Yesaya 18:1-7

18  Tsoka kwa dziko lamkokomo wa tizilombo tamapiko, limene lili m’chigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya.+  Limeneli ndi dziko lomwe limatumiza nthumwi zake+ panyanja, m’ngalawa zoyenda pamadzi zopangidwa ndi gumbwa.* Limauza nthumwizo kuti: “Inu amithenga achangu, pitani ku mtundu wa anthu ataliatali osalala, anthu oopedwa ndi mitundu yonse ya anthu. Umenewu ndi mtundu wa anthu amphamvu kwambiri, ndiponso wopambana pa nkhondo, umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje.”+  Inu nonse okhala panthaka ndi inu okhala m’dziko lapansi,+ mudzaona chinthu chooneka ngati chizindikiro chimene chimaikidwa pamapiri,+ ndipo mudzamva zofanana ndi kulira kwa lipenga.+  Pakuti Yehova wandiuza kuti: “Ine ndidzakhala mosatekeseka n’kumayang’ana pamalo anga okhazikika.+ Ndidzachita zimenezi ngati kutentha kumene kumakhalapo masana kukawala,+ ndiponso ngati mame amene amagwa pa nthawi yokolola, m’nyengo yotentha.+  Pakuti nyengo yokolola isanafike, mitengo ikamaliza kuchita maluwa ndipo mphesa zikamapsa, mlimi amadula mphukira ndi chida chosadzira mitengo ndipo amasadzanso nthambi.+  Onsewo adzasiyidwa kuti mbalame za m’mapiri zodya nyama, ndi nyama zakutchire za padziko lapansi,+ ziwadye. Mbalame zodya nyamazo zidzakhala zikuwadya chilimwe chonse, ndipo nyama zonse zakutchire za padziko lapansi zidzakhala zikuwadya m’nyengo yonse yokolola.+  “Pa nthawi imeneyo, Yehova wa makamu+ adzapatsidwa mphatso ndi mtundu wa anthu ataliatali osalala, anthu oopedwa+ ndi mitundu yonse ya anthu. Umenewu ndi mtundu wa anthu amphamvu kwambiri, ndiponso wopambana pa nkhondo, umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje. Mphatsoyo adzaiika kuphiri la Ziyoni, kumene kuli dzina la Yehova wa makamu.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.