Yeremiya 37:1-21

37  Ndiyeno Mfumu Zedekiya+ mwana wa Yosiya,+ amene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anamuika kukhala mfumu m’dziko la Yuda,+ anayamba kulamulira m’malo mwa Koniya+ mwana wa Yehoyakimu.+  Koma Zedekiyayo, atumiki ake ndi anthu a m’dzikoli sanamvere mawu amene Yehova+ ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya.+  Mfumu Zedekiya inatumiza Yehukali+ mwana wa Selemiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya+ wansembe kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga wakuti: “Chonde, tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu.”+  Yeremiya anali kukhala mwaufulu pakati pa anthu+ chifukwa anali asanamutsekere m’ndende.  Ndiyeno gulu lankhondo la Farao linabwera kuchokera ku Iguputo.+ Akasidi amene anali atazungulira mzinda wa Yerusalemu atamva zimenezi anachoka ku Yerusalemu.+  Kenako Yehova anauza mneneri Yeremiya kuti:  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu inu mukauze mfumu ya Yuda imene yakutumani kuno kudzafunsira uthenga wa Mulungu kwa ine+ kuti: “Taonani! Gulu lankhondo la Farao limene likubwera kwa anthu inu kuti likuthandizeni lidzabwerera kwawo ku Iguputo.+  Ndipo Akasidi adzabweranso ndithu kudzamenyana ndi mzinda uno, kuulanda ndi kuutentha ndi moto.”+  Yehova wanena kuti: “Musadzinyenge+ pomanena kuti, ‘Akasidi amenewa samenyana nafe, achoka ndithu,’ chifukwa sachoka ayi. 10  Pakuti ngakhale anthu inu mutapha gulu lonse lankhondo la Akasidi amene akumenyana nanu+ ndipo pangotsala amuna ovulala kwambiri pakati pawo,+ aliyense wa amenewo adzadzuka muhema wake ndi kubwera kudzatentha mzinda uno.”’” 11  Ndiyeno gulu lankhondo la Akasidi litabwerera kuchoka ku Yerusalemu+ chifukwa cha gulu lankhondo la Farao,+ 12  Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu kupita kudziko la Benjamini+ kuti akalandire malo ake pakati pa anthu ake. 13  Atafika pa Chipata cha Benjamini,+ anakumana ndi mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya. Nthawi yomweyo Iriya anagwira mneneri Yeremiya ndi kunena kuti: “Ukuthawira kwa Akasidi!” 14  Yeremiya anamuyankha kuti: “Zabodza zimenezo!+ Ine sindikuthawira kwa Akasidi.” Koma Iriya sanamumvere. Choncho iye anagwirabe Yeremiya ndi kumubweretsa kwa akalonga. 15  Pamenepo akalonga+ anamukwiyira kwambiri Yeremiya+ ndipo anamumenya+ ndi kumutsekera m’ndende+ m’nyumba ya Yehonatani+ mlembi, pakuti nyumba yake ndi imene anaisandutsa ndende.+ 16  Yeremiya atalowa m’ndende ya pansiyo,+ m’kachipinda ka m’ndendemo, anakhala mmenemo kwa masiku ambiri. 17  Kenako Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akatenge Yeremiya. Atabwera naye, mfumuyo inayamba kumufunsa mafunso m’nyumba mwake pamalo obisika.+ Mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi pali mawu aliwonse ochokera kwa Yehova?” Pamenepo Yeremiya anayankha kuti: “Inde alipo!” Ndiyeno Yeremiya ananenanso kuti: “Inuyo mudzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Babulo!”+ 18  Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti: “Kodi ineyo ndakulakwirani chiyani pamodzi ndi atumiki anu ndiponso anthu onse,+ kuti munditsekere m’ndende? 19  Tsopano ali kuti aneneri anu amene anali kulosera kwa inu ponena kuti, ‘Mfumu ya Babulo sidzabwera kudzamenyana ndi anthu inu ndiponso kudzamenyana ndi dzikoli’?+ 20  Tsopano ndimvereni chonde, mbuyanga mfumu. Chonde, mverani pempho langa lakuti mundikomere mtima.+ Musandibwezere kunyumba ya Yehonatani+ mlembi, chifukwa ndingakafere kumeneko.”+ 21  Chotero Mfumu Zedekiya inalamula kuti atsekere Yeremiya m’Bwalo la Alonda+ ndipo anali kumupatsa mtanda wobulungira wa mkate tsiku ndi tsiku. Mkate umenewu unali kuchokera kumsewu wa ophika mkate+ ndipo anapitiriza kum’patsa mkatewo kufikira mkate wonse utatha mumzindamo.+ Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala m’Bwalo la Alonda.+

Mawu a M'munsi