Yeremiya 51:1-64

51  Yehova wanena kuti: “Babulo+ pamodzi ndi anthu okhala ku Lebi-kamai ndikuwautsira chimphepo chowononga.+  Ine ndidzatumiza anthu opeta ku Babulo kuti akamupete ndi kusiya dziko lake lili lopanda kanthu.+ Pa tsiku la tsoka lake, anthuwo adzamuukira kuchokera kumbali zonse.+  “Munthu wodziwa kukunga uta musamulole kuchita zimenezo.+ Musamulole kunyamuka kuti amenye nkhondo atavala chovala chamamba achitsulo. “Anthu inu musamvere chisoni anyamata ake.+ Wonongani gulu lake lonse la asilikali.+  Muwaphe ndi kusiya mitembo yawo ili paliponse m’dziko la Akasidi.+ Muwasiye mutawabaya m’misewu ya m’dzikolo.+  “Pakuti Mulungu, Yehova wa makamu,+ sanasiye Isiraeli ndi Yuda+ kuti akhale mkazi wamasiye. Dziko la Akasidi lili ndi mlandu waukulu pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+  “Thawani ndi kutuluka m’Babulo+ ndipo aliyense apulumutse moyo wake.+ Musawonongeke chifukwa cha zolakwa zake.+ Ino ndi nthawi yoti Yehova amubwezere chilango.+ Mulungu abwezera Babulo mogwirizana ndi zochita zake.+  Babulo wakhala kapu yagolide m’dzanja la Yehova+ ndipo waledzeretsa dziko lonse lapansi.+ Mitundu ya anthu yaledzera ndi vinyo wake.+ N’chifukwa chake mitundu ya anthu ikuchita zinthu zamisala.+  Babulo wagwa mwadzidzidzi moti wasweka.+ Mulireni mofuula anthu inu.+ M’patseni mafuta a basamu kuti muthetse ululu wake,+ mwina achira.”  “Tinafuna kuchiritsa Babulo, koma iye sanachiritsike. Tiyeni timusiye anthu inu+ ndipo aliyense wa ife apite kudziko lakwawo.+ Pakuti chiweruzo chake chafika kumwamba ndipo chakwera kufika m’mitambo.+ 10  Yehova watichitira zinthu zachilungamo.+ Bwerani kuti tisimbe ntchito za Yehova Mulungu wathu mu Ziyoni.”+ 11  “Nolani mivi yanu.+ Dzitetezeni ndi zishango zozungulira, amuna inu. Yehova wautsa mitima ya mafumu a Amedi,+ chifukwa akufuna kulanga Babulo ndi kumuwononga.+ Yehova akufuna kubwezera Babulo chilango chifukwa cha kachisi wake.+ 12  Kwezerani mpanda wa Babulo mtengo wa chizindikiro.+ Wonjezerani alonda+ ndipo ikani alondawo pamalo awo. Konzekeretsani omenya nkhondo mobisalira anzawo.+ Pakuti Yehova waganiza zoti achite ndipo adzachitira anthu okhala ku Babulo zimene wanena.”+ 13  “Iwe mkazi wokhala pamadzi ambiri,+ wokhala ndi chuma chochuluka,+ mapeto ako afika ndipo nthawi yako+ yoti uzipanga phindu yatha.+ 14  Yehova wa makamu walumbira m’dzina lake+ kuti, ‘M’dziko lako ndidzadzazamo amuna ngati dzombe+ ndipo amunawo adzaimba mokondwa chifukwa chokugonjetsa.’+ 15  Mulungu woona ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake,+ amene mwanzeru+ zake anakhazikitsa dziko+ limene anthu amakhalamo. Iye ndi amenenso anayala kumwamba mwa kuzindikira kwake.+ 16  Mawu ake amapangitsa madzi akumwamba kuchita mkokomo, ndipo amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Iye wapanganso zipata zotulukirapo mvula+ ndipo amatulutsa mphepo yamkuntho m’nkhokwe zake. 17  Munthu aliyense wachita zinthu mopanda nzeru kwambiri moti ndi zoonekeratu kuti sakudziwa kalikonse.+ Mmisiri aliyense wa zitsulo adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+ Pakuti chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonama+ ndipo mafano amenewa alibe moyo.+ 18  Iwo ndi achabechabe,+ ntchito yoyenera kutonzedwa.+ Mulungu akadzatembenukira kwa iwo, adzawawononga.+ 19  “Koma Mulungu wa Yakobo sali ngati mafanowa.+ Iye ndi amene anapanga china chilichonse.+ Mulungu ameneyu ndiye ndodo ya cholowa chake+ ndipo dzina lake ndi Yehova wa makamu.”+ 20  “Iwe ndiwe chibonga changa, zida zanga zankhondo.+ Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mitundu ya anthu kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzawononga maufumu. 21  Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya hatchi ndi wokwerapo wake kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya magaleta* ankhondo ndi okweramo ake kukhala zidutswazidutswa.