Yesaya 51:1-23
51 “Ndimvereni, inu anthu amene mukufunafuna chilungamo,+ inu amene mukufuna kupeza Yehova.+ Yang’anani kuthanthwe+ limene munasemedwako, ndi kuphanga la dzenje limene munakumbidwako.
2 Yang’anani kwa tate+ wanu Abulahamu,+ ndi kwa Sara+ amene anakuberekani ndi zowawa za pobereka. Abulahamuyo anali munthu mmodzi pamene ndinamuitana,+ koma ndinamudalitsa ndi kumusandutsa anthu ambiri.+
3 Pakuti Yehova adzatonthoza Ziyoni.+ Iye adzatonthozadi malo ake onse owonongedwa.+ Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+ ndi dera lake lachipululu kukhala ngati munda wa Yehova.+ Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera, kuyamikira ndi kuimba nyimbo.+
4 “Inu anthu anga, tandimverani. Iwe mtundu wanga,+ tatchera khutu kwa ine. Pakuti kwa ine kudzachokera lamulo+ ndipo ndidzachititsa chigamulo changa kukhazikika monga kuwala kwa mitundu ya anthu.+
5 Chilungamo changa chili pafupi.+ Chipulumutso+ chochokera kwa ine chili m’njira ndipo manja anga adzaweruza mitundu ya anthu.+ Zilumba zidzayembekezera ine+ ndipo zidzadikira dzanja langa.+
6 “Kwezani maso anu kumwamba,+ ndipo yang’anani padziko lapansi. Pakuti kumwamba kudzabenthukabenthuka n’kumwazidwa ngati utsi,+ ndipo dziko lapansi lidzatha ngati chovala.+ Anthu okhalamo adzafa ngati ntchentche. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka kalekale+ ndipo chilungamo changa sichidzaphwanyika.+
7 “Ndimvereni, inu odziwa chilungamo, inu amene muli ndi lamulo langa mumtima mwanu.+ Musaope chitonzo cha anthu ndipo musachite mantha chifukwa cha mawu awo onyoza.+
8 Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala ndipo kachilombo kodya zovala kadzawadya ngati thonje.+ Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka kalekale ndipo chipulumutso changa chidzafikira mibadwo yosawerengeka.”+
9 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu,+ iwe dzanja la Yehova!+ Dzuka ngati masiku akale, ngati m’mibadwo yakalekale.+ Kodi si iwe amene unaphwanyaphwanya Rahabi,+ amene unabaya* chilombo cha m’nyanja?+
10 Kodi si iwe amene unaumitsa nyanja, amene unaumitsa madzi akuya kwambiri?+ Si iwe kodi amene unasandutsa pansi pa nyanja kukhala njira yoti anthu owomboledwa awolokerepo?+
11 Chotero, owomboledwa a Yehova adzabwerera ku Ziyoni ndi mfuu yachisangalalo,+ ndipo pamutu pawo padzakhala chisangalalo mpaka kalekale.+ Iwo adzapeza chisangalalo ndi chimwemwe.+ Chisoni ndi kuusa moyo zidzachoka.+
12 “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.+
“Kodi n’chifukwa chiyani iwe ukuopa munthu woti adzafa,+ ndi mwana wa munthu yemwe adzakhale ngati udzu wobiriwira?+
13 Kodi n’chifukwa chiyani ukuiwala Yehova amene anakupanga,+ amene anatambasula kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi?+ N’chifukwa chiyani ukuchita mantha nthawi zonse, tsiku lonse lathunthu, poopa mkwiyo wa yemwe akukupanikizira mkati,+ ngati kuti iye wakonzeka kuti akuwononge?+ Kodi mkwiyo wa amene akukupanikizira mkati uli kuti?+
14 “Yemwe wawerama atamangidwa maunyolo adzamasulidwa msangamsanga.+ Iye sadzafa, sadzatsikira kudzenje,+ komanso sadzasowa chakudya.+
15 “Koma ine Yehova ndine Mulungu wako, amene ndimavundula nyanja kuti mafunde ake achite phokoso.+ Yehova wa makamu ndiye dzina langa.+
16 Ndidzaika mawu anga m’kamwa mwako+ ndipo ndidzakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa.+ Ndidzachita zimenezi n’cholinga choti ndikhazikitse kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi,+ ndiponso kuti ndiuze Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’+
17 “Dzuka! Dzuka! Imirira iwe Yerusalemu,+ iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo wa Yehova kuchokera m’dzanja lake.+ Iweyo wamwa ndipo wagugudiza chipanda, chikho chochititsa munthu kuyenda dzandidzandi.+
18 Pa ana onse amene iye anabereka, palibe ndi mmodzi yemwe+ amene anali kutsogolera mayiyo poyenda. Pa ana onse amene iye analera, palibe ndi mmodzi yemwe amene anagwira dzanja lake.+
19 Zinthu ziwiri zidzakugwera.+ Kodi adzakumvera chisoni ndani?+ Udzalandidwa katundu ndi kuphwanyidwa, ndiponso udzakumana ndi njala ndi lupanga.+ Kodi adzakutonthoza ndani?+
20 Ana ako akomoka.+ Agona m’misewu yonse ngati nkhosa zakutchire zokodwa mu ukonde,+ ngati anthu okhuta mkwiyo wa Yehova,+ okhuta kudzudzula kwa Mulungu wako.”+
21 Chotero mvetsera izi, iwe mkazi+ wosautsidwa ndi woledzera, koma osati ndi vinyo.+
22 Ambuye wako, Yehova, Mulungu wako, amene amateteza+ anthu ake, wanena kuti: “Taona! Ine ndidzachotsa m’manja mwako chikho chochititsa munthu kudzandira.+ Sudzamwanso chipanda, chikho cha mkwiyo wanga.+
23 Ndidzachiika m’manja mwa amene akukuvutitsa,+ amene akukuuza kuti, ‘Werama kuti tiwolokere pamsana pako,’ amene akuona msana wako ngati pansi popondapo, ndiponso ngati njira yowolokerapo.”+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “kulasa.”