Yesaya 36:1-22

36  M’chaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera kudzachita nkhondo ndi mizinda yonse ya Ayuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo analanda mizindayo.+  Pomalizira pake mfumu ya Asuri inatuma Rabisake*+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu.+ Inamutumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu. Iye anakaima pangalande+ yochokera kudziwe lakumtunda,+ pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+  Kenako kunabwera Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyang’anira banja lachifumu, Sebina+ mlembi, ndi Yowa+ mwana wa Asafu+ wolemba zochitika.+  Choncho Rabisake anawauza kuti: “Mukauze Hezekiya kuti, ‘Mfumu yaikulu,+ mfumu ya Asuri+ yanena kuti: “Kodi ukudalira chiyani?+  Iwe wanena kuti (koma ndi mawu a pakamwa chabe), ‘Ine ndili ndi nzeru ndi mphamvu zofunika pankhondo.’+ Kodi ukudalira ndani popandukira ine?+  Ukudalira thandizo la Iguputo,+ bango lophwanyika loti munthu ataligwira kuti limuchirikize,+ lingamucheke m’manja. Umu ndi mmene Farao+ mfumu ya Iguputo alili kwa onse omudalira.+  Ngati inu mungandiuze kuti, ‘Tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si iye amene Hezekiya wamuchotsera malo ake okwezeka+ ndi maguwa ake ansembe,+ n’kuuza Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzigwada pamaso pa guwa lansembe ili’?”’+  Tsopano ubetcherane+ ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri,+ ndipo ine ndikupatsa mahatchi 2,000 kuti ndione ngati iweyo ungathe kupeza okwerapo.+  Kodi ungathe bwanji kubweza bwanamkubwa mmodzi, yemwe ndi mtumiki wotsika kwambiri wa mbuye wanga,+ pamene iweyo ukuchita kudalira Iguputo kuti akupatse magaleta ndi okwera pamahatchi?+ 10  Kodi ukuganiza kuti ndabwera kudzawononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova weniweniyo wandiuza kuti,+ ‘Pita ukamenyane ndi dzikolo, ndipo ukaliwononge.’”+ 11  Pamenepo Eliyakimu,+ Sebina,+ ndi Yowa+ anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu m’chilankhulo cha Asiriya+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe m’chilankhulo cha Ayuda,+ kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.”+ 12  Koma Rabisake anayankha kuti: “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene mawuwa kwa mbuye wanu yekha ndi kwa inuyo? Kodi sananditumenso kwa amuna amene akhala pamakomawo, kuti adye chimbudzi chawo ndi kumwa mkodzo wawo limodzi nanu?”+ 13  Choncho Rabisake akadali chiimire,+ anapitiriza kulankhula mokweza m’chilankhulo cha Ayuda,+ kuti: “Imvani mawu a mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri.+ 14  Mfumuyo yanena kuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akunamizeni anthu inu,+ chifukwa sangathe kukulanditsani.+ 15  Musalole kuti Hezekiya akuchititseni kudalira Yehova,+ pokuuzani kuti: “Mosakayikira Yehova atilanditsa,+ ndipo mzindawu superekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 16  Musamvere Hezekiya chifukwa mfumu ya Asuri yanena kuti: “Ndigonjereni,+ ndipo bwerani kwa ine. Aliyense azidya zochokera mumtengo wake wa mpesa ndi mumtengo wake wa mkuyu,+ komanso aliyense azimwa madzi a m’chitsime chake,+ 17  kufikira ine nditabwera kudzakutengerani kudziko lofanana ndi dziko lanulo.+ Ndidzakutengerani kudziko la mbewu ndi la vinyo watsopano, dziko la mkate ndi minda ya mpesa. 18  Musamvere Hezekiya chifukwa akukunyengererani+ ndi mawu akuti, ‘Yehova atilanditsa.’ Kodi pali mulungu wa mitundu ina amene wakwanitsa kupulumutsa mtundu wake m’manja mwa mfumu ya Asuri?+ 19  Kodi milungu ya Hamati+ ndi Aripadi+ ili kuti? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu?+ Kodi yalanditsa Samariya m’manja mwanga?+ 20  Ndi mulungu uti pakati pa milungu yonse ya mayiko amenewa, amene walanditsa dziko lake m’manja mwanga,+ kuti Yehova athe kulanditsa Yerusalemu m’manja mwanga?”’”+ 21  Anthuwo anangokhala chete osamuyankha,+ chifukwa lamulo lochokera kwa mfumu linali lakuti: “Musamuyankhe.”+ 22  Koma Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyang’anira banja lachifumu,+ Sebina+ mlembi, ndi Yowa+ mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kwa Hezekiya atang’amba zovala zawo+ n’kumuuza mawu a Rabisake.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “mkulu wa operekera chikho.”