Yesaya 45:1-25
45 Ine Yehova ndalankhula kwa wodzozedwa wanga.+ Ndalankhula kwa Koresi amene ndamugwira dzanja lake lamanja+ kuti ndigonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+ kuti ndimasule m’chiuno mwa mafumu, kuti ndimutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri, moti ngakhale zipata sizidzatsekedwa. Ndalankhula kuti:
2 “Ine ndidzakhala kutsogolo kwako+ ndipo ndidzasalaza zitunda za m’dzikolo.+ Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuwa ndipo ndidzadula mipiringidzo yachitsulo.+
3 Ndidzakupatsa chuma+ chimene chili mu mdima ndi chuma chobisika chimene chili m’malo achinsinsi, kuti udziwe kuti ine ndine Yehova, Mulungu wa Isiraeli, amene ndikukuitana ndi dzina lako.+
4 Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo ndi Isiraeli wosankhidwa wanga,+ ine ndinakuitana ndi dzina lako. Ndinakupatsa dzina laulemu, ngakhale kuti sunali kundidziwa.+
5 Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.+ Palibenso Mulungu kupatulapo ine.+ Ndidzakumanga mwamphamvu m’chiuno mwako, ngakhale kuti sukundidziwa,
6 kuti anthu adziwe kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kolowera dzuwa kuti palibenso wina kupatulapo ine.+ Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+
7 Ndimapanga kuwala+ ndiponso ndimabweretsa mdima.+ Ndimabweretsa mtendere+ ndiponso tsoka.+ Ine Yehova ndimapanga zonsezi.+
8 “Inu kumwamba, chititsani chilungamo kuvumba ngati mvula.+ Kumwamba kwa mitambo kuchuche chilungamo.+ Dziko lapansi litseguke ndipo libale chipulumutso. Lichititse chilungamo kuphuka+ pa nthawi imodzimodziyo. Ine Yehova ndachititsa zimenezi.”+
9 Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”?
10 Tsoka kwa wofunsa bambo kuti: “Kodi n’chiyani mwaberekachi?” Ndiponso wofunsa mkazi kuti: “Kodi zowawa za pobereka zimene mukumvazi mukufuna mubereke chiyani?”+
11 Yehova, Woyera wa Isiraeli+ ndiponso amene anamuumba,+ wanena kuti: “Ndifunseni za zinthu zimene zikubwera+ zokhudza ana anga.+ Ndipo pa zinthu zokhudza ntchito+ ya manja anga mundifunse kuti ndikuyankheni.
12 Ineyo ndinapanga dziko lapansi+ ndipo ndinalenga munthu n’kumuikapo.+ Manja anga anatambasula kumwamba,+ ndipo nyenyezi ndi zonse zimene zili kumwambako ndimazilamulira.”+
13 “Ine ndautsa winawake m’chilungamo+ ndipo njira zake zonse ndidzaziwongola.+ Iye ndi amene adzamange mzinda wanga+ ndipo anthu anga amene ali ku ukapolo adzawamasula,+ koma osati ndi malipiro+ kapena ndi chiphuphu,” watero Yehova wa makamu.
14 Yehova wanena kuti: “Antchito osalipidwa a ku Iguputo,+ amalonda a ku Itiyopiya, ndi Asabeya,+ amuna ataliatali,+ adzabwera kwa iwe ndipo adzakhala ako.+ Iwo adzayenda pambuyo pako. Adzabwera kwa iwe atamangidwa m’matangadza+ ndipo adzakugwadira.+ Adzapemphera kwa iwe kuti, ‘Zoonadi Mulungu ali ndi iwe+ ndipo palibenso wina. Palibenso Mulungu wina.’”+
15 Ndithu, inu ndinu Mulungu yemwe amadzibisa,+ Mulungu wa Isiraeli, Mpulumutsi.+
16 Anthu adzachita manyazi ndipo onsewo adzanyozeka. Anthu opanga mafano adzayenda monyozeka onse pamodzi.+
17 Koma Isiraeli adzapulumutsidwa chifukwa chokhala pa mgwirizano ndi Yehova+ ndipo adzakhala wopulumutsidwa mpaka kalekale.+ Anthu inu simudzachita manyazi+ ndipo simudzanyozeka+ mpaka kalekale, ngakhale kwamuyaya.
18 Pakuti Yehova, Mlengi wa kumwamba,+ Mulungu woona,+ amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga,+ amene analikhazikitsa mwamphamvu,+ amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo,+ wanena kuti: “Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+
19 Ine sindinalankhule m’malo obisika,+ m’malo amdima a padziko lapansi. Sindinauze mbewu ya Yakobo kuti, ‘Anthu inu muzindifunafuna pachabe.’+ Ine ndine Yehova, wolankhula zolungama, wonena zowongoka.+
20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+
21 Lankhulani ndipo mufotokoze mlandu wanu.+ Inde, iwo afunsanefunsane mogwirizana. Kodi ndani wachititsa zimenezi kuti zimveke kuyambira kalekale?+ Ndani wazinena kuyambira nthawi imene ija?+ Kodi si ine Yehova, amene palibenso Mulungu wina kupatulapo ine?+ Ine ndine Mulungu wolungama ndi Mpulumutsi+ ndipo palibenso wina kupatulapo ine.+
22 “Tembenukirani kwa ine kuti mupulumuke,+ inu nonse amene muli kumapeto kwa dziko lapansi, pakuti ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.+
23 Ndalumbira pa ine mwini.+ Mawuwo atuluka m’kamwa mwanga m’chilungamo,+ moti sadzabwerera.+ Ndalumbira kuti bondo lililonse lidzagwadira ine+ ndipo lilime lililonse lidzalumbira kwa ine,+
24 kuti, ‘Zoonadi, kwa Yehova kuli chilungamo chonse ndi mphamvu.+ Onse omukwiyira adzabwereranso kwa iyeyo n’kuchita manyazi.+
25 Mbewu+ yonse ya Isiraeli idzaona kuti inalondola+ potumikira Yehova ndipo idzadzitama.’”+