Yesaya 47:1-15

47  Tsika ukhale pansi pafumbi+ iwe namwali, mwana wamkazi wa Babulo.+ Khala padothi pomwe palibe mpando wachifumu,+ iwe mwana wamkazi wa Akasidi.+ Pakuti anthu adzaleka kukutchula kuti ndiwe wolekereredwa ndiponso wosasatitsidwa.*+  Tenga mphero+ upere ufa. Vula nsalu yako yophimba kumutu.+ Vula chovala chako chokhwekhwerera pansi.+ Ukweze chovala chako m’mwamba mpaka miyendo ionekere,+ ndipo uwoloke mitsinje.  Vula ukhale maliseche,+ komanso manyazi ako aonekere.+ Ine ndidzabwezera+ ndipo sindidzalekerera aliyense wofuna kunditsekereza.  “Pali amene akutiwombola.+ Dzina lake ndi Yehova wa makamu,+ Woyera wa Isiraeli.”+  Iwe mwana wamkazi wa Akasidi,+ khala pansi mwakachetechete+ ndipo ulowe mu mdima.+ Pakuti anthu sadzakutchulanso kuti Dona+ wa Maufumu.+  Ine ndinakwiyira anthu anga.+ Ndinanyoza cholowa changa+ ndipo ndinawapereka m’manja mwako.+ Iwe sunawachitire chifundo.+ Munthu wokalamba unamusenzetsa goli lolemera kwambiri.+  Iwe unali kunena kuti: “Ine ndidzakhala Dona mpaka kalekale,+ mpaka muyaya.” Sunaganizire zinthu izi mumtima mwako ndipo sunaganizire kuti zidzatha bwanji.+  Tsopano imva izi iwe mkazi wokonda zosangalatsa, wokhala pabwino,+ iwe amene umanena mumtima mwako kuti: “Ndine ndekha, palibenso wina.+ Sindidzakhala wamasiye ndipo ana anga sadzafa.”+  Koma zinthu ziwiri izi zidzakugwera modzidzimutsa tsiku limodzi:+ Ana ako adzafa ndiponso udzakhala wamasiye. Zimenezi zidzakugwera ndithu,+ chifukwa cha zamatsenga zochuluka zimene wachita, chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zako zamatsenga, ndiponso chifukwa chakuti wazichita kwambiri.+ 10  Iwe unali kudalira zoipa zako.+ Wanena kuti: “Palibe amene akundiona.”+ Wasochera chifukwa cha nzeru zako ndiponso chifukwa chodziwa zinthu.+ Mumtima mwako umakhalira kunena kuti: “Ndine ndekha, palibenso wina.” 11  Koma tsoka lidzakugwera ndipo sudzatha kuliletsa ndi matsenga ako. Mavuto adzakugwera+ ndipo sudzatha kuwapewa. Chiwonongeko chimene sunali kuchiyembekezera chidzakupeza modzidzimutsa.+ 12  Tsopano imirira, tenga nyanga zako ndiponso zamatsenga zako zambirimbiri+ zomwe wazivutikira kuyambira uli mwana. Uzitenge kuti mwina zingakuthandize kapenanso kuti ungachite nazo zodabwitsa kwa anthu. 13  Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa. Anthu opembedza zinthu zakumwamba, oyang’anitsitsa kayendedwe ka nyenyezi,+ amene amalosera zimene zichitike kwa iwe mwezi watsopano ukakhala, tsopano aimirire ndi kukupulumutsa. 14  Iwotu akhala ngati mapesi.+ Moto udzawatentha ndithu.+ Sadzapulumutsa moyo wawo+ ku mphamvu ya moto walawilawi.+ Sudzakhala moto wamakala woti anthu n’kumawotha. Sudzakhala moto wounikira woti anthu n’kuuyandikira. 15  Umu ndi mmene amatsenga+ ako amene wawavutikira kuyambira uli mwana adzakhalire. Iwo adzabalalika, aliyense kulowera kuchigawo cha kwawo ndipo sipadzakhala woti akupulumutse.+

Mawu a M'munsi

Munthu “wosasatitsidwa” ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pa moyo wake.