Yesaya 4:1-6

4  M’tsiku limenelo, akazi 7 adzagwira mwamuna mmodzi+ n’kumuuza kuti: “Ife tizidya chakudya chathu ndipo tizivala zovala zathu. Inuyo mungotilola kuti tizitchedwa ndi dzina lanu kuti tichotse chitonzo chathu.”+  M’tsiku limenelo, chinthu chimene Yehova adzachiphukitse+ chidzakhala chokongoletsera ndi chaulemerero.+ Zipatso za m’dzikolo zidzakhala zonyaditsa+ ndi zokongola kwa Aisiraeli amene adzapulumuke.+  Amene adzatsale mu Ziyoni ndiponso amene adzatsale mu Yerusalemu adzakhala oyera kwa iye.+ Amenewa adzakhala anthu onse amene analembedwa mayina kuti akhale ndi moyo mu Yerusalemu.+  Yehova, pogwiritsa ntchito mzimu wa chiweruzo ndi mzimu wa moto,+ adzatsuka nyansi za ana aakazi a Ziyoni,+ ndiponso adzatsuka+ mkati mwa Yerusalemu n’kuchotsamo magazi amene Yerusalemuyo anakhetsa.+  Akadzatero, malo onse a paphiri la Ziyoni+ ndiponso malo onse a mu Yerusalemu ochitirapo misonkhano, Yehova adzawapangira mtambo ndi utsi kuti ziziwathandiza masana. Adzawapangiranso kuwala kwa moto walawilawi+ kuti kuziwathandiza usiku,+ ndipo pamwamba pa malo onse aulemererowo padzakhala chotchinga.+  Padzakhala msasa kuti uzipereka mthunzi woteteza ku dzuwa masana,+ ndiponso kuti ukhale pothawirapo ndi pobisalirapo mphepo yamkuntho ndi mvula.+

Mawu a M'munsi