Yesaya 12:1-6
12 M’tsiku limenelo+ ndithu udzanena kuti: “Ndikukuthokozani inu Yehova pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu unabwerera pang’onopang’ono+ ndipo munanditonthoza.+
2 Taonani! Mulungu ndiye chipulumutso changa.+ Ndidzamukhulupirira ndipo sindidzaopa chilichonse,+ pakuti Ya* Yehova ndiye mphamvu zanga+ ndi nyonga zanga,+ ndipo iye wakhala chipulumutso changa.”+
3 Anthu inu ndithu mudzatunga madzi mosangalala pa akasupe a chipulumutso.+
4 M’tsiku limenelo mudzanenadi kuti: “Yamikani Yehova anthu inu.+ Itanani pa dzina lake.+ Dziwitsani mitundu ya anthu zochita zake.+ Nenani kuti dzina lake n’lokwezeka.+
5 Muimbireni nyimbo Yehova+ chifukwa wachita zopambana.+ Zimenezi zikulengezedwa m’dziko lonse lapansi.
6 “Fuula mwachisangalalo iwe mkazi wokhala mu Ziyoni, pakuti Woyera wa Isiraeli ndi wamkulu pakati pako.”+