+ 22  Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mwamuna ndi mkazi kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mwamuna wachikulire ndi kamnyamata kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mnyamata ndi namwali kukhala zidutswazidutswa. 23  Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya m’busa ndi gulu lake la ziweto kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya mlimi ndi ziweto zake zolimira kukhala zidutswazidutswa. Kudzera mwa iwe ndidzaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri kukhala zidutswazidutswa. 24  Ndidzabwezera Babulo ndi anthu onse okhala m’dziko la Kasidi zoipa zonse zimene anachita ku Ziyoni anthu inu mukuona,”+ watero Yehova. 25  “Ine ndikuthira nkhondo iwe+ phiri lowononga,+ amene wawononga dziko lonse lapansi.+ Ndidzatambasula dzanja langa ndi kukuthira nkhondo. Ndidzakugubuduza kukuchotsa pamatanthwe ndipo ndidzakusandutsa phiri lotenthedwa ndi moto,” watero Yehova.+ 26  “Anthu sadzatenga mwala kuchokera kwa iwe kuti ukakhale mwala wapakona kapena mwala wapamaziko+ chifukwa udzakhala mabwinja mpaka kalekale,”+ watero Yehova. 27  “Kwezani mtengo wa chizindikiro amuna inu.+ Imbani lipenga pakati pa mitundu ya anthu. Konzekeretsani+ mitundu ya anthu yoti imuthire nkhondo. Muitanireni maufumu a ku Ararati,+ ku Mini ndi ku Asikenazi.+ Muikireni wolemba anthu usilikali. Mubweretsereni mahatchi+ ngati dzombe lokhala ndi ubweya. 28  Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo, mafumu a ku Mediya,+ abwanamkubwa ake, atsogoleri ake onse ndi madera onse olamulidwa ndi aliyense wa amenewa. 29  Dziko ligwedezeke ndi kumva ululu waukulu,+ chifukwa Yehova waganiza zokhaulitsa Babulo kuti dzikolo likhale chinthu chodabwitsa, lopanda munthu wokhalamo.+ 30  “Amuna amphamvu a ku Babulo asiya kumenya nkhondo. Iwo angokhala m’malo otetezeka. Mphamvu zawo zatha.+ Akhala ngati akazi.+ Nyumba za m’Babulo zatenthedwa. Mipiringidzo yake yathyoledwa.+ 31  “Munthu mmodzi wothamanga wakumana ndi mnzake, ndipo mthenga mmodzi wakumana ndi mnzake,+ onsewa akukanena kwa mfumu ya Babulo kuti mzinda wake walandidwa kumbali zonse.+ 32  Akukanenanso kuti malo owolokera mtsinje alandidwa+ ndipo ngalawa zagumbwa* zatenthedwa. Amuna ankhondo nawonso asokonezeka.”+ 33  Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Mwana wamkazi wa Babulo ali ngati malo opunthira mbewu.+ Ino ndi nthawi yomupondaponda. Koma kwatsala ka nthawi pang’ono kuti nthawi yokolola imufikire.”+ 34  “Nebukadirezara mfumu ya Babulo wandidya.+ Wandisokoneza ndi kundisandutsa chiwiya chopanda kanthu. Wandimeza ngati chinjoka chachikulu.+ Wakhuta zinthu zanga zokoma ndipo wanditsukuluza. 35  Mkazi wokhala mu Ziyoni adzanena kuti, ‘Chiwawa chimene achitira ine ndi thupi langa chigwerenso Babulo.’+ Yerusalemu adzanena kuti, ‘Magazi anga akhale pa anthu okhala m’dziko la Kasidi.’”+ 36  Choncho Yehova wanena kuti: “Ine ndikukuyankhira mlandu,+ ndipo ndidzakubwezerera chilango.+ Ndidzaphwetsa nyanja yake ndi zitsime zake.+ 37  Babulo adzakhala milu yamiyala+ ndi malo obisalamo mimbulu.+ Adzakhala chinthu chodabwitsa ndi chochiimbira mluzu ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.+ 38  Anthu onse okhala mmenemo adzabangula ngati mikango yamphamvu. Adzalira ngati ana a mikango.” 39  “Chilakolako chawo chikadzakhala champhavu kwambiri ndidzawakonzera mapwando ndipo ndidzawaledzeretsa kuti asangalale.+ Pamenepo adzagona tulo tomwe tidzakhalapo mpaka kalekale, ndipo sadzadzukanso,”+ watero Yehova. 40  “Ndidzapita nawo kumalo owaphera ngati nkhosa zamphongo zopita kokaphedwa, ngati nkhosa zamphongo pamodzi ndi mbuzi zamphongo.”+ 41  “Taonani! Sesaki walandidwa.+ Dziko lotamandidwa padziko lonse lapansi latengedwa.+ Babulo wakhala chinthu chodabwitsa pakati pa mitundu ya anthu.+ 42  Nyanja yasefukira ndi kumiza Babulo. Mzinda wa Babulo wamizidwa pansi pa mafunde ambiri a nyanjayo.+ 43  Mizinda yake yakhala chinthu chodabwitsa, dziko lopanda madzi komanso chipululu.