Yesaya 37:1-38

37  Mfumu Hezekiya itangomva zimenezi, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake n’kuvala chiguduli.+ Kenako inapita m’nyumba ya Yehova.+  Komanso inatuma Eliyakimu+ amene anali woyang’anira banja la mfumu, Sebina mlembi,+ ndi akuluakulu a ansembe,+ onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+  Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa+ ndi lodzudzula, tsiku la mnyozo ndi mwano.+ Tili ngati mkazi amene watsala pang’ono kubereka, koma alibe mphamvu zoti aberekere.+  Mwina Yehova Mulungu amva mawu onse a Rabisake,+ amene mbuye wake mfumu ya Asuri yamutuma, kuti adzatonze+ nawo Mulungu wamoyo. Ndipo mwina amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva.+ Inuyo mupereke pemphero+ m’malo mwa otsalira amene alipo.’”+  Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.+  Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki+ a mfumu ya Asuri andilankhulira monyoza.  Ndiika maganizo+ mwa iye, kuti akamva nkhani inayake,+ abwerere kudziko lake. Ndipo mosalephera, ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga m’dziko lake.”’”+  Rabisake+ anali atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi,+ choncho anabwerera kwa mfumuyo n’kukaipeza ikumenyana ndi Libina.+  Tsopano mfumuyo inamva kuti Tirihaka+ mfumu ya Itiyopiya wabwera kudzamenyana nayo. Itangomva zimenezo, nthawi yomweyo inatumizanso amithenga+ kwa Hezekiya n’kuwauza kuti: 10  “Amuna inu mukamuuze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Usalole Mulungu wako amene ukumudalira kuti akunamize,+ ponena kuti: “Yerusalemu saperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11  Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachita kumayiko onse mwa kuwawononga.+ Ndiye kodi iweyo ukuona ngati upulumuka?+ 12  Kodi milungu+ ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawalanditsa?+ Kodi inalanditsa Gozani,+ Harana,+ Rezefi ndi ana a Edeni+ amene anali ku Tela-sara? 13  Ili kuti mfumu ya Hamati,+ mfumu ya Aripadi,+ ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu,+ Hena, ndi Iva?’”+ 14  Kenako Hezekiya anatenga kalatayo m’manja mwa amithengawo n’kuiwerenga.+ Pambuyo pake iye anapita nayo kunyumba ya Yehova, n’kuitambasula pamaso pa Yehova.+ 15  Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera kwa Yehova,+ kuti: 16  “Inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+ 17  Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu,+ inu Yehova, muone, ndipo imvani mawu onse a Senakeribu+ amene watumiza kudzatonza nawo Mulungu wamoyo.+ 18  N’zoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mayiko onse, ndi dziko lawo lomwe.+ 19  Atentha milungu yawo pamoto,+ chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga.+ 20  Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ tipulumutseni m’manja mwake,+ kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+ 21  Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti wapemphera kwa ine za Senakeribu mfumu ya Asuri,+ 22  awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza ndipo wakuseka.+Kumbuyo kwako, mwana wamkazi wa Yerusalemu wakupukusira mutu.+ 23  Kodi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumulankhula monyoza?+Ndipo ndani amene iwe wam’kwezera mawu,+Ndi kum’kwezera maso ako m’mwamba?+Ndi Woyera wa Isiraeli!+ 24  Kudzera mwa antchito ako watonza Yehova ndipo wanena kuti,+Ndi magaleta anga ankhondo ambiri, ine,+Ineyo ndidzakwera ndithu madera amapiri mpaka pamwamba.+Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni+Ndipo ndidzadula mitengo yake ya mkungudza italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri yofanana ndi mkungudza.+Ndidzalowa kumalo ake okhala akutali kwambiri, kunkhalango yokongola.+ 25  Ndithu ineyo ndidzakumba zitsime ndi kumwa madzi,Ndidzaumitsa ndi mapazi anga ngalande zonse zamadzi za mtsinje wa Nailo+ wa ku Iguputo.’+ 26  Kodi sunamve?+ Kuyambira nthawi zakale izi n’zimene ndidzachite.+Ndinakonza zimenezi kuyambira masiku amakedzana.+ Tsopano ndizichita.+Iweyo udzagwira ntchito yosandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, kukhala yopanda anthu ngati milu ya mabwinja.+ 27  Anthu okhala m’mizindayo adzafooka manja.+Adzachita mantha kwambiri ndiponso adzachita manyazi.+ Adzakhala ngati zomera zakutchire, ndi udzu wanthete wobiriwira,+Ngati udzu womera padenga+ ndiponso wa m’mizere ya m’munda, ukawauka ndi mphepo yotentha yakum’mawa.+ 28  Ukakhala phee, ukamatuluka,+ ndiponso ukamalowa, ine ndimadziwa bwino,+Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+ 29  Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika m’makutu mwanga.+Ndithu ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga, ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako.+Kenako ndidzakukoka n’kukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”+ 30  “‘Ichi chidzakhala chizindikiro chanu: Chaka chino mudya mbewu zomera zokha zimene zinagwera pansi.+ Chaka chamawa mudzadya mbewu zongomera zokha, koma chaka chamkuja, anthu inu mudzabzale mbewu n’kukolola, ndipo mudzalime minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.+ 31  Anthu a m’nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+ 32  Chifukwa anthu otsala adzachoka ku Yerusalemu,+ ndipo opulumuka adzachoka kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+ 33  “‘Chotero Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+ “Sadzalowa mumzinda uno,+ kapena kuponyamo muvi, kapena kufikamo ndi chishango, kapenanso kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo pafupi ndi mpanda wa mzindawu atauzungulira.”’+ 34  “‘Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera, ndipo sadzalowa mumzinda uno,’ ndiwo mawu a Yehova.+ 35  ‘Ndithu ndidzateteza+ mzinda uno kuti ndiupulumutse chifukwa cha ine mwini+ ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’”+ 36  Ndiyeno mngelo+ wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.+ Anthu podzuka m’mawa, anangoona kuti onse aja ndi mitembo yokhayokha.+ 37  Choncho Senakeribu+ mfumu ya Asuri anachokako n’kubwerera+ kukakhala ku Nineve.+ 38  Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi