zolakwa zawo zonse zimene anachimwa nazo pamaso panga,+ ndipo ndiwakhululukira zolakwa zawo zonse zimene anandichimwira nazo ndi kuphwanya nazo malamulo anga.+
9 Mzindawu udzakhala ndi dzina limene lidzandikondweretsa,+ dzina lochititsa kuti nditamandidwe ndi kulandira ulemerero pakati pa mitundu yonse ya padziko lapansi imene idzamva za zinthu zabwino zimene ndikuwachitira.+ Anthu a mitundu inawo adzachita mantha+ ndi kunjenjemera+ chifukwa cha zinthu zabwino ndi mtendere wonse umene ndikubweretsa pamzindawu.’”+
10 “Yehova wanena kuti, ‘Anthu inu mudzanena za dziko lino kuti ndi lopanda pake chifukwa mulibe anthu ndi ziweto. Mudzanena zimenezi za mizinda ya Yuda ndi misewu ya Yerusalemu imene yawonongeka,+ moti mulibe anthu ndipo simukukhala munthu aliyense ngakhale ziweto.+
11 M’malo amenewa mudzamveka mawu achikondwerero ndi achisangalalo.+ Mudzamveka mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi, ndi mawu a anthu onena kuti: “Tamandani Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndi wabwino.+ Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale!”’+
“‘Anthuwo azidzabweretsa nsembe yoyamikira kunyumba ya Yehova,+ pakuti ndidzabwezeretsa anthu a m’dzikoli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina kuti akhalenso ngati mmene analili poyamba,’+ watero Yehova.”
12 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘M’dziko lino lopanda pake, lopanda anthu ndi lopanda ziweto+ ndi mizinda yake yonse, mudzakhala malo odyetserako ziweto kumene abusa adzalola ziweto zawo kugona pansi.’+
13 “Yehova wanena kuti, ‘Ziweto zidzadutsa pansi pa dzanja la munthu woziwerenga+ m’mizinda ya m’madera amapiri, m’mizinda ya m’chigwa,+ m’mizinda ya kum’mwera,+ m’dziko la Benjamini,+ m’madera ozungulira Yerusalemu+ ndi m’mizinda ya Yuda.’”+
14 “‘Taonani! Masiku adzafika+ pamene ndidzakwaniritsa lonjezo langa+ lokhudza nyumba ya Isiraeli+ ndi nyumba ya Yuda,’ watero Yehova.
15 M’masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira yolungama+ ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo m’dzikoli.+
16 M’masiku amenewo, Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.+ Yerusalemu adzatchedwa kuti, Yehova Ndiye Chilungamo Chathu.’”+
17 “Yehova wanena kuti, ‘M’nyumba ya Davide simudzasowa munthu wokhala pampando wachifumu wa nyumba ya Isiraeli.+
18 Ndipo ponena za ansembe achilevi, pakati pawo sindidzasowa mwamuna wopereka nsembe zopsereza zathunthu, nsembe yambewu yofukiza komanso nsembe zina nthawi zonse.’”+
19 Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti:
20 “Yehova wanena kuti, ‘Ngati anthu inu mungathe kuphwanya pangano langa loti kukhale usana ndi pangano langa loti kukhale usiku, kuti usana ndi usiku zisafike pa nthawi yake,+
21 ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga+ kuti asakhale ndi mwana woti adzalamulire monga mfumu pampando wachifumu wa Davide.+ Ndingachitenso chimodzimodzi ndi atumiki anga, ansembe achilevi.+
22 Ine ndidzachulukitsa mbewu ya Davide mtumiki wanga ndi Alevi amene akunditumikira.+ Ndidzawachulukitsa mofanana ndi makamu akumwamba amene sangathe kuwerengedwa ndiponso mofanana ndi mchenga umene munthu sangathe kuuyeza.’”+
23 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Yeremiya kuti:
24 “Kodi sunamve zimene ena mwa anthu awa akunena kuti, ‘Mabanja awiri amene Yehova wasankha,+ adzawakananso’? Adani akuchitira anthu anga zachipongwe+ ndipo sakuwaonanso ngati mtundu wa anthu.
25 “Yehova wanena kuti, ‘Monga momwedi ndinakhazikitsira pangano langa loti kukhale usana ndi usiku,+ malamulo anga akumwamba ndi dziko lapansi,+
26 momwemonso sindidzakana mbewu ya Yakobo ndi mbewu ya Davide mtumiki wanga,+ kuti pakati pa mbewu yake nditengepo olamulira mbewu ya Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Pakuti ndidzasonkhanitsa onse amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina+ ndipo ndidzawamvera chisoni.’”+