+ Mizindayo yakhala ngati dziko limene simukukhala munthu aliyense ndipo sipadzapezeka mwana aliyense wa munthu wodutsa mmenemo.+ 44  Ndidzalanga Beli+ ku Babulo ndipo ndidzamulavulitsa zimene wameza.+ Mitundu ya anthu sidzakhamukiranso kwa iye.+ Kuwonjezera apo, mpanda wa Babulo udzagwa.+ 45  “Tulukani mwa iye anthu anga,+ ndipo aliyense wa inu apulumutse moyo wake+ ku mkwiyo wa Yehova woyaka moto.+ 46  Mukapanda kutero mudzaopa m’mitima yanu+ ndipo mudzachita mantha chifukwa cha uthenga umene udzamveka m’dzikolo. M’chaka chimodzi uthengawo udzafika, kenako m’chaka china mudzamvekanso uthenga ndipo padzachitika chiwawa padziko lapansi. Wolamulira adzaukira wolamulira mnzake. 47  Taonani! Masiku adzafika ndipo ndidzalanga zifaniziro zogoba za ku Babulo.+ Dziko lake lonse lidzachita manyazi ndipo mitembo ya anthu ake onse ophedwa idzakhala paliponse mumzindawo.+ 48  “Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo zidzafuula mosangalala chifukwa cha kugwa kwa Babulo,+ pakuti ofunkha zinthu zake adzafika kuchokera kumpoto,”+ watero Yehova. 49  “Babulo sanangophetsa anthu a mu Isiraeli okha+ koma anaphetsanso anthu a padziko lonse lapansi m’Babulomo.+ 50  “Inu amene mwathawa lupanga, pitirizani kuthawa. Musaime chilili.+ Kumbukirani Yehova+ pamene muli kutali kwambiri ndipo mukumbukirenso Yerusalemu mumtima mwanu.”+ 51  “Tamva mawu otonza+ ndipo tachita manyazi.+ Manyazi atiphimba nkhope+ chifukwa alendo aukira malo oyera m’nyumba ya Yehova.”+ 52  “Chotero masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo ndidzalanga zifaniziro zake zogoba.+ M’dziko lake lonse anthu obayidwa adzakhala akubuula.”+ 53  “Ngakhale Babulo atakwera kukafika kumwamba,+ kapenanso atakweza mphamvu zake kukhala zosafikirika,+ anthu ofunkha zinthu zake ochokera kwa ine adzamupeza,”+ watero Yehova. 54  “Tamverani! Ku Babulo kukumveka kulira kofuula+ ndipo m’dziko la Akasidi mukumveka phokoso la chiwonongeko chachikulu,+ 55  chifukwa Yehova akufunkha zinthu za Babulo ndi kuthetsa mawu ake aakulu.+ Mafunde awo adzachita phokoso ngati madzi ambiri.+ Komanso phokoso la mawu awo lidzamveka m’Babulo. 56  Wofunkha adzafikira Babulo+ ndipo amuna ake amphamvu adzagwidwa.+ Mauta awo adzathyoledwa,+ pakuti Yehova ndi Mulungu wobwezera.+ Iye adzawabwezera ndithu.+ 57  Ndidzaledzeretsa akalonga, anthu ake anzeru, abwanamkubwa ake, atsogoleri ake ndi anthu ake amphamvu.+ Adzagona tulo tomwe tidzakhalapo mpaka kalekale ndipo sadzadzukanso,”+ yatero Mfumu,+ imene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ 58  Yehova wa makamu wanena kuti: “Ngakhale kuti mpanda wa Babulo ndi waukulu udzagwetsedwa ndithu.+ Ngakhale kuti zipata zake ndi zazitali zidzatenthedwa.+ Anthu adzagwira ntchito yolemetsa pachabe.+ Mitundu ya anthu idzagwira ntchito yolemetsa imene idzawonongedwa ndi moto+ ndipo adzangodzitopetsa.” 59  Mneneri Yeremiya anapereka malangizo kwa Seraya mwana wa Neriya+ mwana wa Maseya.+ Anapereka malangizowo pamene Seraya anapita ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babulo m’chaka chachinayi cha ufumu wake. Pa nthawiyo Seraya anali mkulu woyang’anira zinthu za mfumu. 60  Yeremiya analemba m’buku limodzi+ za masoka onse odzagwera Babulo. Iye analemba mawu onsewa okhudza zimene zidzachitikire Babulo. 61  Chotero Yeremiya anauza Seraya kuti: “Ukakafika ku Babulo ndi kuona mzindawo, ukawerenge mokweza mawu onsewa.+ 62  Ukanene kuti, ‘Inu Yehova! Inu mwanena zowononga malo ano ndi kuwafafaniza kuti pasapezekenso chilichonse chokhalamo.+ Musapezeke munthu kapena chiweto koma mzindawo ukhale bwinja mpaka kalekale.’ 63  Ndiye ukakamaliza kuwerenga bukuli, ukalimangirire mwala ndi kuliponya pakati pa mtsinje wa Firate.+ 64  Ndiyeno ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene Babulo adzamirire osatulukanso chifukwa cha masoka amene ndikumugwetsera.+ Ndipo Ababulowo adzadzitopetsa okha.’”+ Mawu a Yeremiya athera pamenepa.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.