Yesaya 21:1-17

21  Uwu ndi uthenga wokhudza chipululu cha nyanja:*+ Kuchipululu kukubwera chinthu chinachake kuchokera kudziko lochititsa mantha.+ Chikubwera ngati mphepo yamkuntho+ yochokera kum’mwera.  Pali masomphenya ochititsa mantha+ amene ndaona: Mtundu wochita chinyengo ukuchita zachinyengo, ndipo mtundu wolanda zinthu ukulanda zinthu.+ Pita ukachite nkhondo, iwe Elamu! Kazungulire mzindawo, iwe Mediya!+ Ndathetsa kuusa moyo* konse kumene mzindawo unachititsa.+  N’chifukwa chake m’chiuno mwanga mwadzaza ululu woopsa.+ Zopweteka zandigwira, ngati zowawa za mkazi amene akubereka.+ Ndazunguzika moti sindikumva. Ndasokonezeka moti sindikuona.  Mtima wanga ukuthamanga. Ndikunjenjemera ndi mantha. Chisisira cha madzulo chimene ndinali kuchikonda chakhala chondichititsa mantha.+  Yalani patebulo. Ikani mipando m’malo mwake. Idyani, imwani.+ Akalonga inu,+ nyamukani, dzozani chishango.+  Pakuti Yehova wandiuza kuti: “Pita, kaike mlonda pamalo ake, kuti anene zonse zimene aone.”+  Mlondayo anaona magaleta ankhondo okokedwa ndi mahatchi awiriawiri, magaleta ankhondo okokedwa ndi abulu, ndi magaleta ankhondo okokedwa ndi ngamila. Iye anali kuyang’anitsitsa, ndipo anali tcheru kwambiri.  Kenako anafuula mwamphamvu ngati kubangula kwa mkango,+ kuti: “Inu Yehova, ine ndimaimirira tsiku lonse pansanja ya mlonda, ndipo usiku uliwonse ndimakhala pamalo anga olonderapo.+  Tsopano taonani! Kukubwera magaleta ankhondo okokedwa ndi mahatchi awiriawiri, mutakwera amuna ankhondo.”+ Kenako iye anayamba kufuula kuti: “Wagwa! Babulo wagwa!+ Zifaniziro zonse zogoba za milungu yake zaphwanyidwa ndipo zili pansi.”+ 10  Inu anthu anga amene mwapunthidwa ngati mbewu, ndi iwe mwana wa pamalo anga opunthira mbewu,+ zimene ndamva kwa Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, n’zimene ndakuuzani anthu inu. 11  Uwu ndi uthenga wokhudza Duma: Ndikumva winawake akundifunsa mofuula kuchokera ku Seiri+ kuti: “Mlonda, kodi usiku watsala wotalika bwanji? Mlonda, kodi usiku watsala wotalika bwanji?”+ 12  Mlondayo anayankha kuti: “M’mawa ufika, ndipo usiku ufikanso. Ngati anthu inu mukufuna kufunsa, funsani ndipo mubwerenso.” 13  Uwu ndi uthenga wokhudza chipululu: Inu amuna amtengatenga a ku Dedani oyenda pa ngamila, usiku mudzagona m’nkhalango ya m’chipululu.+ 14  Mubweretse madzi podzakumana ndi munthu waludzu. Inu anthu okhala ku Tema,+ mukhale ndi chakudya podzakumana ndi munthu amene akuthawa. 15  Pakuti iwo athawa chifukwa cha malupanga, chifukwa cha lupanga losololedwa m’chimake, chifukwa cha uta wopindidwa, ndiponso chifukwa cha kukula kwa nkhondo. 16  Pakuti Yehova wandiuza kuti: “Pakutha chaka chimodzi, osawonjezerapo ngakhale tsiku limodzi,*+ ulemerero wonse wa Kedara+ udzakhala utatha. 17  Anthu otsala pa amuna oponya mivi ndi uta, omwe ndi amuna amphamvu a ana a Kedara, adzakhala ochepa,+ pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena zimenezi.”+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “chipululu cha nyanja” mwina akutanthauza chigawo cha kum’mwera cha dziko lakale la Babulo, kumene mitsinje ya Firate ndi Tigirisi inali kusefukira chaka chilichonse.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “malinga ndi zaka za munthu waganyu.” Onani mawu a m’munsi pa Yes 16:14.